Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ophunzilila Buku Langa la Nkhani za m’Baibo

Mafunso Ophunzilila Buku Langa la Nkhani za m’Baibo

Nkhani 1

Mulungu Ayamba Kupanga Vinthu

  1. Kodi zinthu zabwino zonse zinacokela kuti? Nanga ungachuleko zinthu zabwino ziti?

  2. Cinthu coyamba cimene Mulungu anapanga cinali ciani?

  3. N’cifukwa ciani mngelo woyamba anali wapadela?

  4. Fotokoza mmene dziko linalili paciyambi? (Ona cithunzi-thunzi.)

  5. Kodi Mulungu anayamba bwanji kukonza dziko lapansi kuti zinyama ndi anthu akhalepo?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yeremiya 10:12.

    Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu amene amaonekela mu cilengedwe cake? (Yes. 40:26; Aroma 11:33)

  2. Ŵelenga Akolose 1:15-17.

    Kodi Yesu anacita mbali yanji polenga zinthu, ndipo tiyenela kumuona bwanji pacifukwa cimeneci? (Akol. 1:15-17)

  3. Ŵelenga Genesis 1:1-10.

    1. Ndani anapanga dziko lapansi? (Gen. 1:1)

    2. N’ciani cinacitika patsiku loyamba la kulenga? (Gen. 1:3-5)

    3. Fotokoza zimene zinacitika patsiku laciŵili la kulenga? (Gen. 1:7, 8)

Nkhani 2

Munda Wokongola

  1. Kodi Mulungu anakonza bwanji dziko lapansi kuti likhale malo athu?

  2. Fotokoza zinyama zosiyana-siyana zimene Mulungu anapanga. (Ona pacithunzi-thunzi.)

  3. N’cifukwa ciani munda wa Edeni unali wapadela?

  4. Kodi Mulungu anafuna kuti dziko lonse lapansi likhale bwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 1:11-25.

    1. Mulungu analenga ciani patsiku lacitatu lolenga zinthu? (Gen. 1:12)

    2. N’ciani cinacitika patsiku lacinai? (Gen. 1:16)

    3. Kodi Mulungu analenga nyama ziti patsiku lacisanu, ndi patsiku lacisanu ndi cimodzi? (Gen. 1:20, 21, 25)

  2. Ŵelenga Genesis 2:8,9.

    Ni mitengo iŵili iti yapadela imene Mulungu anaika m’munda wa Edeni, ndipo inali kuimila ciani?

Nkhani 3

Mwamuna ndi Mkazi Woyamba

  1. Kodi cithunzi-thunzi ca m’nkhani namba 3 cisiyana bwanji na cithunzi-thunzi ca m’nkhani namba 2?

  2. Ndani anapanga mwamuna woyamba, ndipo dzina la mwamuna ameneyo anali ndani?

  3. Kodi Mulungu anapatsa Adamu nchito yanji?

  4. N’cifukwa ciani Mulungu anagoneka Adamu tulo tofa nato?

  5. Kodi Adamu ndi Hava akanakhala kwautali wabwanji, ndipo Mulungu anali kufuna kuti io acite nchito yanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Masalimo 83:18.

    Kodi dzina la Mulungu ndani, ndipo ali ndi udindo wapadela wabwanji padziko lapansi? (Yer. 16:21; Dan. 4:17)

  2. Ŵelenga Genesis 1:26-31.

    1. Patsiku lacisanu ndi cimodzi, kodi Mulungu analenga cinthu capadela citi, ndipo colengedwa cimeneci cinasiyana bwanji ndi zinyama? (Gen. 1:26)

    2. Kodi n’cakudya canji cimene Yehova anapangila anthu ndi zinyama? (Gen. 1:30)

  3. Ŵelenga Genesis 2:7-25.

    1. Kodi Adamu anali kupatsa bwanji zinyama maina? (Gen. 2:19)

    2. Lemba la Genesis 2:24 limatithandiza bwanji kumvetsetsa mmene Yehova amaonela zinthu zitatu izi; cikwati, kupatukana ndi kulekana? (Mat. 19:4-6, 9)

Nkhani 4

Mmene Anataila Malo Ao Okhalako

  1. Pacithunzi-thunzi ico, kodi n’ciani cicitika kwa Adamu ndi Hava?

  2. N’cifukwa ciani Yehova anawalanga?

  3. Kodi njoka inauza Hava ciani?

  4. Ndani anacititsa kuti njoka ikambe ndi Hava?

  5. N’cifukwa ciani Adamu ndi Hava anataya malo ao a Paladaiso?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 2:16, 17 ndi 3:1-13, 24.

    1.   

    2. Kodi Hava akhala bwanji citsanzo coticenjeza? (Afil. 4:8; Yak. 1:14, 15; 1 Yoh. 2:16)

    3. Kodi Adamu ndi Hava anaonetsa bwanji kuti aliyense sanavomele kulakwa kwake? (Gen. 3:12, 13)

    4. Kodi angelo amene anaikidwa kum’mawa kwa munda wa Edeni anacilikiza bwanji ulamulilo wa Yehova? (Gen. 3:24)

  2. Ŵelenga Chivumbulutso 12:9.

    Kodi Satana wapandutsa anthu ambili bwanji ku ulamulilo wa Mulungu? (1 Yoh. 5:19)

Nkhani 5

Kuyamba kwa Umoyo Wovuta

  1. Kodi umoyo wa Adamu ndi Hava unakhala wabwanji kunja kwa munda wa Edeni?

  2. N’ciani cinayamba kucitika kwa Adamu ndi Hava, ndipo n’cifukwa ninji?

  3. N’cifukwa ciani ana a Adamu ndi Hava anayamba kukalamba ndi kufa?

  4. Sembe Adamu ndi Hava anamvela Yehova, kodi umoyo wao ndi wa ana ao ukanakhala wabwanji?

  5. Kodi kusamvela kwa Hava kunamubweletsela zoŵaŵa zabwanji?

  6. Kodi ana aŵili oyamba a Adamu ndi Hava maina ao ndani?

  7. Nanga ana ena amene ali pacithunzi-thunzi apa ndani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 3:16-23 ndi 4:1, 2.

    1. Pamene nthaka inatembeleledwa, kodi umoyo wa Adamu unakhala wabwanji? (Gen. 3:17-19; Aroma 8:20, 22)

    2. N’cifukwa ciani dzina lakuti Hava lotanthauza “Wamoyo,” lili loyenelela? (Gen. 3:20)

    3. Kodi Yehova anaonetsa bwanji cifundo kwa Adamu ndi Hava, ngakhale kuti anacimwa? (Gen. 3:7, 21)

  2. Ŵelenga Chivumbulutso 21:3, 4.

    Kodi ni ‘zinthu zakale’ ziti zimene umafuna kwambili kuti zikacotsedwe?

Nkhani 6

Mwana Wabwino, ndi Mwana Woipa

  1. Kodi Kaini ndi Abele anali kugwila nchito zanji?

  2. Kodi Kaini ndi Abele anabweletsa nsembe zabwanji kwa Yehova?

  3. N’cifukwa ciani Yehova anakondwela ndi nsembe ya Abele? Nanga n’cifukwa ciani sanakondwele ndi nsembe ya Kaini?

  4. Kodi Kaini ni munthu wabwanji, ndipo Yehova anayesa kumuongolela bwanji?

  5. Kaini anacita ciani pamene anali aŵili cabe ndi mng’ono wake kumunda?

  6. Fotokoza cimene cinacitika kwa Kaini pamene anapha mng’ono wake.

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 4:2-26.

    1. Kodi Yehova anamucenjeza za ciani Kaini? (Gen. 4:7)

    2. Kodi Kaini anaonetsa bwanji zimene zinali mu mtima mwake? (Gen. 4:9)

    3. Kodi Yehova amakuona bwanji kupha anthu osalakwa? (Gen. 4:10; Yes. 26:21)

  2. Ŵelenga 1 Yohane 3:11, 12.

    1. N’cifukwa ciani Kaini anakalipa kwambili, ndipo zimenezi zili cenjezo labwanji kwa ife? (Gen. 4:4, 5; Miy. 14:30; 28:22)

    2. Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti ngakhale ngati apabanja athu onse atsutsa Yehova, ife tikhoza kukhalabe okhulupilika kwa iye? (Sal. 27:10; Mat. 10:21, 22)

  3. Ŵelenga Yohane 11:25.

