Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 58

Davide Ndi Goliyati

Davide Ndi Goliyati

AFILISTI abwelanso kuti amenyane ndi Aisiraeli. Akulu ake a Davide atatu tsopano ali m’gulu la nkhondo la Sauli. Conco, tsiku lina Jese anauza Davide kuti: ‘Tenga tiligu ndi mitanda ya mkate ukapatse abale ako. Ukaonenso kuti abale ako ali bwanji.’

Pamene Davide afika pamsasa wa asilikali, athamangila kumalo omenyela nkhondo kuti akaone abale ake. Cimphona ca Afilisti, dzina lake Goliyati cibwela ndi kuyamba kunyoza Aisiraeli. Cinali kucita zimenezi kum’mawa ndi kumadzulo kwa masiku 40. Cifuula kuti: ‘Sankhani munthu amene adzamenyane ndi ine. Ngati angamenyane ndi ine ndi kundipha, ndiye kuti tidzakhala akapolo anu. Koma ngati ningalimbane naye mpaka kumupha, inu mudzakhala akapolo athu. Conco ndikuuzani kuti, sankhani munthu amene adzamenyana ndi ine.’

Ndiyeno Davide afunsa asilikali ena kuti: ‘Kodi munthu amene angaphe Mfilisti ameneyu ndi kucotsa citonzo pa Isiraeli adzamucitila ciani?’

Msilikali wina akuti: ‘Sauli adzamupatsa cuma cambili ndi kumupatsanso mwana wake kuti akhale mkazi wake.’

Koma Aisiraeli onse aopa Goliyati cifukwa ni cimphona. Ni wamthali pafupi-fupi mamita atatu, ndipo acita kukhala ndi msilikali wina womunyamulila cishango.

Asilikali ena apita kukauza Mfumu Sauli kuti Davide afuna kumenyana ndi Goliyati. Koma Sauli auza Davide kuti: ‘Sungamenyane ndi Mfilisti ameneyu, cifukwa ndiwe mwana. Mfilisti ameneyu wakhala akumenya nkhondo moyo wake wonse.’ Davide ayankha kuti: Ine ndinapha cimbalangondo ndi mkango zimene zinagwila nkhosa za atate anga. Ndipo Mfilisti ameneyu ndidzamupha mmene ndinaphela zilombo zimenezi. Yehova adzandithandiza.’ Conco Sauli akuti: ‘Pita, ndipo Yehova akhale nawe.’

Davide apita ku mtsinje ndi kutenga miyala isanu yosalala kwambili, ndipo aiika mu kacola kake. Atenganso legeni kapena kuti gulaye lake ndi kupita kukakumana ndi cimphona cija. Pamene Goliyati aona Davide, sakhulupilila zimene aona. Iye aganiza kuti cidzakhala cosavuta kupha Davide.

Goliyati anati: ‘Uyese kubwela kuno, nidzapeleka thupi lako kwa mbalame ndi kwa zilombo kuti zidye.’ Koma Davide anati: ‘Iwe ubwela kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine nibwela kwa iwe mu dzina la Yehova. Lelo Yehova akupeleka m’manja mwanga, ndipo n’dzakupha.’

Pamenepo Davide athamangila kwa Goliyati. Atenga mwala mu kacola kake ndi kuuika pa legeni yake, ndi kuuponya ndi mphamvu zake zonse. Mwala uja ulunjika pa mutu wa Goliyati, ndiyeno uboola ndi kulowelatu mkati. Pamenepo Goliyati pansi khu, n’kufelatu! Pamene Afilisti aona kuti ngwazi yao yagwa, onse alapuka kuthaŵa. Aisiraeli athamangitsa Afilisti ndi kuwagonjetsa.

1 Samueli 17:1-54.