Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Gao 4

Kucokela pa Mfumu Yoyamba ya Isiraeli, Kukafika pa Nthawi Yotengedwa Ukapolo ku Babulo

Kucokela pa Mfumu Yoyamba ya Isiraeli, Kukafika pa Nthawi Yotengedwa Ukapolo ku Babulo

Sauli anakhala mfumu yoyamba ya Isiraeli. Koma Yehova anam’kana, ndipo anasankha Davide kukhala mfumu m’malo mwa iye. Tidzaphunzila zinthu zambili ponena za Davide. Akali wacinyamata, anapha Goliyati amene anali cimphona. Pambuyo pake anathaŵa Mfumu Sauli amene anali wansanje. Ndiyeno mkazi wokongola Abigayeli anamuletsa kucita cinthu coipa.

Tidzaphunzilanso zinthu zambili ponena za Solomo mwana wa Davide, amene anakhala mfumu ya Isiraeli pamene atate ake anamwalila. Mafumu atatu oyambilila a Isiraeli, aliyense analamulila kwa zaka 40. Pamene Solomo anamwalila, ufumu wa Isiraeli unagaŵikana, kukhala ufumu wakumpoto ndi ufumu wakum’mwela.

Ufumu wakumpoto wa mafuko 10 unakhalako kwa zaka 257 usanaonongedwe ndi Asuri. Ndiyeno pambuyo pa zaka 133, ufumu wakum’mwela wa mafuko aŵili naonso unaonongedwa. Panthawi imeneyi, Aisiraeli anatengeledwa ku Babulo kukakhala akapolo. Conco Gao 4 ni mbali ya zinthu zimene zinacitika mu nyengo ya zaka 510. Panthawi imeneyi, zinthu zocititsa cidwi zambili zinacitika ife tikalibe kukhalako.