    Kodi n’citsimikizo canji cimene Yehova wapeleka kwa anthu amene anafa cifukwa cocita cilungamo? (Yoh. 5:24)

Nkhani 7

Munthu Wopanda Mantha

  1. Kodi Inoki anali wosiyana bwanji ndi anthu ena?

  2. N’cifukwa ciani anthu m’nthawi ya Inoki anali kucita vinthu voipa kwambili?

  3. Kodi anthu anali kucita vinthu voipa vabwanji? (Ona pacithunzi-thunzi.)

  4. N’cifukwa ciani Inoki anafunikila kukhala wopanda mantha?

  5. Kodi anthu anali kukhala nthawi yaitali bwanji m’masiku amenewo? Nanga Inoki anakhala moyo kwa nthawi yaitali bwanji?

  6. N’ciani cinacitika pambuyo pa kumwalila kwa Inoki?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 5:21-24, 27.

    1. Kodi panali unansi wanji pakati pa Inoki ndi Yehova? (Gen. 5:24)

    2. Malinga ndi Baibo, kodi ndi munthu uti amene anakhala zaka zambili kupambana anthu onse? Nanga anali ndi zaka zingati pamene anamwalila? (Gen. 5:27)

  2. Ŵelenga Genesis 6:5.

    Kodi zinthu padziko lapansi zinaipa kwambili bwanji pambuyo pa imfa ya Inoki, ndipo zifanana bwanji ndi masiku ano? (2 Tim. 3:13)

  3. Ŵelenga Aheberi 11:5.

    Kodi ni khalidwe lanji la Inoki limene linakondweletsa kwambili Mulungu, ndipo panakhala zotsatilapo zabwanji? (Gen. 5:22.)

  4. Ŵelenga Yuda 14, 15.

    Kodi Akristu masiku ano angakhale bwanji opanda mantha monga Inoki pamene acenjeza anthu za nkhondo ya Aramagedo imene idzabwela? (2 Tim. 4:2; Aheb. 13:6)

Nkhani 8

Vimphona Padziko Lapansi

  1. Kodi n’ciani cinacitika pamene angelo a Mulungu ena anamvela Satana?

  2. N’cifukwa ciani angelo ena anasiya nchito yao kumwamba ndi kubwela padziko lapansi?

  3. N’cifukwa ciani kunali kulakwa kuti angelo abwele padziko lapansi ndi kuvala matupi aumunthu?

  4. Kodi ana a angelo anali osiyana bwanji ndi ana ena?

  5. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi ana a angelo acita ciani pamene akhala vimphona?

  6. Inoki atamwalila, kodi ni munthu wabwino uti amene anakhala padziko lapansi, ndipo n’cifukwa ciani Mulungu anali kumukonda?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 6:1-8.

    Kodi lemba la Genesis 6:6 limaonetsa bwanji kuti Yehova amakhudzidwa ndi zocita zathu?

  2. Ŵelenga Yuda 6.

    Kodi “angelo amene sanasunge malo ao oyambilila” m’nthawi ya Nowa apeleka cenjezo lanji kwa ife? (1 Akor. 3:5-9; 2 Pet. 2:4, 9, 10)

Nkhani 9

Nowa Apanga Cingalawa

  1. Kodi m’banja la Nowa munali anthu angati, ndipo ana ake amuna atatu anali ndani maina ao?

  2. Kodi n’cinthu capadela citi cimene Mulungu anapempha Nowa kuti acite, ndipo n’cifukwa ciani?

  3. Kodi anthu amene anali kukhala pafupi ndi Nowa anacita ciani pamene anauzidwa za kupanga cingalawa?

  4. Kodi Mulungu anauza Nowa kuti acite ciani ndi zinyama?

  5. Pambuyo pakuti Mulungu watseka citseko ca cingalawa, kodi Nowa ndi banja lake anafunikila kucita ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 6:9-22.

    1. N’ciani cinacititsa Nowa kukhala wolambila wabwino kwambili wa Mulungu woona? (Gen. 6:9, 22)

    2. Kodi Yehova amamva bwanji akaona zaciwawa, ndipo zimenezi ziyenela kukhudza bwanji zosangulutsa zimene timasankha? (Gen. 6:11, 12; Sal. 11:5)

    3. Tingatsatile bwanji citsanzo ca Nowa pamene tilandila malangizo m’gulu la Yehova? (Gen. 6:22; 1 Yoh. 5:3)

  2. Ŵelenga Genesis 7:1-9.

    Kodi mfundo yakuti Yehova anaona Nowa, munthu wopanda ungwilo, kukhala wolungama, imatilimbikitsa bwanji masiku ano? (Gen. 7:1; Miy. 10:16; Yes. 26:7)

Nkhani 10

Cigumula Cacikulu

  1. N’cifukwa ciani palibe amene akanaloŵa m’cingalawa pamene mvula inayamba?

  2. Kodi Yehova analola mvula kuti igwe masiku angati, ndipo madzi anaculuka bwanji?

  3. Kodi cingalawa cinacita bwanji pamene madzi anayamba kuphimba dziko lonse?

  4. Kodi vimphona vinapulumuka Cigumula? Nanga n’ciani cinacitika kwa atate a vimphona?

  5. Kodi cingalawa cinacita bwanji pambuyo pa miyezi isanu?

  6. 6. N’cifukwa ciani Nowa anatulutsa khwangwala m’cingalawa?

  7. Kodi Nowa anadziŵa bwanji kuti madzi acepa padziko lapansi?

  8. 8. Kodi Mulungu anati ciani kwa Nowa pamene iye ndi banja lake anakhala m’cingalawa kwa nthawi yopitilila caka cimodzi?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 7:10-24.

    1. Kodi Mulungu anaonongelatu zamoyo zonse padziko lapansi? (Gen. 7:23)

    2. Kodi madzi a Cigumula anatenga nthawi yaitali bwanji kuti aphwilile?

  2. Ŵelenga Genesis 8:1-17.

    Kodi lemba la Genesis 8:17 lionetsa bwanji kuti colinga ca Yehova coyambilila ca dziko lapansi sicinasinthe? (Gen. 1:22)

  3. Ŵelenga 1 Petulo 3:19, 20.

    1. Pamene angelo opanduka anabwelela kumwamba, kodi anapatsidwa cilango cabwanji? (Yuda 6)

    2. Kodi nkhani ya Nowa ndi banja lake, imalimbitsa bwanji cidalilo cathu cakuti Yehova ali ndi mphamvu zopulumutsa anthu ake? (2 Pet. 2:9)

Nkhani 11

Utawaleza Woyamba

  1. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi cinthu coyamba cimene Nowa anacita pamene anatuluka m’cingalawa n’ciani?

  2. Kodi ni lamulo liti limene Mulungu anapatsa Nowa ndi banja lake pambuyo pa Cigumula?

  3. Kodi Mulungu analonjeza ciani?

  4. Tikaona utawaleza, uyenela kutikumbutsa lonjelo liti?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 8:18-22.

    1. Kodi masiku ano, tingapeleke bwanji “fungo lokhazika mtima pansi” kwa Yehova? (Gen. 8:21; Aheb. 13:15, 16)

    2. Kodi Yehova anena ciani za mmene mtima wa munthu ulili? Nanga tiyenela kukhala osamala bwanji? (Gen. 8:21; Mat. 15:18, 19)

  2. Ŵelenga Genesis 9:9-17.

    1. Kodi Yehova anacita cipangano cabwanji ndi zamoyo zonse za padziko lapansi? (Gen. 9:10, 11)

    2. Kodi cipangano ca utawaleza cidzakhala cikugwila ntchito mpaka liti? (Gen. 9:16)

Nkhani 12

Anthu Amanga Cinsanja

  1. Kodi Nimurodi anali ndani, ndipo Mulungu anali kumuona bwanji?

  2. N’cifukwa ciani anthu amene ali pacithunzi-thunzi aumba nchelwa?

  3. N’cifukwa ciani Yehova sanakondwele ndi nchito yao yomanga?

  4. Kodi Mulungu anaimitsa bwanji nchito yomanga cinsanja?

  5. Kodi mzinda unali kuchedwa kuti ciani, ndipo dzina limenelo linali kutanthauza ciani?

  6. N’ciani cinacitika kwa anthu pamene Mulungu anasokoneza zinenelo zao?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 10:1, 8-10.

