Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 101

Yesu Aphedwa

Yesu Aphedwa

ONA cinthu comvetsa cisoni kwambili cimene cicitika! Yesu aphedwa. Am’pacika pa mtengo, mwa kumukhokhomela misomali kumanja ndi kumiyendo. Kodi acitila ciani zimenezi kwa Yesu?

N’cifukwa cakuti anthu ena samukonda Yesu. Kodi anthu amenewa uwadziŵa? Mmodzi wa io ni mngelo woipa Satana Mdyelekezi. Ndiye anacititsa Adamu ndi Hava kuti apandukile Yehova. Ndipo ndiye anacititsanso kuti adani a Yesu acite cinthu coipa cimeneci.

Asanapacike Yesu pamtengo, adani ake amenewa amucitila zinthu zankhanza kwambili. Kodi ukumbukila mmene anabwelela kumunda wa Getsemane ndi kumugwila? Kodi adani amenewo ndani? Ni atsogoleli acipembedzo. Cabwino, tiye tione cimene citsatilapo.

Pamene Yesu atengedwa ndi atsogoleli acipembedzo, atumwi ake amuthaŵa. Amusiya yekha ndi adani ake cifukwa ca mantha. Koma Mtumwi Petulo ndi Yohane sathaŵila kutali. Iwo atsatila pambuyo kuti aone zimene zidzacitika kwa Yesu.

Ansembe apeleka Yesu kwa munthu wacikulile dzina lake Anasi, amene kale anali mkulu wa ansembe. Gulu la anthu silinakalitse kumeneku. Kucoka kumeneku apeleka Yesu ku nyumba ya Kayafa, amene tsopano ndiye mkulu wa ansembe. Atsogololeli acipembedzo ambili asokhana pa nyumba yake.

Pamene ali ku nyumba ya Kayafa, aika Yesu pa nsaka kuti amuweluze mlandu. Anthu aitanidwa kuti anamizile Yesu. Atsogoleli acipembedzo onse akamba kuti: ‘Yesu ayenela kuphedwa.’ Ndiyeno amulavulila mate kumaso ndi kumumenya makofi.

Pamene zinthu zonsezi zicitika, Petulo ali panja. Usiku umenewu kwazizila kwambili, conco anthu ayatsa moto. Pamene aotha moto, mkazi wanchito ayang’ana Petulo ndipo akuti: ‘Mwamuna uyu analinso ndi Yesu.’

Petulo ayankha kuti: ‘Iyai, sin’nali naye!’

Katatu konse anthu auza Petulo kuti anali ndi Yesu. Koma nthawi iliyonse imene afunsidwa akana kuti si zoona. Nthawi yacitatu imene Petulo akamba zimenezi, Yesu aceuka ndi kumuyang’ana. Petulo amvela kuipa kwambili cifukwa cokamba bodza, ndipo acokapo ndi kuyamba kulila.

Pamene dzuŵa liyamba kutuluka pa Cisanu m’mawa, ansembe atenga Yesu ndi kupita naye ku Khoti Yaikulu ya Ayuda. Kumeneku akambitsilana zimene adzamucita. Iwo apita naye kwa Pontiyo Pilato, wolamulila wa cigao ca Yudeya.

Ansembe auza Pilato kuti: ‘Uyu ni munthu woipa. Ayenela kuphedwa.’ Pambuyo pofunsa Yesu mafunso, Pilato akuti: ‘Palibe cimene walakwa munthu uyu.’ Ndiyeno Pilato atumiza Yesu kwa Herode Antipa. Herode ni wolamulila wa ku Galileya, koma amakhala mu Yerusalemu. Herode naye sapeza ciliconse cimene Yesu walakwa, conco amutumizanso kwa Pilato.

Pilato afuna kumasula Yesu kuti apite. Koma adani a Yesu afuna kuti mkaidi wina amasulidwe osati Yesu. Mkaidi ameneyu ni Baraba. Tsopano ni nthawi ya kumasana pamene Pilato atulutsa Yesu panja. Iye auza anthu kuti: ‘Onani mfumu yanu!’ Koma ansembe aakulu afuula kuti: ‘Aphedwe! Aphedwe!’ Conco Pilato amasula Baraba, ndipo atenga Yesu ndi kupita naye kuti akaphedwe.

Pa Cisanu kumasana Yesu apacikidwa pamtengo. Kumbali iliyonse ya Yesu kuli cigaŵenga. Nazonso azipacika pamtengo kuti zife, koma sungazione pacithunzi-thunzi apa. Kanthawi pang’ono Yesu asanafe, cimodzi ca zigaŵengazo cipempha Yesu kuti: ‘Mukanikumbukile mukaloŵa mu ufumu wanu.’ Ndipo Yesu ayankha kuti: ‘Ni kulonjeza kuti udzakhala ndi ine mu Paladaiso.’

Kodi limenelo si lonjezo labwino? Nanga udziŵa paladaiso imene Yesu akamba? Kodi Paladaiso imene Mulungu anapanga paciyambi inali kuti? Inali padziko lapansi. Ndipo Yesu akayamba kulamulila monga mfumu kumwamba, adzaukitsa munthu ameneyu kuti adzasangalale ndi moyo mu Paladaiso padziko lapansi. Kodi zimenezi si zokondweletsa?

Mateyu 26:57-75; 27:1-50; Luka 22:54-71; 23:1-49; Yohane 18:12-40; 19:1-30.