Nkhani 79
Danieli Mu Dzenje La Mikango
A-AA! Zioneka kuti Danieli ali mu vuto likulu kwambili. Koma mikango siimupweteka! Kodi udziŵa cifukwa cake? Kodi ndani waika Danieli mu dzenje la mikango? Tiye tione.
Dariyo tsopano ndiye Mfumu ya Babulo. Iye amukonda kwambili Danieli cifukwa cakuti Danieli ni munthu wabwino mtima ndipo ni wanzelu. Dariyo asankha Danieli kukhala mkulu wa akulu-akulu a mu ufumu wake. Zimenezi zipangitsa amuna ena kucitila Danieli nsanje. Tsopano io acita ciani?
Apita kwa Dariyo ndi kumuuza kuti: ‘Tagwilizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo loletsa munthu aliyense kupemphela kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense kwa masiku 30, kusiyapo kwa inu cabe mfumu. Aliyense amene sadzamvela lamulo limeneli, aponyedwe mu dzenje la mikango.’ Dariyo sadziŵa cifukwa cake amuna amenewa afuna kuti lamulo limeneli lipangidwe. Iye aona kuti ndi lingalilo labwino, conco alilemba. Tsopano lamulo limeneli silingasinthidwe.
Pamene Danieli adziŵa za lamulo limeneli, ayenda kunyumba kwake ndi kukapemphela, monga mmene amacitila masiku onse. Amuna oipa amenewa adziŵa kuti Danieli sadzaleka kupemphela kwa Yehova. Koma akondwela cifukwa adziŵa kuti pulani yao yakuti acotsetse Danieli idzagwila nchito.
Pamene Mfumu Dariyo idziŵa cifukwa cake amuna amenewa afuna lamulo limeneli, amvela kuipa kwambili. Koma sangasinthe lamulo. Conco alamula kuti Danieli aponyedwe mu dzenje la mikango. Ndipo mfumu iuza Danieli kuti: ‘Nikhulupilila kuti Mulungu wako amene umamutumikila adzakupulumutsa.’
Dariyo akalipa kwambili cakuti sagona tulo usiku. M’maŵa mwake, athamangila kudzenje la mikango. Wamuona uyo apo. Ndiye afuula kuti: ‘Danieli mtumiki wa Mulungu wamoyo! Kodi Mulungu wako amene umatumikila wakupulumutsa ku mikango?’
Danieli ayankha kuti: ‘Mulungu watumiza mngelo wake kugwila pakamwa pa mikango, ndipo mikango sinanivulaze.’
Mfumu ikondwela kwambili. Ndipo ilamula anthu ake kuti acotse Danieli mu dzenje la mikango. Koma tsopano ilamula kuti amuna oipa aja amene safuna Danieli, aponyedwe mu dzenje la mikango. Iwo akalibe kufika pansi pa dzenje, mikango iwakhadzula-khadzula ndi kuphwanya mafupa ao.
Ndiyeno, Mfumu Dariyo ilembela anthu onse mu ufumu wake kuti: ‘Ine nilamula kuti aliyense azilemekeza Mulungu wa Danieli. Iye amacita zinthu zodabwitsa. Anapulumutsa Danieli kuti mikango isamudye.’
Danieli 6:1-28.