Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 84

Mngelo Acezela Mariya

Mngelo Acezela Mariya

MKAZI wokongola uyu ni Mariya. Iye ni mkazi waciisiraeli, ndipo akhala ku Nazareti. Mulungu adziŵa kuti iye ni munthu wabwino kwambili. Ndiye cifukwa cake atuma mngelo wake Gabrieli kuti akakambe naye. Kodi udziŵa zimene Gabrieli afuna kuuza Mariya? Tiye tione.

Gabrieli auza Mariya kuti: ‘Mtendele ukhale ndi iwe munthu wodalitsika kwambili. Yehova ali nawe.’ Mariya akalibe kumuonapo munthu uyu, ndipo adela nkhawa cifukwa sadziŵa zimene mngelo watanthauza. Koma panthawi imeneyo Gabrieli amuthandiza kucotsa mantha.

Iye akamba kuti: ‘Usaope Mariya, pakuti Mulungu wakukomela mtima kwambili. Ndiye cifukwa cake adzakucitila cinthu cabwino kwambili. Posacedwa udzakhala ndi mwana. Ndipo udzamupatsa dzina lakuti Yesu.’

Gabrieli apitiliza kufotokoza kuti: ‘Mwana ameneyu adzakhala wamphamvu ndipo adzachedwa Mwana wa Mulungu Wam’mwamba-mwamba. Yehova adzamuika kukhala mfumu monga mmene Davide analili. Koma Yesu adzakhala mfumu kwamuyaya, ndipo ufumu wake sudzasila!’

Mariya afunsa kuti: ‘Koma ine sindine wokwatiwa ndipo sin’nakhalepo ndi mwamuna, nanga ningakhale bwanji ndi mwana?’

Gabrieli ayankha kuti: ‘Mphamvu ya Mulungu idzafika pa iwe, conco mwana amene udzabala adzachedwa Mwana wa Mulungu.’ Ndiyeno auza Mariya kuti: ‘Kumbukila wacibanja wako Elizabeti, anthu anali kukamba kuti sangakhale ndi ana cifukwa ni wokalamba. Koma posacedwa adzakhala ndi mwana mwamuna. Conco waona kuti kulibe cinthu cimene Mulungu angalephele kucita.’

Pamenepo Mariya auza mngelo kuti: ‘Ine ndine kapolo wa Yehova! Zimene mwakamba zicitike kwa ine ndithu.’ Pamenepo mngelo acoka.

Mariya mwamsanga ayenda kukaona Elizabeti. Pamene Elizabeti amvela mau a Mariya, mwana amene ali m’mimba mwake alumpha ndi cikondwelelo. Elizabeti adzazidwa ndi mzimu wa Mulungu, ndipo auza Mariya kuti: ‘Ndiwe wodalitsika mwa akazi onse.’ Mariya akhala ndi Elizabeti pafupi-fupi miyezi itatu, ndiyeno abwelela kwao ku Nazareti.

Mariya ali pafupi kukwatiwa ndi mwamuna, dzina lake Yosefe. Koma pamene Yosefe amvela kuti Mariya adzakhala ndi mwana, aganiza kuti asamukwatile. Koma mngelo wa Mulungu amuuza kuti: ‘Usaope kutenga Mariya kuti akhale mkazi wako. Pakuti Mulungu ndiye amupatsa mwana mwamuna.’ Conco Mariya ndi Yosefe akwatilana, ndipo ayembekezela kuti Yesu abadwe.

Luka 1:26-56; Mateyu 1:18-25.