    Kodi Nimurodi anaonetsa makhalidwe abwanji, ndipo zimenezi zitipatsa cenjezo lanji? (Miy. 3:31)

  2. Ŵelenga Genesis 11:1-9.

    Kodi colinga comangila cinsanja cimeneco cinali ciani, ndipo n’cifukwa ninji nchito imeneyi inalephela? (Gen. 11:4; Miy. 16:18; Yoh. 5:44)

Nkhani 13

Abulahamu—Mnzake wa Mulungu

  1. Kodi ni anthu abwanji amene anali kukhala mu mzinda wa Uri?

  2. Mwamuna amene ali pacithunzi-thunzi apa ndani? Nanga anabadwa liti? Ndipo anali kukhala kuti?

  3. Kodi Mulungu anauza Abulahamu kucita ciani?

  4. N’cifukwa ciani Abulahamu anachedwa mnzake wa Mulungu?

  5. Pamene Abulahamu anacoka ku Uri, ndani amene anayenda naye pamodzi?

  6. Kodi Mulungu anauza ciani Abulahamu pamene anafika ku dziko la Kanani?

  7. Kodi Mulungu analonjeza ciani Abulahamu pamene anali ndi zaka 99?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 11:27-32.

    1. Kodi panali cibale canji pakati pa Abulahamu ndi Loti? (Gen. 11:27)

    2. Ngakhale kuti Tera anayamikilidwa cifukwa cosamutsila banja lake ca ku Kanani, kodi tidziŵa bwanji kuti Abulahamu ni amene kweni-kweni anayambitsa ulendowu, ndipo n’cifukwa ciani anacita zimenezi? (Gen. 11:31; Mac. 7:2-4)

  2. Ŵelenga Genesis 12:1-7.

    Kodi Yehova anakulitsa bwanji cipangano ca Abulahamu pamene Abulahamu anafika ku dziko la Kanani? (Gen. 12:7)

  3. Ŵelenga Genesis 17:1-8, 15-17.

    1. Pamene anakhala ndi zaka 99, dzina la Abulamu linasinthidwa kukhala ndani, ndipo n’cifukwa ciani? (Gen. 17:5)

    2. Kodi Yehova analonjeza Sara madalitso abwanji? (Gen. 17:15, 16)

  4. Ŵelenga Genesis 18:9-19.

    1. Lemba la Genesis 18:19, limafotokoza udindo uti wa atate? (Deut. 6:6, 7; Aef. 6:4)

    2. Kodi n’cokumana naco citi ca Sara cimene cimaonetsa kuti palibe cimene tingabise kwa Yehova? (Gen. 18:12, 15; Sal. 44:21)

Nkhani 14

Mulungu Ayesa Cikhulupililo ca Abulahamu

  1. Kodi Mulungu analonjeza Abulahamu ciani, ndipo anakwanilitsa bwanji lonjezo lake?

  2. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi Mulungu anayesa bwanji cikhulupililo ca Abulahamu?

  3. Nanga Abulahamu anacita ciani, ngakhale kuti sanamvetsetse cifukwa cake Mulungu analamula zimenezo?

  4. Kodi cinacitika n’ciani pamene Abulahamu anacotsa mpeni kuti aphe mwana wake?

  5. Kodi cikhulupililo ca Abulahamu mwa Mulungu cinali colimba bwanji?

  6. Kodi Mulungu anapatsa Abulahamu ciani kuti apeleke nsembe? Kodi anam’patsa bwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 21:1-7.

    N’cifukwa ciani Abulahamu anacita mdulidwe mwana wake patsiku la cisanu ndi citatu? (Gen. 17:10-12; 21:4)

  2. Ŵelenga Genesis 22:1-18.

    Kodi Isaki anaonetsa bwanji kugonjela atate ake, Abulahamu? Nanga zimenezi zinacitila bwanji cithunzi cocitika capadela camtsogolo? (Gen. 22:7-9; 1 Akor. 5:7; Afil. 2:8, 9)

Nkhani 15

Mkazi wa Loti Anayang’ana Kumbuyo

  1. N’cifukwa ciani Abulahamu ndi Loti anapatukana?

  2. N’cifukwa ciani Loti anasankha kukakhala mu Sodomu?

  3. Kodi anthu a ku Sodomu anali a makhalidwe abwanji?

  4. Kodi n’cenjezo lakuti ciani limene angelo aŵili anapeleka kwa Loti?

  5. N’cifukwa ciani mkazi wa Loti anasanduka mwala wamcele?

  6. Kodi zimene zinacitikila mkazi wa Loti zitiphunzitsa ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 13:5-13.

    Ponena za kuthetsa mavuto amene tingakhale nao ndi anzathu, kodi tiphunzila ciani kwa Abulahamu? (Gen. 13:8, 9; Aroma 12:10; Afil. 2:3, 4)

  2. Ŵelenga Genesis 18:20-33.

    Kodi mmene Yehova anacitila zinthu ndi Abulahamu zimatipatsa bwanji cidalilo cakuti Yehova ndi Yesu adzaweluza mwacilungamo? (Gen. 18:25, 26; Mat. 25:31-33)

  3. . Ŵelenga Genesis 19:1-29.

    1. Kodi nkhani ya m’Baibo iyi imaonetsa ciani za mmene Mulungu amaonela kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha, kapena kuti kucita zauhomo? (Gen. 19:5, 13; Lev. 20:13)

    2. Kodi pali kusiyana kwanji pakati pa Loti ndi Abulahamu, tikaona mmene analabadilila malangizo a Mulungu? Nanga tiphunzila ciani pa zimenezi? (Gen. 19:15, 16, 19, 20; 22:3)

  4. Ŵelenga Luka 17:28-32.

    Kodi mkazi wa Loti anaonetsa mtima wabwanji pankhani ya zinthu zakuthupi? Nanga zimenezi ziticenjeza bwanji? (Luka 12:15; 17:31, 32; Mat. 6:19-21, 25)

  5. Ŵelenga 2 Petulo 2:6-8.

    Potengela citsanzo ca Loti, kodi tiyenela kuliona bwanji dziko lino la anthu osakonda Mulungu? (Ezek. 9:4; 1 Yoh. 2:15-17)

Nkhani 16

Isaki Apeza Mkazi Wabwino

  1. Kodi mwamuna ndi mkazi amene ali pacithunzi-thunzi apa ndani?

  2. Kodi Abulahamu anacita ciani kuti apezele mwana wake mkazi, ndipo cifukwa ciani?

  3. Kodi pemphelo la mtumiki wa Abulahamu linayankhidwa bwanji?

  4. Kodi Rabeka anayankha bwanji pamene anafunsidwa ngati afuna kukwatilana ndi Isaki?

  5. Kodi n’ciani cinacititsa kuti Isaki akhalenso wokondwela?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 24:1-67.

    1. Kodi Rabeka anaonetsa makhalidwe abwino ati pamene anakumana ndi mtumiki wa Abulahamu pacitsime? (Gen. 24:17-20; Miy. 31:17, 31)

    2. Zimene Abulahamu anakonzela Isaki zipeleka citsanzo cabwino cabwanji kwa Akristu masiku ano? (Gen. 24:37, 38; 1 Akor. 7:39; 2 Akor. 6:14)

    3. N’cifukwa ciani tifunika kupeza nthawi yosinkha-sinkha, monga mmene Isaki anacitila? (Gen. 24:63; Sal. 77:12; Afil. 4:8)

Nkhani 17

Amapasa Osiyana

  1. Kodi Esau ndi Yakobo anali ndani, ndipo anali osiyana bwanji?

  2. Kodi Esau ndi Yakobo anali ndi zaka zingati pamene ambuye wao Abulahamu anamwalila?

  3. Kodi n’ciani cimene Esau anacita cimene cinakalipitsa kwambili amai ndi atate ake?

  4. N’cifukwa ciani Esau anakalipa kwambili ndi zimene mng’ono wake Yakobo anacita?

  5. Kodi Isaki anapeleka malangizo anji kwa mwana wake, Yakobo?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 25:5-11, 20-34.

