Nkhani 63
Solomo Mfumu Yanzelu
SOLOMO akhala mfumu pamene akali mnyamata. Amakonda Yehova, ndipo amatsatila malangizo abwino amene atate ake a Davide anamupatsa. Yehova akondwela ndi zimene Solomo amacita, cakuti tsiku lina amuuza m’maloto kuti: ‘Solomo, kodi ufuna n’kupatse ciani?’
Ndipo Solomo ayankha kuti: ‘Yehova Mulungu wanga, ndine mwana ndipo sindidziŵa kulamulila. Conco, nipatseni nzelu zonithandiza kulamulila anthu anu mu njila yoyenela.’
Yehova akondwela kwambili ndi zimene Solomo wapempha. Conco amuuza kuti: ‘Cifukwa wapempha nzelu osati moyo wautali kapena cuma, n’dzakupatsa nzelu zambili kupambana munthu aliyense amene anakhalako. Koma n’dzakupatsanso zimene sunapemphe, cuma ndi ulemelelo.’
Patapita nthawi yocepa, akazi aŵili abwela kwa Solomo ndi vuto lalikulu. Mmodzi wa io akuti: ‘Ine ndi mkazi uyu timakhala mu nyumba imodzi. Ine n’nabala mwana mwamuna, ndipo patapita masiku aŵili naye uyu anabala mwana mwamuna. Ndiyeno tsiku lina, mwana wake anafa. Koma pamene ine n’nali mu tulo, iye watenga mwana wake wakufa n’kumuika pambali panga, ndiyeno n’kutenga mwana wanga. Pamene nauka, nayan’ganitsitsa mwana wakufa ndipo naona kuti si wanga.’
Koma, mkazi winayo akuti: ‘Iyai! Mwana wamoyo ni wanga, wakufa ndiye wake!’ Ndiyeno mkazi woyamba akamba kuti: ‘Iyai! Mwana wakufa ni wako, wamoyo ndiye wanga!’ Izi n’zimene akazi amenewa akangana. Kodi Solomo adzacita ciani?
Iye aitanitsa lupanga. Ndipo pamene abweletsa lupanga, alamula kuti: ‘M’cekeni pakati mwana wamoyo. Hafu m’patse mkazi uyu, ndipo hafu ina m’patse mkazi winayu.’
Pamenepo mai wake weni-weni alila kuti: ‘Iyai! Musamuphe mwanayo conde. M’patseni mkazi winayu!’ Koma mkazi winayo akuti: ‘Mwanayu musapatse ine kapena uyu, mucekeni cabe pakati.’
Potsilizila pake Solomo akuti: ‘Musamuphe mwanayo! M’patseni kwa mkazi woyamba, iye ndiye mai wake weni-weni.’ Solomo wadziŵa zimenezi cifukwa mai wake weni-weni akonda kwambili mwana wake, cakuti avomela kuti apatsidwe kwa mkazi winayo m’malo mwakuti amuphe. Pamene anthu akumva mmene Solomo anaweluzila mlanduwu, akondwela kwambili kuti ali ndi mfumu yanzelu.
Pamene Solomo alamulila, Mulungu adalitsa anthu mwa kucititsa nthaka kubala kwambili tiligu ndi balele, mpesa ndi nkhuyu ndiponso zakudya zina. Anthu avala zovala zabwino ndi kukhala mu nyumba zabwino. Ndipo ali ndi zinthu zabwino zonse zokwanila aliyense.
1 Mafumu 3:3-28; 4:29-34.