Nkhani 69
Kamtsikana Kathandiza Munthu Wamphamvu Kwambili
KODI udziŵa zimene kamtsikana aka kakamba? Kauza dona uyu za Elisa mneneli wa Yehova. Kamuuzanso zinthu zabwino zimene Yehova wathandiza Elisa kucita. Dona uyu sadziŵa Yehova cifukwa si Mwisiraeli. Tiye tione tsopano cifukwa cake kamtsikana aka kali mu nyumba ya dona ameneyu.
Dona uyu ni Msiriya, ndipo mwamuna wake ni Namani, mkulu wa gulu la asilikali a dziko la Siriya. Asiriya anagwila kamtsikana kaciisiraeli kameneka, ndi kukabweletsa kwa mkazi wa Namani kuti kazimuseŵenzela.
Namani ali ndi matenda oipa a khate. Matenda amenewa angacititse mnofu wa munthu kunyotsoka-nyotsoka. Conco kamtsikanaka kauza mkazi wa Namani kuti: ‘Mbuyanga akayenda kwa mneneli wa Yehova amene ali ku Isiraeli, angamucilitse khate lake.’ Pambuyo pake, Mkaziyu auza mwamuna wake nkhani imeneyi.
Namani afuna kwambili kuti acile, conco ayenda ku Isiraeli. Pamene afika kumeneko, ayenda ku nyumba ya Elisa. Ndipo Elisa atuma wanchito wake kuuza Namani kuti ayende akasambe mu mtsinje wa Yorodano maulendo 7. Zimenezi zikalipitsa kwambili Namani, ndipo akamba kuti: ‘Mitsinje ya kwathu iposa mitsinje yonse ku Isiraeli!’ Pambuyo pokamba zimenezi, Namani acoka.
Koma mmodzi wa atumiki ake amuuza kuti: ‘Mbuyanga, kodi mneneliyo akanakuuzani kuti mucite cinthu cacikulu, simukanacita? Nanga bwanji simungangopita kukasamba monga mmene wakuuzilani?’ Namani amvela zimene mtumiki wake amuuza, ndipo apita ndi kukambila maulendo 7 mu mtsinje wa Yorodano. Pamene acita zimenezi, mnofu wake ukhala bwino-bwino ndipo acila!
Namani akondwela kwambili. Ndipo abwelela kwa Elisa ndi kumuuza kuti: ‘Tsopano ndadziŵa ndithu kuti, padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu woona kusiyapo ku Isiraeli cabe. Ndiye landilani mphatso kucokela kwa ine mtumiki wanu.’ Koma Elisa ayankha kuti: ‘Iyai, sinidzailandila.’ Elisa adziŵa kuti kungakhale kulakwa kuti iye atenge mphatso ija, cifukwa Yehova ni amene wacilitsa Namani. Koma Gehazi wanchito wa Elisa aifuna mphatso ija.
Udziŵa zimene Gehazi acita? Pamene Namani acokapo, Gehazi amuthamangila kuti amupeze. Ndiyeno Gehazi akamba kuti: ‘Elisa wandituma kuti n’kuuzeni kuti afunako mphatso zina kuti apatse anzake amene abwela kudzamucezela.’ Limeneli ni bodza. Koma Namani sanadziŵe kuti ni bodza, conco anapatsa Gehazi zinthu zina.
Pamene Gehazi abwelela ku nyumba, Elisa adziŵa zimene iye wacita. Yehova ndiye wamuuza. Conco iye akamba kuti: ‘Cifukwa wacita cinthu coipaci, khate la Namani lidzabwela pa iwe.’ Ndipo nthawi imeneyo zinacitika!
Kodi tiphunzilapo ciani pa zimenezi? Coyamba, tifunikila kukhala monga kamtsikana kaja, kukamba za Yehova. Kucita zimenezi kungatithandize kwambili. Caciŵili, tisakhale odzikudza ngati mmene Namani analili poyamba, koma tiyenela kumvela atumiki a Mulungu. Ndipo cacitatu, sitiyenela kunama monga mmene Gehazi anacitila. Tingaphunzile zambili mwa kuŵelenga Baibo, si conco?
2 Mafumu 5:1-27.