    1. Kodi Yehova analosela ciani za ana amuna aŵili a Rabeka? (Gen. 25:23)

    2. Kodi Yakobo ndi Esau anali kuiona mosiyana bwanji nkhani ya kukhala woyamba kubadwa? (Gen. 25:31-34)

  2. Ŵelenga Genesis 26:34, 35; 27:1-46; ndi 28:1-5.

    1. Kodi Esau anaonetsa bwanji kuti anali ndi mtima wosayamikila zinthu za kuuzimu? (Gen. 26:34, 35; 27:46)

    2. Kuti Yakobo alandile dalitso la Mulungu, kodi Isaki anamuuza kucita ciani? (Gen. 28:1-4)

  3. Ŵelenga Aheberi 12:16, 17.

    Kodi citsanzo ca Esau cionetsa bwanji zotulukapo zimene anthu amene amanyalanyaza zinthu zopatulika angakumane nazo?

Nkhani 18

Yakobo Ayenda ku Harana

  1. Kodi mkazi wacitsikana ali pacithunzi-thunzi apa ndani, ndipo Yakobo anamucitila ciani?

  2. Kodi Yakobo anali wokonzeka kucita ciani kuti akwatile Rakele?

  3. Kodi Labani anacita ciani pamene nthawi yakuti Yakobo akwatile Rakele inafika?

  4. Kodi Yakobo anavomela kucita ciani kuti atenge Rakele kukhala mkazi wake?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 29:1-30.

    1. Ngakhale kuti Labani anapusitsa Yakobo, kodi Yakobo anadzilemekeza bwanji, ndipo tingaphunzile ciani pa zimenezi? (Gen. 25:27; 29:26-28; Mat. 5:37)

    2. Kodi citsanzo ca Yakobo cionetsa bwanji kusiyana pakati pa cikondi ceni-ceni ndi kungotengeka maganizo? (Gen. 29:18, 20, 30; Nyimbo 8:6)

    3. Kodi ndi akazi anai ati amene anakhala a m’nyumba ya Yakobo, ndipo panthawi ina anam’belekela ana amuna? (Gen. 29:23, 24, 28, 29)

Nkhani 19

Yakobo Ali ndi Banja Lalikulu

  1. Kodi ana 6 amene Yakobo anabala kwa mkazi wake woyamba Leya anali ndani maina ao?

  2. Kodi ana aŵili amene Zilipa kapolo wa Leya anabala kwa Yakobo anali ndani?

  3. Kodi ana aŵili amene Biliha kapolo wa Rakele anabala kwa Yakobo anali ndani?

  4. Kodi ana aŵilli amene Rakele anabala anali ndani, koma n’ciani cinacitika pamene mwana waciŵili anabadwa?

  5. Monga mmene tionela pacithunzi-thunzi, Yakobo anali ndi ana amuna angati, ndipo mwa io munacokela ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 29:32-35; 30:1-26 ndi 35:16-19.

    Monga mmene taonela ndi ana amuna 12 a Yakobo, kodi m’nthawi zakale anyamata aciheberi nthawi zambili anali kupatsidwa bwanji maina?

  2. Ŵelenga Genesis 37:35.

    Ngakhale kuti Dina yekha ndiye achulidwa m’Baibo, kodi tidziŵa bwanji kuti Yakobo anali ndi ana ena akazi? (Gen. 37:34, 35)

Nkhani 20

Dina Agwela m’Mavuto

  1. N’cifukwa ciani Abulahamu ndi Isaki sanafune kuti ana ao akwatile anthu a m’dziko la Kanani?

  2. Kodi Yakobo anavomeleza kuti mwana wake wamkazi akhale paubwenzi ndi atsikana acikanani?

  3. Kodi mwamuna amene ayang’ana Dina pacithunzi-thunzi apa ndani, ndipo anacita cinthu coipa cabwanji?

  4. Kodi Simiyoni ndi Levi, alongosi a Dina, anacita ciani pamene anamva zimene zinacitika?

  5. Kodi Yakobo anakondwela ndi zimene Simiyoni ndi Levi anacita?

  6. Kodi mavuto okhudza banja lonse anayamba bwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 34:1-31.

    1. Kodi kuceza kwa Dina ndi atsikana acikanani kunangocitika kamodzi cabe? Fotokoza. (Gen. 34:1)

    2. N’cifukwa ciani Dina naye analipo ndi mbali pa kutaya unamwali wake? (Agal. 6:7)

    3. Kodi acicepele masiku ano angaonetse bwanji kuti amamvela cenjezo la zimene zinacitikila Dina? (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33; 1 Yoh. 5:19)

Nkhani 21

Abale a Yosefe Amuzonda

  1. N’cifukwa ciani abale a Yosefe am’citila nsanje, ndipo io acita ciani?

  2. Kodi abale a Yosefe afuna kucita ciani kwa iye, ndipo Rubeni akamba ciani?

  3. N’ciani cicitika pamene Aisimaeli amalonda apita mu njila?

  4. Kodi abale a Yosefe acita ciani kuti atate ao aganize kuti Yosefe waphedwa?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 37:1-35.

    1. Kodi Akristu angatsatile bwanji citsanzo ca Yosefe mwa kuulula zolakwa mumpingo? (Gen. 37:2; Lev. 5:1; 1 Akor. 1:11)

    2. Kodi n’ciani cinacititsa kuti abale a Yosefe amucitile zinthu zoipa? (Gen. 37:11, 18; Miy. 27:4; Yak. 3:14-16)

    3. Kodi Yakobo anacita ciani cimene n’cacibadwa kucita polila malilo? (Gen. 37:35)

Nkhani 22

Yosefe Aponyedwa m’Ndende

  1. Kodi Yosefe ali ndi zaka zingati pamene atengedwa ku Iguputo, ndipo cicitika n’ciani pamene afika kumeneko?

  2. Kodi Yosefe apezeka bwanji m’ndende?

  3. Kodi Yosefe apatsidwa udindo wanji m’ndende?

  4. M’ndende, n’ciani cimene Yosefe acitila wopelekela cikho ndi wophika mkate wa Farao?

  5. Kodi n’ciani cicitika pamene wopelekela cikho acotsedwa m’ndende?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 39:1-23.

    Popeza kuti m’nthawi ya Yosefe kunalibe lamulo lolembedwa la Mulungu loletsa cigololo, kodi n’ciani cinamucititsa kuti athawe kwa mkazi wa Potifara? (Gen. 2:24; 20:3; 39:9)

  2. Ŵelenga Genesis 40:1-23.

    1. Mwacidule, fotokoza loto la wopelekela cikho ndi tanthauzo lake limene Yehova anapeleka kwa Yosefe. (Gen. 40:9-13)

    2. Kodi wophika mkate analota ciani, ndipo loto lake linatanthauza ciani? (Gen. 40:16-19)

    3. Kodi gulu la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu limatengela bwanji citsanzo ca maganizo a Yosefe? (Gen. 40:8; Sal. 36:9; Yoh. 17:17; Mac. 17:2, 3)

    4. Kodi lemba la Genesis 40:20 limanena ciani za mmene Akristu amaonela kukondwelela tsiku lakubadwa? (Mlal. 7:1; Marko 6:21-28)

Nkhani 23

Maloto a Farao

  1. Kodi n’ciani cinacitikila Farao usiku wina?

  2. Kodi n’ciani cinapangitsa wopelekela cikho kukumbukila Yosefe potsilizila pake?

  3. Monga mmene tionela pacithunzi-thunzi, kodi Farao alota maloto aŵili abwanji?

  4. Kodi Yosefe akamba kuti maloto amenewo atanthauza ciani?

  5. Kodi Yosefe akhala bwanji munthu waciŵili kwa Farao mu Iguputo?

  6. N’cifukwa ciani abale a Yosefe abwela ku Iguputo, ndipo n’cifukwa ciani sanamudziŵe?

  7. Kodi Yosefe akumbukila loto lakuti bwanji, ndipo limuthandiza kumvetsetsa ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 41:1-57.

