Nkhani 77
Iwo Sanagwadile Fano
KODI unamvelapo za anyamata atatu awa amene ali pacithunzi-thunzi? Anyamata amenewa ni anzake a Danieli amene anakana kudya zakudya zimene sizinali zabwino kwa io. Ababulo anawapatsa maina akuti Sadirake, Mesake, ndi Abedinego. Ona zimene anyamata amenewa acita pacithunzi-thunzi apa. N’cifukwa ciani sagwadila fano lalikulu limeneli monga mmene acitila anthu onse? Tiye tione.
Kodi uyakumbukila malamulo amene Yehova analemba ochedwa kuti Malamulo Khumi? Lamulo loyamba pa malamulo amenewa ni lakuti: ‘Usalambile milungu ina iliyonse kusiyapo ine.’ Anyamata amenewa atsatila lamulo limeneli ngakhale sicinthu copepuka kucita.
Nebukadinezara, mfumu ya ku Babulo, iitana anthu olemekezeka kuti adzalambile fano limene wapanga. Iye wauza anthu onse kuti: ‘Mukamvela kulila kwa lipenga, zitolilo ndi zoimbila zina, mugwade ndi kulambila fano la golide limeneli. Aliyense amene sadzagwadila ndi kulambila fano adzaponyedwa mu ng’anjo yoyaka moto.’
Pamene Nebukadinezara amvela kuti Sadirake, Mesake, ndi Abedinego sanagwadile fano, akalipa kwambili. Ndipo awaitana ndi kuwauzanso kuti agwade. Koma anyamata amenewa akhulupilila Yehova. Iwo auza Nebukadinezara kuti: ‘Mulungu amene timatumikila akhoza kutipulumutsa, koma ngati sadzatipulumutsa sitidzagwadila fano lanu la golide.’
Pamene Nebukadinezara amvela zimenezi akalipa kwambili. Pali ng’anjo ya moto pafupi ndipo alamula kuti: ‘Sonkhezani ng’anjo moŵilikiza nthawi 7 kuposa mmene imatenthela nthawi zonse!’ Ndiyeno auza asilikali ake amphamvu kwambili kuti amange Sadirake, Mesake, ndi Abedinego ndi kuwaponya mu ng’anjo. Ng’anjo ni yotentha kwambili cakuti amuna amphamvu amenewa akufa ndi malawi a moto cabe. Nanga n’ciani cacitikila anyamata atatu amene aponyedwa mu ng’anjo?
Mfumu iyang’ana mu ng’anjo ndipo icita mantha kwambili. Ifunsa kuti: ‘Kodi sitinamange amuna atatu ndi kuwaponya mu ng’anjo ya moto?’
Asilikali ake ayankha kuti: ‘Inde n’zimene tacita.’
Ndiyeno mfumu ikamba kuti: ‘Koma niona amuna anai amene ayenda-yenda pakati pa moto. Iwo siomangidwa, komanso sakupsa iyai. Ndipo wacinai aoneka ngati mulungu.’ Ndiyeno mfumu iyenda kufupi ndi citseko ca ng’anjo ndi kufuula kuti: ‘Sadirake! Mesake! Abedinego! Tulukani, atumiki a Mulungu Wam’mwamba-mwamba!’
Pamene atuluka, anthu onse aona kuti io sanapse. Ndiyeno mfumu ikamba kuti: ‘Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesake, ndi Abedinego! Iye watumiza mngelo wake kuti awapulumutse cifukwa anakana kugwadila ndi kulambila milungu ina kupatulapo iye.’
Kodi sicitsanzo cabwino ca kukhulupilika kwa Yehova cimene tiyenela kutsatila?
Ekisodo 20:3; Danieli 3:1-30.