Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 76

Yerusalemu Aonongedwa

Yerusalemu Aonongedwa

PAPITA zaka zoposa 10 kucokela panthawi imene Mfumu Nebukadinezara anatenga Aisiraeli onse ophunzila kwambili kupita nao ku Babulo. Koma tsopano ona zimene zicitika pacithunzi-thunzi apa! Yerusalemu atenthedwa. Ndipo Aisiraeli amene sanaphedwe anawagwila kukhala akaidi, ndipo awatengela ku Babulo.

Kumbukila kuti izi n’zimene aneneli a Yehova anacenjeza kuti zidzacitika ngati anthu sadzasintha makhalidwe ao oipa. Koma Aisiraeli sanamvele zimene aneneli anakamba. Iwo anapitiliza kulambila milungu yonama m’malo molambila Yehova. Conco n’koyenela kuti anthu apatsidwe cilango. Tidziŵa zimenezi cifukwa mneneli wa Mulungu Ezekieli amatiuza zinthu zoipa zimene Aisiraeli anali kucita.

Kodi umudziŵa Ezekieli? Iye ni mmodzi wa anyamata amene Mfumu Nebukadinezara anapita nao ku Babulo, zaka zoposa 10 cionongeko cacikulu cimeneci ca Yerusalemu cisanacitike. Panthawi imodzi-modziyo, Danieli ndi anzake atatu aja, Sadirake, Mesake ndi Abedinego, naonso anatengedwa kupita ku Babulo.

Pamene Ezekieli ali ku Babulo, Yehova amuonetsa zinthu zoipa zimene zicitika pa kacisi ku Yerusalemu. Yehova acita zimenezi mozizwitsa. Ezekieli akali ku Babulo, koma Yehova amuonetsa zonse zimene zicitika pa kacisi. Ndipo zimene Ezekieli aona n’zodabwitsa kwambili!

Yehova auza Ezekieli kuti: ‘Ona zinthu zonyansa zimene anthu acita pa kacisi. Ona zipupa zimene anajambulapo njoka ndi nyama zina. Ndipo ona Aisiraeli azilambila!’ Ezekieli aona zinthu zimenezi, ndipo alemba zimene zicitika.

Yehova afunsa Ezekieli kuti: ‘Kodi waona zimene atsogoleli a Aisiraeli acita mwamseli? Ezekieli naye aona yekha zimene io acita. Pali amuna 70, ndipo onse alambila milungu yonama. Atsogoleli amenewo akamba kuti: Yehova sationa, ndipo wacokamo m’dziko muno.’

Ndiyeno Yehova aonetsa Ezekieli akazi amene ali pageti kapena kuti pacipata ca kumpoto kwa kacisi. Iwo akhala pamenepo ndipo alambila mulungu wonama Tamuzi. Ndipo ona amuna pafupi-fupi 25 awo amene ali pakhomo la kacisi wa Yehova! Ezekieli awaona, ndipo io aŵelamila kum’mawa kulambila dzuŵa!

Yehova akuti: ‘Anthu awa sanilemekeza. Amacita vinthu voipa, cakuti amacita kubwela kudzacitila vinthu voipa pa kacisi wanga!’ Conco Yehova alonjeza kuti: ‘Iwo adzamva ululu wanga. Ndipo sinidzawamvelela cifundo pamene adzaonongedwa.’

Papita pafupi-fupi zaka zitatu cabe kucokela pamene Yehova anaonetsa Ezekieli zinthu zimenezi, ndiyeno Aisiraeli apandukila Mfumu Nebukadinezara. Conco iye apita kukacita nao nkhondo. Patapita caka cimodzi ndi hafu, Ababulo aloŵa mu Yerusalemu ndi kutenthelatu mzinda wonse. Anthu ambili aphedwa ndipo ena atengedwa kukakhala akaidi ku Babulo.

N’cifukwa ciani Yehova walola kuti cionongeko cacikulu cimeneci cicitikile Aisiraeli? N’cifukwa cakuti io sanamvele Yehova, ndipo sanatsatile malamulo ake. Zimenezi zionetsa kuti nthawi zonse n’kofunika kwambili kucita zimene Mulungu amatiuza.

Paciyambi, anthu ocepa avomelezedwa kukhala m’dziko la Isiraeli. Ndiyeno Nebukadinezara aika Myuda wochedwa Gedaliya kuti aziyang’anila anthu amenewa. Koma Aisiraeli ena amupha Gedaliya. Conco anthu acita mantha kuti Ababulo adzabwela ndi kuwaononga onse cifukwa ca cinthu coipa cimene cacitika. Akakamiza Yeremiya kuti athaŵile nao pamodzi, ndipo athaŵila ku Iguputo.

Zimenezi zitanthauza kuti m’dziko la Isiraeli mutsala mulibe munthu aliyense. Kwa zaka 70, mu dzikolo simukhala anthu, ndipo mulibiletu kanthu kalikonse. Koma Yehova alonjeza kuti adzawabweza anthu ake mu dziko limenelo pambuyo pa zaka 70. Panthawiyi, kodi n’ciani cicitika kwa anthu a Mulungu ku Babulo kumene atengedwela? Tiye tione.

2 Mafumu 25:1-26; Yeremiya 29:10; Ezekieli 1:1-3; 8:1-18.