    1. Kodi Yosefe anayang’ana bwanji kwa Yehova, ndipo Akristu masiku ano angatengele bwanji citsanzo cake? (Gen. 41:16, 25, 28; Mat. 5:16; 1 Pet. 2:12)

    2. Kodi zaka za cakudya coculuka ndi zaka za njala mu Iguputo, zimaonetsa bwino bwanji kusiyana kwa mkhalidwe wauzimu wa anthu a Yehova masiku ano ndi wa Machalichi Acikristu? (Gen. 41:29, 30; Amosi 8:11, 12)

  2. Ŵelenga Genesis 42:1-8 ndi 50:20.

    Kodi n’kulakwa ngati olambila Yehova aŵelamila munthu waudindo kuti amuonetse ulemu mogwilizana ndi mwambo wa m’dziko lao? (Gen. 42:6)

Nkhani 24

Yosefe Ayesa Abale ake

  1. N’cifukwa ciani Yosefe anamizila abale ake kuti ni azondi?

  2. N’cifukwa ciani Yakobo avomeleza kuti mwana wake wamng’ono, Benjamini, ayende ku Iguputo?

  3. Kodi kapu yasiliva ya Yosefe ipezeka bwanji m’thumba la Benjamini?

  4. Kodi Yuda acita ciani kuti Benjamini amasulidwe?

  5. Kodi abale a Yosefe asintha bwanji makhalidwe ao?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 42:9-38.

    Kodi mau a Yosefe pa lemba la Genesis 42:18, ali cikumbutso cabwino bwanji kwa anthu amene ali paudindo m’gulu la Yehova masiku ano? (Neh. 5:15; 2 Akor. 7:1, 2)

  2. Ŵelenga Genesis 43:1-34.

    1. Ngakhale kuti Rubeni anali woyamba kubadwa, kodi n’coonekelatu bwanji kuti Yuda ndiye anakhala wolankhulilako abale ake? (Gen. 43:3, 8, 9; 44:14, 18; 1 Mbiri 5:2)

    2. Kodi Yosefe anawayesa bwanji abale ake, ndipo n’cifukwa ciani? (Gen. 43:33, 34)

  3. Ŵelenga Genesis 44:1-34.

    1. Kodi Yosefe anacita bwanji kuti abale ake asamudziŵe? (Gen. 44:5, 15; Lev. 19:26)

    2. Kodi abale a Yosefe anaonetsa bwanji kuti tsopano analibe mzimu wa nsanje umene anali nao poyamba? (Gen. 44:13, 33, 34)

Nkhani 25

Banja Lonse Lisamukila ku Iguputo

  1. Kodi n’ciani cicitika pamene Yosefe adziŵitsa abale ake amene iye ali?

  2. Kodi Yosefe mokoma mtima afotokoza ciani kwa abale ake?

  3. Kodi Farao akamba ciani pamene amvela za abale a Yosefe?

  4. Kodi banja la Yakobo linali lalikulu bwanji pamene linasamukila ku Iguputo?

  5. Kodi banja la Yakobo linayamba kuchulidwa kuti bwanji, ndipo n’cifukwa ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Genesis 45:1-28.

    Kodi nkhani ya m’Baibo ya Yosefe ionetsa bwanji kuti, Yehova akhoza kusintha zinthu zimene anthu angakonze kuti zivulaze atumiki ake, ndi kuzipangitsa kuti ziwapindulitse potsilizila pake? (Gen. 45:5-8; Yes. 8:10; Afil. 1:12-14)

  2. Ŵelenga Genesis 46:1-27.

    Kodi Yehova anapatsa Yakobo citsimikizo cabwanji pamene anali kupita ku Iguputo? (Gen.46:1-4)

Nkhani 26

Yobu Akhalabe Wokhulupilika kwa Mulungu

  1. Kodi Yobu anali ndani?

  2. Kodi Satana anayesa kucita ciani, koma kodi anakwanitsa?

  3. Kodi Yehova anavomeleza Satana kucita ciani, ndipo n’cifukwa ciani?

  4. N’cifukwa ciani mkazi wa Yobu auza mwamuna wake kuti “tukanani Mulungu mufe”? (Ona cithunzi-thunzi)

  5. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi caciŵili, kodi Yehova anamudalitsa bwanji Yobu, ndipo n’cifukwa ciani?

  6. Ngati takhala okhulupilika kwa Yehova monga Yobu, kodi tidzalandila madalitso abwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yobu 1:1-22.

    Kodi Akristu masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca Yobu? (Yobu 1:1; Afil. 2:15; 2 Pet. 3:14)

  2. Ŵelenga Yobu 2:1-13.

    Kodi Yobu ndi mkazi wake analandila cizunzo ca Satana m’njila ziŵili ziti zosiyana? (Yobu 2:9, 10; Miy. 19:3; Mika 7:7; Mal. 3:14)

  3. Ŵelenga Yobu 42:10-17.

    1. Kodi dalitso limene Yobu analandila, ndi limene Yesu analandila cifukwa ca moyo wake wokhulupilika, afanana bwanji? (Yobu 42:12; Afil. 2:9-11)

    2.       

Nkhani 27

Mfumu Yoipa Ilamulila ku Iguputo

  1. Kodi mwamuna amene ali ndi mkwapulo pacithunzi-thunzi apa ndani, ndipo amenya ndani?

  2. Pamene Yosefe anamwalila, kodi n’ciani cinacitika kwa Aisiraeli?

  3. N’cifukwa ciani Aiguputo anayamba kuopa Aisiraeli?

  4. Kodi Farao anapeleka lamulo lanji kwa anamwino, kapena kuti azimai amene anali kuthandiza akazi aciisiraeli kubeleka?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 1:6-22.

    1. Kodi Yehova anayamba bwanji kukwanilitsa lonjezo lake kwa Abulahamu? (Eks. 1:7; Gen. 12:2; Mac. 7:17)

    2. Kodi anamwino aciheberi anaonetsa bwanji kuti anali kuona moyo kukhala wopatulika? (Eks. 1:17; Gen. 9:6)

    3. Kodi anamwino amenewo anadalitsidwa bwanji cifukwa cokhala okhulupilika kwa Yehova? (Eks. 1:20, 21; Miy. 19:17)

    4. Kodi Satana anafuna kusokoneza bwanji colinga ca Yehova ponena za mbeu yolonjezedwa ya Abulahamu? (Eks. 1:22; Mat. 2:16)

Nkhani 28

Mmene Kamwana, ka Mose, Kanapulumukila

  1. Kodi kamwana kali pacithunzi-thunzi apa n’ka ndani, ndipo kagwililila cikumo ca ndani?

  2. Kodi amai a Mose anacita ciani kuti am’pulumutse?

  3. Kodi mtsikana ali pacithunzi-thunzi apa ndani, ndipo anacita ciani?

  4. Pamene mwana wa Farao anapeza kamwana aka, Miriamu anamuuza ciani?

  5. Kodi mwana wa Farao anakamba ciani kwa amai a Mose?

Funso Loonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 2:1-10.

    Kodi amai a Mose anali ndi mwai wanji wophunzitsa Mose ali mwana, ndipo zimenezi zipeleka citsanzo cabwanji kwa makolo masiku ano? (Eks. 2:9, 10; Deut. 6:6-9; Miy. 22:6; Aef. 6:4; 2 Tim. 3:15)

Nkhani 29

Cimene Mose Anathaŵila

  1. Kodi Mose anakulila kuti, ndipo anali kudziŵa ciani za makolo ake?

  2. Kodi Mose anacita ciani pamene anali ndi zaka 40?

  3. Kodi Mose anakamba ciani kwa Mwiisiraeli amene anali kucita ndeo, ndipo mwamunayu anamuyankha kuti ciani?

  4. N’cifukwa ciani Mose anathaŵa ku Iguputo?

  5. Kodi Mose anathaŵila kuti, ndipo anakumana ndi ndani kumeneko?

  6. Kodi Mose anali kucita ciani pa zaka 40 pamene anathaŵa ku Iguputo?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 2:11-25.

    Ngakhale kuti anaphunzitsidwa nzelu za Aiguputo kwa zaka zambili, kodi Mose anaonetsa bwanji kuti anali wokhulupilika kwa Yehova ndi kwa anthu ake? (Eks. 2:11, 12; Aheb. 11:24)

  2. Ŵelenga Machitidwe 7:22-29.

