Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 67

Yehosafati Adalila Yehova

Yehosafati Adalila Yehova

KODI uwadziŵa amuna awa amene ali pacithunzi-thunzi. Nanga udziŵa zimene acita? Iwo ayenda kunkhondo, ndipo amuna amene ali kutsogolo ni oimba. Koma ungafunse kuti: ‘N’cifukwa ciani oimba alibe malupanga ndi mikondo yomenyela nkhondo?’ Tiye tione.

Yehosafati ni mfumu ya ufumu wa mafuko aŵili a Isiraeli. Iye akhalako panthawi imodzi-modzi ndi Mfumu Ahabu ndi Yezebeli wa ku ufumu wakumpoto wa mafuko 10. Koma Yehosafati ni mfumu yabwino, ndipo ngakhale atate ake a Asa nawonso anali mfumu yabwino. Conco kwa zaka zambili anthu a mu ufumu wa mafuko aŵili wa kum’mwela akhala ndi umoyo wokondwela.

Koma cinacake cicitika cimene cipangitsa anthu kukhala ndi mantha. Amithenga auza Yehosafati kuti: ‘Gulu la asilikali locokela ku dziko la Moabu, Amoni ndi phili la Seiri libwela kudzacita nanu nkhondo.’ Aisiraeli ambili asonkhana ku Yerusalemu kuti apemphe thandizo la Yehova. Iwo ayenda ku kacisi, ndipo pamene ali kumeneko, Yehosafati apemphela kuti: ‘O Yehova Mulungu wathu, sitidziŵa cimene tingacite. Tilibe mphamvu yolimbana ndi gulu la asilikali ili. Tiyang’ana kwa inu kuti mutithandize.’

Yehova amvela pemphelo lao, ndipo auza mmodzi wa atumiki ake kuuza anthu kuti: ‘Nkhondoyi si yanu, koma ndi ya Mulungu. Simudzafunikila kumenya nkhondo iyai. Mufunikila kungoyang’ana ndi kuona mmene Yehova adzakupulumutsilani.’

Conco tsiku lotsatila Yehosafati auza anthu kuti: ‘Dalilani Yehova!’ Ndiyeno aika oimba patsogolo pa asilikali ake, ndipo pamene aguba aimba nyimbo zotamanda Yehova. Kodi udziŵa cimene cicitika pamene afika pafupi ndi kumalo omenyela nkhondo? Yehova acititsa asilikali a adani ao kumenyana okha-okha. Ndipo pamene Aisiraeli afika, apeza kuti asilikali onse a adani ao ni akufa kale!

Yehosafati anaonetsadi nzelu yodalila Yehova, si conco? Nafenso tidzakhala anzelu ngati timadalila Yehova.

1 Mafumu 22:41-53; 2 Mbiri 20:1-30.