Gao 5
Kucokela pa Ukapolo ku Babulo, Kukafika pa Kumangidwanso kwa Mpanda wa Yerusalemu
Pamene Aisiraeli anali mu ukapolo ku Babulo, anakumana ndi ziyeso zosiyana-siyana zoyesa cikhulupililo cao. Sadirake, Mesake ndi Abedinego anaponyedwa mu ng’anjo ya moto, koma Mulungu anawapulumutsa. Ndiyeno pambuyo pakuti Ababulo agonjetsedwa ndi Amedi ndi Aperisiya, Danieli anaponyedwa mu dzenje la mikango, koma Mulungu anamupulumutsa mwa kutseka pakamwa pa mikango.
Potsilizila pake, Koresi Mfumu ya ku Perisiya, inalola Aisiraeli kubwelela kwao. Panapita zaka 70 kucokela pamene io anagwidwa kukhala akapolo ku Babulo. Cimene anayambilila kucita pamene anabwelela ku Yerusalemu cinali kumanga kacisi wa Yehova. Ngakhale zinali conco, adani anawalepheletsa kucita nchito imeneyi. Conco panatenga zaka 22 kucokela pamene anabwelela ku Yerusalemu, kuti atsilize kumanga kacisi.
Ndiponso, tidzaphunzilanso za ulendo wa Ezara wopita ku Yerusalemu kuti akakongoletse kacisi. Izi zinacitika zaka 47 pambuyo pakuti Aisiraeli atsiliza kumanga kacisi. Ndiyeno zaka 13 pambuyo paulendo wa Ezara, Nehemiya anathandizila pa kumanganso mpanda kapena kuti cipupa ca Yerusalemu cimene cinaonongedwa. Gao 5 limeneli limakamba za zocitika zakale mpaka kudzafika m’nthawi yathu ino, ndipo zocitika zimenezi zinatenga zaka 152.