    Kodi tiphunzila ciani pa kuyesa-yesa kwa Mose kuti apulumutse Aisiraeli muukapolo ku Iguputo mwa mphamvu zake? (Mac. 7:23-25; 1 Pet. 5:6, 10)

Nkhani 30

Citsamba Coyaka Moto

  1. Kodi phili lili pacithunzi-thunzi apa amalicha kuti ciani?

  2. Fotokoza cinthu codabwitsa cimene Mose anaona pamene anayenda ku phili ndi nkhosa zake?

  3. Kodi mau ocokela pacitsamba anakamba kuti ciani, ndipo anali mau a ndani?

  4. Kodi Mose anayankha bwanji pamene Mulungu anamuuza kuti adzatsogolela anthu a Mulungu kucoka mu Iguputo?

  5. Kodi Mulungu anauza Mose kuti aziyankha kuti ciani anthu akamufunsa amene wamutuma?

  6. Kodi Mose anayenela kucita ciani kuonetsa kuti Mulungu ndiye amene anamutuma?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 3:1-22.

    Ngakhale ngati tingadzione kuti sitingakwanitse kucita nchito inayake m’gulu la Mulungu, kodi zimene Mose anakumana nazo zimatipatsa bwanji cidalilo cakuti Yehova adzatithandiza? (Eks. 3:11, 13; 2 Akor. 3:5, 6)

  2. Ŵelenga Ekisodo 4:1-20.

    1. Kodi Mose anasintha bwanji pazaka zonse zimene anakhala m’dziko la Midiyani, ndipo amene afuna udindo mumpingo angaphunzilepo ciani pamenepa? (Eks. 2:11, 12; 4:10, 13; Mika 6:8; 1 Tim. 3:1, 6, 10)

    2. Ngakhale kuti Yehova angatilange kupitila m’gulu lake, kodi citsanzo ca Mose cingatipatse cidalilo cabwanji? (Eks. 4:12-14; Sal. 103:14; Aheb. 12:4-11)

Nkhani 31

Mose ndi Aroni Aonana ndi Farao

  1. Kodi zozizwitsa zimene Mose ndi Aroni anacita zinawakhudza bwanji Aisiraeli?

  2. Kodi Mose ndi Aroni anauza ciani Farao, ndipo Farao anayankha kuti ciani?

  3. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi n’ciani cinacitika pamene Aroni anaponya ndodo yake pansi?

  4. Kodi Yehova anakhaulitsa bwanji Farao, ndipo Farao anacita ciani?

  5. N’ciani cinacitika pambuyo pa mlili wa namba 10?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 4:27-31 ndi 5:1-23.

    Kodi Farao anatanthauza ciani pamene anakamba kuti: ‘Ine sinimudziŵa Yehova ngakhale pang’ono’? (Eks. 5:2; 1 Sam. 2:12; Aroma 1:21)

  2. Ŵelenga Ekisodo 6:1-13, 26-30.

    1. Kodi Yehova sanadzidziŵikitse bwanji kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo? (Eks. 3:13, 14; 6:3; Gen. 12:8)

    2. Kodi timamva bwanji kuona kuti Yehova anagwilitsila nchito Mose, ngakhale kuti Mose anali kuona kuti sanali woyenelela nchito imene anapatsidwa? (Eks. 6:12, 30; Luka 21:13-15)

  3. Ŵelenga Ekisodo 7:1-13.

    1. Pamene Mose ndi Aroni molimba mtima anauza Farao ziweluzo za Yehova, kodi n’citsanzo canji cimene anaonetsa kwa atumiki a Mulungu masiku ano? (Eks. 7:2, 3, 6; Mac. 4:29-31)

    2. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti ali ndi mphamvu kupambana milungu ya Iguputo? (Eks. 7:12; 1 Mbiri 29:12)

Nkhani 32

Milili 10

  1. Mwa kugwilitsila nchito zithunzi-thunzi zimene zaonetsedwa, fotokoza milili itatu yoyambilila imene Yehova anabweletsa pa Iguputo.

  2. Kodi milili itatu yoyambilila inali kusiyana bwanji ndi milili ina yonse?

  3. Kodi milili ya namba 4, 5, ndi 6 inali ya ciani?

  4. Fotokoza milili ya namba 7, 8 ndi 9.

  5. Kodi Yehova anauza Aisiraeli kucita ciani akalibe kubweletsa mlili wa namba 10?

  6. Kodi mlili wa namba 10 unali wa ciani, ndipo n’ciani cinacitika pambuyo pake?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 7:19–8:23.

    1. Ngakhale kuti ansembe ocita zamatsenga a ku Iguputo naonso anacita milili yao iŵili yoyambilila, kodi anakakamizidwa kuvomeleza ciani pambuyo pa mlili wacitatu? (Eks. 8:18, 19; Mat. 12:24-28)

    2. Kodi mlili wacinai unaonetsa bwanji mphamvu za Yehova zakuti angachinjilize anthu ake, ndipo kudziŵa zimenezi kucititsa anthu a Mulungu kumva bwanji pamene ayang’anizana ndi “cisautso cacikulu” cimene cinanenedwelatu? (Eks. 8:22, 23; Chiv. 7:13, 14; 2 Mbiri 16:9)

  2. Ŵelenga Ekisodo 8:24; 9:3, 6, 10, 11, 14, 16, 23-25 ndi 10:13-15, 21-23.

    1. Kodi milili 10 inaonetsa kuti pali magulu aŵili ati, ndipo zimenezi zimaonetsa bwanji mmene tionela magulu amenewa masiku ano? (Eks. 8:10, 18, 19; 9:14)

    2. Kodi lemba la Ekisodo 9:16 litithandiza bwanji kumvetsetsa cifukwa cimene Yehova walolela Satana kukhalapo mpaka lelo? (Aroma 9:21, 22)

  3. Ŵelenga Ekisodo 12:21-32.

    Kodi Paska inathandiza bwanji kuti anthu ambili apulumuke, ndipo Paska imeneyi inaimila ciani? (Eks. 12:21-23; Yoh. 1:29; Aroma 5:18, 19, 21; 1 Akor. 5:7)

Nkhani 33

Kuoloka Nyanja Yofiila

  1. Kodi ni amuna aciisiraeli angati amene anacoka mu Iguputo pamodzi ndi akazi ndi ana, ndipo ndani anawatsatila?

  2. Kodi Farao anamvela bwanji pamene analola Aisiraeli kuti apite, ndipo anacita ciani?

  3. Kodi Yehova anacita ciani kuti alepheletse Aiguputo kuukila anthu ake?

  4. N’ciani cinacitika pamene Mose anatambasulila ndodo yake pa Nyanja Yofiila, ndipo Aisiraeli anacita ciani?

  5. N’ciani cinacitika pamene Aiguputo anathamangila pa Nyanja kutsatila Aisiraeli?

  6. Kodi Aisiraeli anaonetsa bwanji kuti anakondwela ndi kuyamikila Yehova cifukwa cowapulumutsa?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 12:33-36.

    Kodi Yehova anacita ciani kuti anthu ake adalitsike cifukwa ca zaka zonse zimene anakhala muukapolo ku Iguputo? (Eks. 3:21, 22; 12:35, 36)

  2. Ŵelenga Ekisodo 14:1-31.

    Kodi mau a Mose opezeka pa Ekisodo 14:13, 14, amakhudza bwanji atumiki a Yehova masiku ano pamene ayang’anizana ndi nkhondo ya Aramagedo imene ibwela? (2 Mbiri 20:17; Sal. 91:8)

  3. Ŵelenga Ekisodo 15:1-8, 20, 21.

    1. N’cifukwa ciani atumiki a Yehova ayenela kumuimbila nyimbo zacitamando? (Eks. 15:1, 2; Sal. 105:2, 3; Chiv. 15:3, 4)

    2. Kodi Miriamu ndi akazi ena pa Nyanja Yofiila anapeleka citsanzo canji kwa akazi acikristu pankhani yotamanda Yehova masiku ano? (Eks. 15:20, 21; Sal. 68:11)

Nkhani 34

Cakudya Catsopano

  1. Kodi pacithunzi-thunzi apa anthu ayola ciani?

  2. Kodi Mose apatsa anthu malangizo akuti bwanji poyola mana?

  3. Kodi Yehova auza anthu kucita ciani patsiku la 6, nanga n’cifukwa ciani?

  4. Kodi Yehova acita cozizwitsa cabwanji anthu akasunga mana mpaka patsiku la 7?

  5. Kodi Yehova adyetsa anthu mana kwa zaka zingati?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 16:1-36 ndi Numeri 11:7-9.

