Gao 6
Kucokela pa Kubadwa kwa Yesu Kukafika pa Imfa Yake
Mngelo Gabrieli anatumidwa kwa Mariya, mkazi wacitsikana wabwino. Mngeloyo anamuuza kuti adzakhala ndi mwana amene adzalamulila monga mfumu kwamuyaya. Mwana ameneyu, dzina lake Yesu, anabadwila mu khola, kumene abusa anapita kukamuona. Pambuyo pake, nyenyezi inatsogolela amuna amene anacokela Kum’mawa kubwela kumene kunali mwana. Tidzaphunzila amene anawacititsa kuti aone nyenyezi imeneyi, ndiponso mmene Yesu anapulumutsidwila kwa anthu amene anali kufuna kumupha.
Ndiyeno tidzaphunzilanso za Yesu pamene anali kukamba ndi aphunzitsi mu kacisi nthawi imene anali ndi zaka 12. Patapita zaka 18, Yesu anabatizika, ndipo anayamba nchito yolalikila ndi kuphunzitsa za Ufumu wa Mulungu, imene Mulungu anamutuma kuti adzacite padziko lapansi. Yesu anasankha amuna 12 kukhala atumwi ake kuti amuthandize panchito imeneyi.
Yesu nayenso anacita zozizwitsa zambili. Anadyetsa anthu masauzande ndi tunsomba toŵelengeka ndi mikate yocepa. Anacilitsa odwala ndi kuukitsa akufa. Potsilizila pake, tidzaphunzila zinthu zambili zimene zinacitikila Yesu patsiku lake lotsilizila, ndi mmene anafela. Yesu analalikila kwa zaka zitatu ndi hafu, conco GAO 6 likamba za zinthu zimene zinacitika pa zaka zoposa 34.