Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 91

Yesu Aphunzitsa Pa Phili

Yesu Aphunzitsa Pa Phili

WAMUONA Yesu ali khale pacithunzi-thunzi apa? Iye aphunzitsa anthu onse awa pa phili la Galileya. Ao amene akhala pafupi naye ni ophunzila ake. Iye wasankha amuna 12 kukhala atumwi. Atumwi ni ophunzila apadela a Yesu. Kodi uwadziŵa maina ao?

Pali Simoni Petulo ndi m’bale wake Andreya. Ndiyeno pali Yakobo ndi Yohane, amenenso ali pacibale. Ndipo pali wina wochedwanso Yakobo ndi wina wochedwanso Simoni. Atumwi aŵili amachedwa Yudasi. Mmodzi ni Yudasi Isikariyoti ndipo Yudasi wina amachedwanso Tadeyo. Ndiyeno pali Filipo ndi Natanayeli (amene amachedwanso Batolomeyo). Ndiyeno pali Mateyu ndi Tomasi.

Pamene Yesu anabwela kucokela ku Samariya, anayamba nchito yolalikila. Muulaliki wake woyamba umenewu, iye anati: ‘Ufumu wakumwamba wayandikila.’ Kodi ufumu umenewo waudziŵa? Ni boma leni-leni la Mulungu, ndipo Yesu ndiye mfumu ya ufumu umenewo. Iye adzalamulila kucokela kumwamba, ndipo adzabweletsa mtendele padziko lapansi. Ufumu wa Mulungu udzasandutsa dziko lonse lapansi kukhala paladaiso yokongola.

Yesu pacithunzi-thunzi apa aphunzitsa anthu za ufumu. Awafotokozela kuti: ‘Inu muzipemphela conco: Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe, ufumu wanu ubwele, cifunilo canu cicitike monga kumwamba cimodzi-modzinso pansi pano.’ Pemphelo limeneli ambili amalicha, ‘Pemphelo la Ambuye.’ Ena amati ni pemphelo la ‘Atate wakumwamba.’ Kodi ungawakambe mau onse a pemphelo limeneli?

Yesu aphunzitsanso anthu mmene ayenela kucitila zinthu ndi anzao. Iye akuti: ‘Zinthu zonse zimene mufuna kuti anthu akucitileni, acitileni zimenezo.’ Kodi umakondwela ngati ena akucitila zinthu mokoma mtima? Conco, Yesu akuti, tiyenela kucitila anthu ena mokoma mtima. Kodi suona kuti zidzakhala zokondweletsa pamene anthu onse adzakhala akucita zimenezi mu paladaiso padziko lapansi?

Mateyu caputa 5 mpaka 7; Mt 10:1-4.