    1. Kodi lemba la Ekisodo 16:8 litiuza ciani pankhani yolemekeza anthu amene Mulungu wapatsa udindo mumpingo wacikristu? (Aheb. 13:17)

    2. Pamene anali m’cipululu, kodi Aisiraeli anakumbutsidwa bwanji tsiku ndi tsiku kuti afunika kudalila Yehova? (Eks. 16:14-16, 35; Deut. 8:2, 3)

    3. Kodi Yesu anafotokoza kuti mana anaimila ciani, ndipo timapindula bwanji ndi “cakudya cocokela kumwamba” cimeneci? (Yoh. 6:31-35, 40)

  2. Ŵelenga Yoswa 5:10-12.

    Kodi Aisiraeli anadya mana zaka zingati, ndipo izi zinawaika bwanji paciyeso? Nanga ife tiphunzilapo ciani pankhani imeneyi? (Eks. 16:35; Num. 11:4-6; 1 Akor. 10:10, 11)

Nkhani 35

Yehova Apeleka Malamulo Ake

  1. Patapita pafupi-fupi miyezi iŵili kucokela pamene Aisiraeli anacoka ku Iguputo, kodi amanga kuti msasa?

  2. Kodi Yehova akamba kuti afuna kuti anthu acite ciani, ndipo io akuti bwanji?

  3. Kodi miyala iŵili yafulati imene Yehova anapatsa Mose inali yaciani?

  4. Kodi Yehova anapatsa Aisiraeli malamulo ena ati kuonjezela pa Malamulo Khumi?

  5. Kodi ni malamulo aŵili ati amene Yesu anakamba kuti ndiye akulu kwambili?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 19:1-25; 20:1-21; 24:12-18 ndi 31:18.

    Kodi mau apa Ekisodo 19:8 amatithandiza bwanji kumvetsetsa zimene zimafunika pa kudzipeleka kwacikristu? (Mat. 16:24; 1 Pet. 4:1-3)

  2. Ŵelenga Deuteronomo 6:4-6; Levitiko 19:18 ndi Mateyu 22:36-40.

    Kodi Akristu amaonetsa bwanji cikondi cao kwa Mulungu ndi kwa anzao? (Maliko 6:34; Mac. 4:20; Aroma 15:2)

Nkhani 36

Mwana wa Ng’ombe Wagolide

  1. Kodi anthu pacithunzi-thunzi apa acita ciani? Nanga acitilanji zimenezi?

  2. N’cifukwa ciani Yehova wakalipa, ndipo kodi Mose acita ciani poona zimene anthu acita?

  3. Kodi Mose auza amuna ena kucita ciani?

  4. Kodi tiphunzilapo ciani pankhani imeneyi?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 32:1-35.

    1. Kodi nkhani imeneyi ionetsa bwanji maganizo a Yehova pankhani yophatikiza cipembedzo coona ndi conama? (Eks. 32:4-6, 10; 1 Akor. 10:7, 11)

    2. Kodi Akristu ayenela kusamala bwanji pankhani yosankha zosangulutsa, monga nyimbo ndi kuvina? (Eks. 32:18, 19; Aef. 5:15, 16; 1 Yoh. 2:15-17)

    3. Kodi fuko la Alevi linapeleka bwanji citsanzo cabwino pankhani yotsatila cilungamo? (Eks. 32:25-28; Sal. 18:25)

Nkhani 37

Tenti Yolambililako

  1. Kodi nyumba imene ili pacithunzi-thunzi apa ni ciani, ndipo ni ya ciani?

  2. N’cifukwa ciani Yehova anauza Mose kuti apange tenti yosavuta kumasula?

  3. Kodi bokosi limene lili m’cipinda cacing’ono kumapeto kwa tenti ni ciani, ndipo mkati mwake muli ciani?

  4. Kodi Yehova wasankha ndani kukhala mkulu wa ansembe, ndipo kodi mkulu wa ansembe amacita ciani?

  5. Ndiuze zinthu zitatu zimene zili m’cipinda cacikulu ca tenti imeneyi.

  6. Kodi mu yadi ya cihema muli zinthu ziŵili ziti, ndipo n’za ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ekisodo 25:8-40; 26:1-37; 27:1-8 ndi 28:1.

    Kodi akelubi pamwamba pa “likasa la umboni” anaimila ciani? (Eks. 25:20, 22; Num. 7:89; 2 Maf. 19:15)

  2. Ŵelenga Ekisodo 30:1-10, 17-21; 34:1, 2 ndi Aheberi 9:1-5.

    1. N’cifukwa ciani Yehova anagogomeza kuti ansembe amene anali kutumikila pacihema afunika kukhala oyela mwakuthupi? Nanga zimenezi ziyenela kutikhudza bwanji lelo? (Eks. 30:18-21; 40:30, 31; Aheb. 10:22)

    2. Kodi mtumwi Paulo aonetsa bwanji kuti cihema ndi pangano la Cilamulo sizinali kugwila nchito panthawi imene analemba kalata yake yopita kwa Akristu acihebeli? (Aheb. 9:1, 9; 10:1)

Nkhani 38

Azondi 12

  1. Kodi zipatso za mpesa zioneka bwanji pacithunzi-thunzi ici, ndipo zinacokela kuti?

  2. N’cifukwa ciani Mose atuma azondi 12 kudziko la Kanani?

  3. Kodi azondi 10 akamba ciani pamene afika kwa Mose?

  4. Kodi azondi aŵili aonetsa bwanji kuti akhulupilila Yehova, ndipo maina ao ndani?

  5. N’cifukwa ciani Yehova wakalipa, ndipo auza Mose ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Numeri 13:1-33.

    1. Ndani anasankhidwa kuti akazonde dziko, ndipo anali ndi mwai waukulu uti? (Num. 13:2, 3, 18-20)

    2. N’cifukwa ciani maganizo a Yoswa ndi Kalebe anasiyana ndi maganizo a azondi ena aja, ndipo tiphunzilapo ciani? (Num. 13:28-30; Mat. 17:20; 2 Akor. 5:7)

  2. Ŵelenga Numeri 14:1-38.

    1. Kodi n’cenjezo liti limene tiyenela kumvela pankhani yodandaula za anthu amene amaimila Yehova padziko lapansi? (Num. 14:2, 3, 27; Mat. 25:40, 45; 1 Akor. 10:10)

    2. Kodi lemba la Numeri 14:24 lionetsa bwanji kuti Yehova amaona zimene mtumiki wake aliyense amacita? (1 Maf. 19:18; Miy. 15:3)

Nkhani 39

Ndodo ya Aroni Imela Maluŵa

  1. Kodi ndani amene wapandukila ulamulilo wa Mose ndi Aroni, ndipo Mose amuuza ciani?

  2. Kodi Mose auza Kora ndi otsatila ake okwana 250 kuti acite ciani?

  3. Kodi Mose auza ciani anthu, nanga cimene cicitika n’ciani pamene iye atsiliza cabe kukamba?

  4. Nanga n’ciani cimene cicitikila Kora ndi otsatila ake okwana 250?

  5. Kodi Eleazara mwana wa Aroni, acita ciani ndi mapani ofukizila a anthu amene afa, ndipo n’cifukwa ciani?

  6. N’cifukwa ciani Yehova wacititsa kuti ndodo ya Aroni imele maluŵa? (Ona cithunzi-thunzi.)

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Numeri 16:1-49.

    1. Kodi Kora ndi otsatila ake anacita ciani, nanga n’cifukwa ciani anapandukila Yehova ndi zimene anacita? (Num. 16:9, 10, 18; Lev. 10:1, 2; Miy. 11:2)

    2. Kodi Kora ndi “atsogoleli a anthu” okwana 250 anakhala ndi maganizo olakwika ati? (Num. 16:1-3; Miy. 15:33; Yes. 49:7)

  2. Ŵelenga Numeri 17:1-11 ndi 26:10.

