Nkhani 83
Mpanda Wa Yerusalemu
ONA nchito imene icitika apa. Aisiraeli atangwanika ndi nchito yomanga mpanda kapena kuti cipupa ca Yerusalemu. Pamene Mfumu Nebukadinezara anaononga Yerusalemu zaka 152 zapita, anagwetsa mpanda ndi kuocha zitseko za zipata za mzinda. Aisiraeli sanamangenso mpanda pamene anabwelela kucoka ku Babulo.
Kodi uganiza kuti anthu anali kumvela bwanji kukhala zaka zonsezi mu mzinda ulibe mpanda? Sanali kudzimva kukhala ochinjilizika. Adani ao anali kuloŵa mosavuta ndi kuwaukila. Koma tsopano munthu uyu Nehemiya wabwela kudzathandiza anthu kumanganso mpanda. Kodi umudziŵa Nehemiya?
Nehemiya ni Mwisiraeli amene acokela ku mzinda wa Susani, kumene Mordekai ndi Esitere akhala. Nehemiya anali kuseŵenza ku nyumba ya mfumu, mwina anali mnzake wa Mordekai ndi Mfumukazi Esitere. Koma Baibo siimafotokoza kuti Nehemiya anali kuseŵenzela Mfumu Ahasiwero, mwamuna wa Esitere. Anali kuseŵenzela Mfumu yotsatila, Mfumu Aritasasta.
Kumbukila kuti, Aritasasta anali mfumu yabwino imene inapatsa Ezara ndalama zambili kuti apeleke ku Yerusalemu kuti akakonze kacisi wa Yehova. Koma Ezara sanamange mpanda wa mzinda umene unagwa. Tiye tione zimene zinacitika kuti Nehemiya acite nchito imeneyi.
Papita zaka 13 kucokela pamene Aritasasta anapatsa Ezara ndalama zokonzela kacisi. Ndipo tsopano Nehemiya ni wopelekela cikho wamkulu wa Mfumu Aritasasta. Zimenezi zitanthauza kuti iye apeleka vinyo kwa mfumu, ndi kuonetsetsa kuti palibe munthu amene afuna kuikila mfumu poizoni. Nchito iyi ni yofunika kwambili.
Tsiku lina Hanani m’bale wa Nehemiya, ndi amuna ena ocokela ku dziko la Isiraeli abwela kudzaona Nehemiya. Ndiyeno amuuza vuto limene Aisiraeli ali nalo, ndi kugwa kwa mpanda wa Yerusalemu. Zimenezi zicititsa Nehemiya kumva cisoni kwambili, ndipo ayamba kuchula nkhani imeneyi m’mapemphelo ake kwa Yehova.
Tsiku lina mfumu iona kuti Nehemiya ali ndi cisoni, conco imufunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani uoneka wacisoni?’ Nehemiya auza mfumu kuti n’cifukwa cakuti Yerusalemu ali mu mkhalidwe woipa ndi kuti mpanda niwakugwa. Ndipo mfumu imufunsa kuti: ‘Kodi ufuna ciani?’.
Nehemiya ayankha kuti: ‘Niloleni niyende ku Yerusalemu kuti nikamangenso mpanda.’ Mfumu Aritasasta ni wokoma mtima kwambili. Alola Nehemiya kupita, ndipo amuthandiza kupeza mapulanga omangila. Pamene Nehemiya anangofika ku Yerusalemu, anauza anthu za lingalilo lake. Anthu analikonda lingalilo lake ndipo anati: ‘Tiyeni tiyambe kumanga.’
Pamene adani a Aisiraeli aona kuti mpanda wayamba kukwela, akamba kuti: ‘Tidzapita kuwapha, ndi kuimitsa nchito yomanga.’ Koma pamene Nehemiya amvela zimenezi, apatsa anchito malupanga ndi mikondo. Ndipo akamba kuti: ‘Musaope adani athu. Menyelani nkhondo abale anu, ana anu, akazi anu, ndi nyumba zanu.’
Anthu ni olimba mtima kwambili. Iwo asunga zida zao usana ndi usiku, ndipo apitilizabe kumanga. Conco atsiliza kumanga mpanda m’masiku 52 okha. Tsopano anthu akumva kukhala ochinjilizika mkati mwa mzinda. Nehemiya ndi Ezara aphunzitsa anthu cilamulo ca Mulungu, ndipo anthu ni okondwela.
Koma zinthu sizili monga mmene zinalili kale, pamene Aisiraeli anali mu ukapolo ku Babulo. Mfumu ya Aperisiya ndiye ilamulila anthu ndipo ndi imene amatumikila. Koma Yehova walonjeza kuti adzatumiza mfumu yatsopano, ndipo mfumu imeneyi idzabweletsa mtendele kwa anthu. Kodi mfumu imeneyi ndani? Ndipo idzabweletsa bwanji mtendele padziko? Zaka pafupi-fupi 450 zipita pakalibe kumveka ciliconse cokhudza nkhani imeneyi. Koma potsilizila pake, kubadwa mwana wofunika kwambili. Tidzamvela zambili m’nkhani zotsatilapo.
Nehemiya caputa 1 mpaka 6.