Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 100

Yesu Ali M’munda

Yesu Ali M’munda

PAMENE acoka m’cipinda capamwamba, Yesu ndi atumwi ake ayenda ku munda wa Getsemane. Iwo amabwela kumalo amenewa nthawi zambili. Yesu tsopano auza ophunzila ake kuti akhale maso ndipo azipemphela. Koma iye apita patsogolo pang’ono, agwada ndipo aŵelamila pansi ndi kuyamba kupemphela.

Patapita kanthawi, Yesu abwelela kumene kuli atumwi ake. Kodi uganiza kuti io acita ciani? Ali gone! Katatu konse Yesu awauza kuti afunika kukhala maso, koma nthawi iliyonse imene abwelela awapeza ali gone. Nthawi yotsilizila imene Yesu abwelela awauza kuti: ‘Mungagone bwanji panthawi ngati ino? Nthawi yakuti ndipelekedwe kwa adani anga yafika.’

Panthawi imeneyo, pamveka congo ca gulu la anthu. Ona! Amuna amene abwela ao, anyamula malupanga ndi mitengo! Anyamulanso miuni kuti iziunikila. Pamene anthu amenewa afika pafupi, mmodzi wa io acoka pa gululo ndi kubwela kwa Yesu. Iye apsompsona Yesu monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Mwamuna ameneyu ni Yudasi Isikariyoti! Nanga n’cifukwa ciani apsompsona Yesu?

Yesu amufunsa kuti: ‘Yudasi, kodi unipeleka mwa kunipsompsona?’ Inde, kupsompsonaku ni cizindikilo. Zimenezi zithandiza amuna amene ali ndi Yudasi kudziŵa kuti uyu ndiye Yesu, munthu amene io afuna. Conco adani a Yesu afika pafupi kuti amugwile. Koma Petulo salola anthu awa kuti atenge Yesu popanda kucitapo kanthu. Conco asolola lupanga limene ali nalo ndi kutema munthu ali pafupi naye. M’malo motema m’mutu, lupanga linadulilatu khutu la munthuyu. Koma Yesu agwila khutu la munthuyu ndi kulibwezelapo.

Yesu auza Petulo kuti: ‘Bwezela lupanga lako mu cimake. Uganiza siningapemphe Atate anga kuti anitumizile masauzande a angelo kuti anipulumutse?’ Zoona angacite zimenezi! Koma Yesu sapempha Mulungu kutumiza angelo alionse, cifukwa adziŵa kuti nthawi yafika yakuti adani ake amugwile. Conco awalola kuti amutenge ndi kupita naye. Tiye tione tsopano zimene zicitikila Yesu.

Mateyu 26:36-56; Luka 22:39-53; Yohane 18:1-12.