Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 3

Mwamuna Ndi Mkazi Oyamba

Mwamuna Ndi Mkazi Oyamba

N’CIANI cimene waonapo pa cithunzi-thunzi apa cimene palibe pa cithunzi-thunzi cili kumbuyo uku? Zoona, waonapo anthu. Amenewa ni mwamuna ndi mkazi woyamba. Kodi ndani amene anawapanga? Ni Mulungu. Kodi ulidziŵa dzina la Mulungu? Ni Yehova. Mwamuna uyu anapatsidwa dzina lakuti Adamu, ndipo mkazi lakuti Hava.

Tiye tione mmene Yehova Mulungu anapangila Adamu. Iye anatenga dothi lapansi ndi kupanga thupi langwilo la mwamuna. Ndiyeno Mulungu anafuzilila mpweya m’mphuno mwa mwamunayo, ndipo Adamu anakhala wamoyo.

Tsopano Mulungu anapatsa Adamu nchito yakuti acite. Anauza Adamu kuti apatse maina vinyama vonse va mitundu yosiyana-siyana. Adamu ayenela kuti anakhala ndi vinyama vimenevi kwa nthawi yaitali, conco anadziŵa kusankha maina abwino kwambili akuti avipatse. Pamene Adamu anali kupatsa maina vinyama, anayamba kudabwa cinthu cina. Kodi udziŵa kuti anadabwa ciani?

Anaona kuti vinyama vonse vinali ndi mwamuna wake ndi mkazi wake. Panali njovu ikazi ndi njovu imuna. Panalinso mkango ukazi ndi mkango umuna. Koma Adamu analibe mkazi. Pamenepo, Yehova anagoneka Adamu tulo tofa nato, ndiyeno anacotsa mbambo imodzi kumbali imodzi ya Adamu. Yehova anatenga mbambo imeneyi, ndi kupangila Adamu mkazi.

Tsopano Adamu anakondwela kwambili! Ganiza cabe mmene Hava naye anakondwelela pamene anaikidwa kukhala m’munda wabwino kwambili umenewu! Tsopano cinali cotheka kuti nao abale ana ndi kukhala ndi moyo wacimwemwe.

Yehova anafuna kuti Adamu ndi Hava akhale ndi moyo kwamuyaya. Anafuna kuti io apange dziko lonse lapansi kukhala lokongola monga munda wa Edeni. Ee! Adamu ndi Hava anakondwela kwambili pamene anaganizila zimenezi! Kodi iwe ukanakonda kuthandizako kupanga dziko lapansi kukhala munda wokongola? Koma cimwemwe ca Adamu ndi Hava sicinakhalitse. Tiye tione zimene zinacititsa.

Masalimo 83:18; Genesis 1:26-31; 2:7-25.