Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 5

Kuyamba Kwa Umoyo Wovuta

Kuyamba Kwa Umoyo Wovuta

PAMENE anali kunja kwa munda wa Edeni, Adamu ndi Hava anakhala ndi mavuto ambili. Kuti apeze cakudya anayenela kugwila nchito zolimba. M’malo ao okhala abwino, mmene munali mitengo yokongola yobala zipatso, munayamba kumela minga yambili ndi zitsamba zolasa. Zimenezi zinacitika pamene Adamu ndi Hava anapandukila Mulungu ndi kuleka kukhala mnzao.

Koma coipa kwambili n’cakuti Adamu ndi Hava anayamba kufa. Kumbukila kuti Mulungu anawacenjeza kuti adzafa akadya cipatso ca mtengo uja. Conco tsiku limene io anadya, anayamba kufa. Kusamvela kwao Mulungu kunali kupanda nzelu!

Ana onse a Adamu ndi Hava anabadwa pambuyo pakuti Mulungu wathamangitsa makolo ao kucoka m’munda wa Edeni. Zimenezi zitanthauza kuti ana naonso adzayamba kukalamba ndi kufa.

Sembe Adamu ndi Hava anamvela Mulungu, sembe umoyo wao ndi wa ana ao unakhala wacimwemwe. Sembe onse anakhala kwamuyaya ndi mwacimwemwe padziko lapansi. Palibe amene akanakalamba, kudwala ndi kufa.

Mulungu afuna kuti anthu azikhala ndi moyo kwamuyaya mwacimwemwe, ndipo analonjeza kuti tsiku lina zimenezi zidzacitika. Dziko lonse lapansi lidzakhala lokongola kwambili, ndiponso anthu onse adzakhala ndi thanzi labwino. Anthu onse padziko lapansi adzakhala paubwenzi wina ndi mnzake, ndiponso adzakhala paubwenzi ndi Mulungu.

Koma Hava sanalinso mnzake wa Mulungu. Conco cinali covuta kwambili pamene anayamba kubala ana ake. Anali kumva kuŵaŵa kwambili. Kusamvela Yehova kunamubweletsela mavuto ambili, si conco?

Adamu ndi Hava anakhala ndi ana amuna ndi akazi ambili. Pamene mwana wao woyamba anabadwa, anam’patsa dzina lakuti Kaini. Mwana wao waciŵili anam’patsa dzina lakuti Abele. Nanga n’ciani cinacitika kwa io? Kodi udziŵa?

Genesis 3:16-23; 4:1, 2; Chivumbulutso 21:3, 4.