Nkhani 90
Yesu Ali Pacitsime Ndi Mkazi
YESU apumula pacitsime ca ku Samariya. Ophunzila ake aloŵa mu mzinda kukagula cakudya. Mkazi amene Yesu akamba naye wabwela kudzatapa madzi pacitsime. Iye auza mkaziyu kuti: ‘Munipatseko madzi akumwa.’
Zimenezi zimudabwitsa kwambili mkaziyu. Kodi udziŵa cifukwa cake? N’cifukwa cakuti Yesu ni Myuda, ndipo mkaziyu ni Msamariya. Ndipo Ayuda ambili sakonda Asamariya. Ngakhale kukamba nao sakamba nao. Koma Yesu amakonda anthu a mitundu yonse. Conco iye akuti: ‘Mukanadziŵa amene akupemphani madzi akumwa, mukanam’pempha madzi amoyo ndipo akanakupatsani.’
Mkaziyu akuti: ‘Citsime n’citali, ndipo inu mulibe ngakhale cotapila madzi. Nanga mudzatenga kuti madzi opatsa moyo?’
Yesu afotokoza kuti: ‘Mukamwa madzi a mu citsime ici mudzamvanso ludzu. Koma madzi amene n’dzakupatsani angacititse munthu kukhala ndi moyo wamuyaya.’
Mkaziyu akuti: ‘Nipatseni madzi amenewo kuti nisakamvenso ludzu, komanso kuti n’sakabwelenso kuno kudzatapa madzi.’
Mkazi ameneyu aganiza kuti Yesu akamba za madzi eni-eni. Koma akamba za coonadi ca Mulungu ndi ufumu wake. Coonadi cimeneci cili monga madzi opatsa moyo, ndipo cingapangitse munthu kukhala ndi moyo wamuyaya.
Tsopano Yesu auza mkaziyu kuti: ‘Pitani, kaitaneni mwamuna wanu ndipo mubwele naye kuno.’
Iye ayankha kuti: ‘Ndilibe mwamuna.’
Yesu akuti: ‘Mwakamba zoona. Koma munakwatiwapo ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene mukhala naye si mwamuna wanu.’
Mkaziyu adabwa kwambili cifukwa zonse zimene Yesu akamba n’zoona. Kodi Yesu anadziŵa bwanji zimenezi? Cifukwa cakuti Yesu ndiye Wolonjezedwa amene anatumidwa ndi Mulungu, ndipo Mulungu ndiye amuuza zinthu zimenezi. Panthawi imeneyi ophunzila a Yesu abwelako, ndipo adabwa kwambili kuona kuti iye akamba ndi mkazi wacisamariya.
Kodi cocitika cimeneci citiphunzitsa ciani? Citionetsa kuti Yesu ni wokoma mtima kwa anthu a mitundu yonse. Ndipo nafenso tifunikila kucita zimenezi. Sitiyenela kuganiza kuti anthu ena ndi oipa, cabe cifukwa cakuti ndi a mtundu wina. Yesu afuna kuti anthu onse adziŵe coonadi cimene cimatsogolela ku moyo wamuyaya. Ndipo nafenso tiyenela kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza anthu kuphunzila coonadi.
Yohane 4:5-43; 17:3.