Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 78

Dzanja Lilemba Pacipupa

Dzanja Lilemba Pacipupa

KODI n’ciani cicitika pacithunzi-thunzi apa? Anthu ali pa phwando lalikulu. Mfumu ya ku Babulo yaitanila anthu olemekezeka okwana masauzande ku phwando limeneli. Anthu amwela m’makapu agolide ndi asiliva, ndi kudyela pa mbale zimene anatenga mu kacisi wa Yehova ku Yerusalemu. Ndiyeno mwadzidzidzi, paoneka dzanja la munthu, ndipo liyamba kulemba pacipupa. Anthu onse acita mantha.

Panthawi imeneyi, Belisazara, mdzukulu wa Nebukadinezara ndiye Mfumu ya Babulo. Conco pamene izi zicitika iye anaitana anthu ake anzelu ndi kuwauza kuti: ‘Aliyense amene angaŵelenge mau awa ndi kuniuza tanthauzo lake, nidzamupatsa mphatso zambili ndipo adzakhala wolamulila wacitatu mu ufumu wanga.’ Koma amuna onse anzelu sakwanitsa kuŵelenga mauwo ndi kumasulila tanthauzo lake.

Pamene amai a mfumu amvela congo, abwela kucipinda codyelamo kumene kunali phwando. Ndipo auza mfumu kuti: ‘Musacite mantha, mu ufumu wanu muli mwamuna amene adziŵa milungu yoyela. Pamene ambuye anu a Nebukadinezara anali mfumu, anaika munthu ameneyu kukhala mkulu wa amuna onse anzelu. Dzina lake ni Danieli. Mubweletseni, ndipo adzakuuzani tanthauzo la zimenezi.’

Conco panthawi imeneyi abweletsa Danieli. Pambuyo pokana kulandila mphatso iliyonse, Danieli awauza cifukwa cake Yehova anacotsela Nebukadinezara ambuye a Belisazara pa ufumu. Danieli akamba kuti: ‘Iye anali wodzikweza kwambili, conco Yehova anamulanga.’

Danieli auza Belisazara kuti: ‘Koma iwe udziŵa zonse zimene zinacitikila Nebukadinezara, ndipo ukali wodzikweza monga mmene iye analili. Wagwilitsila nchito makapu ndi mbale za ku kacisi wa Yehova. Watamanda milungu yamitengo ndi yamiyala, ndipo sunalemekeze Mlengi wathu wamkulu. Ndiye cifukwa cake Mulungu watumiza dzanja kuti lilembe mau awa.

Danieli akamba kuti: ‘Izi ndiye zimene zalembedwa, MENE, MENE, TEKELI, ndi PARASINI.’

‘MENE itanthauza kuti Mulungu waŵelenga masiku a ufumu wanu ndipo wautsiliza. TEKELI itanthauza kuti mwapimidwa pasikelo ndipo mwapezeka kuti mwapeleŵela. PARASINI itanthauza kuti ufumu wanu wapatsidwa kwa Amedi ndi Aperisiya.’

Pamene Danieli akamba zimenezi, Amedi ndi Aperisiya ayamba kale kulanda mzinda wa Babulo. Alanda mzinda ndi kupha Belisazara. Usiku umenewo mau amene alembedwa pacipupa akwanilitsika! Koma kodi n’ciani cidzacitikila Aisiraeli tsopano? Tidzaona, koma coyamba tiye tione zimene zicitika kwa Danieli.

Danieli 5:1-31.