    1. Kodi kumela maluŵa kwa ndodo ya Aroni kunaonetsa ciani, nanga n’cifukwa ciani Yehova analamula kuti isungidwe mu likasa? (Num. 17:5, 8, 10)

    2. Kodi ni phunzilo lofunika liti limene titengapo pa cozizwitsa ca ndodo ya Aroni? (Num. 17:10; Mac. 20:28; Afil. 2:14; Aheb. 13:17)

Nkhani 40

Mose Amenya Cimwala ndi Ndodo

  1. Kodi Yehova awasamalila bwanji Aisiraeli m’cipululu?

  2. Kodi Aisiraeli adandaula ciani pamene afika ku Kadesi?

  3. Kodi Yehova acita ciani kuti apeleke madzi kwa anthu ndi ziweto zao?

  4. Kodi pacithunzi-thunzi apa, ndani amene akudzisotha yekha, nanga acita zimenezi cifukwa ciani?

  5. N’cifukwa ciani Yehova wakalipa ndi Mose ndi Aroni, nanga awapatsa cilango canji?

  6. Kodi cicitika n’ciani paphili la Hora, nanga ndani amene akhala mkulu wa ansembe?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Numeri 20:1-13, 22-29 ndi Deuteronomo 29:5.

    1. Kodi tiphunzilapo ciani panjila imene Yehova anasamalila Aisiraeli m’cipululu? (Deut. 29:5; Mat. 6:31; Aheb. 13:5; Yak. 1:17)

    2. Pamene Mose ndi Aroni analephela kulemekeza Yehova pamaso pa Aisiraeli, kodi Mulungu aitenga bwanji nkhaniyo? (Num. 20:12; 1 Akor. 10:12; Chiv. 4:11)

    3. Kodi tiphunzilapo ciani pazimene Mose anacita ndi cilango cimene Yehova anamupatsa? (Num. 12:3; 20:12, 27, 28; Deut. 32:4; Aheb. 12:7-11)

Nkhani 41

Njoka Yamkuwa

  1. Kodi pacithunzi-thunzi apa, n’ciani cimene capomba kumtengo? Nanga n’cifukwa ciani Yehova wauza Mose kuti aiike pamenepo?

  2. Kodi anthu aonetsa bwanji kuti sayamikila zonse zimene Mulungu waacitila?

  3. Kodi anthu amuuza ciani Mose pamene Yehova watuma njoka zapoizoni kuti ziwalume?

  4. N’cifukwa ciani Yehova wauza Mose kuti apange njoka yamkuwa?

  5. Kodi pankhani iyi tiphunzilapo ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Numeri 21:4-9.

    1. Kodi tipezapo cenjezo liti pa madandaulo a Aisiraeli pa zinthu zimene Yehova anawapatsa? (Num. 21:5, 6; Aroma 2:4)

    2. Kodi mtsogolo Aisiraeli anagwilitsila nchito bwanji njoka yamkuwa, nanga Mfumu Hezekiya inacita ciani? (Num. 21:9; 2 Maf. 18:1-4)

  2. Ŵelenga Yohane 3:14, 15.

    Kodi kuika njoka yamkuwa pamtengo kunacitila bwanji cithunzi kupacikidwa kwa Yesu Kristu? (Agal. 3:13; 1 Pet. 2:24)

Nkhani 42

Bulu Akamba

  1. Kodi Balaki ndani, nanga n’cifukwa ciani aitana Balamu?

  2. N’cifukwa ciani bulu wa Balamu wakhala panjila?

  3. Kodi Balamu wamva bulu akamba kuti ciani?

  4. Kodi mngelo amuuza ciani Balamu?

  5. Kodi n’ciani cicitika pamene Balamu afuna kutembelela Aisiraeli?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Numeri 21:21-35.

    N’cifukwa ciani Aisiraeli anamenya nkhondo, ndi Mfumu Sihoni ya Aamori ndi Mfumu Ogi ya Basana, ndi kuwagonjetsa? (Num. 21:21, 23, 33, 34)

  2. Ŵelenga Numeri 22:1-40.

    Kodi Balamu anali kufuna ciani pamene anayesa kutembelela Isiraeli, nanga tiphunzilapo ciani? (Num. 22:16, 17; Miy. 6:16, 18; 2 Pet. 2:15; Yuda 11)

  3. Ŵelenga Numeri 23:1-30.

    Ngakhale kuti Balamu anali kukamba ngati mlambili wa Yehova, kodi zocita zake zinaonetsa bwanji kuti sanali mlambili wa Yehova? (Num. 23:3, 11-14; 1 Sam. 15:22)

  4. Ŵelenga Numeri 24:1-25.

    Kodi nkhani iyi ya m’Baibo ingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu cakuti Yehova sadzalephela kucita cifunilo cake? (Num. 24:10; Yes. 54:17)

Nkhani 43

Yoswa Akhala Mtsogoleli

  1. Kodi pacithunzi-thunzi apa, anthu aŵili amene aimilila ndi Mose ndani?

  2. Kodi Yehova amuuza ciani Yoswa?

  3. N’cifukwa ciani Mose akwela pamwamba pa phili la Nebo, ndipo Yehova amuuza ciani?

  4. Kodi Mose akufa ali ndi zaka zingati?

  5. N’cifukwa ciani anthu ali ndi cisoni? Ngakhale zili conco, n’cifukwa ciani ali okondwela?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Numeri 27:12-23.

    Kodi Yoswa analandila udindo wapadela uti kwa Yehova, ndipo umboni wakuti Yehova amasamalila anthu Ake umaoneka bwanji masiku ano? (Num. 27:15-19; Mac. 20:28; Aheb. 13:7)

  2. Ŵelenga Deuteronomo 3:23-29.

    Kodi n’cifukwa ciani Yehova sanalole Mose ndi Aroni kuloŵa m’dziko lolonjezedwa, nanga tiphunzilapo ciani pamenepa? (Deut. 3:25-27; Num. 20:12, 13)

  3. Ŵelenga Deuteronomo 31:1-8, 14-23.

    Kodi mau a Mose olailana ndi Aisiraeli aonetsa bwanji kuti analandila modzicepetsa cilango ca Yehova? (Deut. 31:6-8, 23)

  4. Ŵelenga Deuteronomo 32:45-52.

    Kodi Mau a Mulungu ayenela kukhudza bwanji umoyo wathu? (Deut. 32:47; Lev. 18:5; Aheb. 4:12)

  5. Ŵelenga Deuteronomo 34:1-12.

    Ngakhale kuti Mose sanaone Yehova maso ndi maso, kodi lemba la Deuteronomo 34:10 limaonetsa ciani pankhani ya unansi wake ndi Yehova? (Eks. 33:11, 20; Num. 12:8)

Nkhani 44

Rahabi Abisa Azondi

  1. Kodi Rahabi akhala kuti?

  2. Kodi amuna aŵili awa pacithunzi-thunzi ndani, nanga n’cifukwa ciani ali ku Yeriko?

  3. Kodi mfumu ya ku Yeriko ilamula Rahabi kucita ciani, nanga Rahabi ayankha kuti ciani?

  4. Kodi Rahabi awathandiza bwanji amuna aŵili amenewa, ndipo awapempha ciani?

  5. Kodi azondi aŵili amulonjeza ciani Rahabi?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yoswa 2:1-24.

    Kodi lonjezo la Yehova la pa Ekisodo 23:28 linakwanilitsika bwanji pamene Aisiraeli anaukila Yeriko? (Yos. 2:9-11)

  2. Ŵelenga Aheberi 11:31.

    Kodi citsanzo ca Rahabi cionetsa bwanji kuti cikhulupililo n’cofunika? (Aroma 1:17; Aheb. 10:39; Yak. 2:25)

Nkhani 45

Aoloka Mtsinje wa Yorodano

  1. Kodi Yehova acita codabwitsa cabwanji kuti Aisiraeli aoloke mtsinje wa Yorodano?

  2. N’cifukwa ciani Aisiraeli afunika cikhulupililo colimba kuti aoloke mtsinje wa Yorodano?

  3. N’cifukwa ciani Yehova auza Yoswa kutenga miyala 12 ikulu-ikulu pansi pa mtsinje?

  4. Kodi cicitika n’ciani pamene ansembe angotuluka mu mtsinje wa Yorodano?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yoswa 3:1-17.

    1. Malinga ndi nkhani imeneyi, kodi tiyenela kucita ciani kuti Yehova atithandize ndi kutidalitsa? (Yos. 3:13, 15; Miy. 3:5; Yak. 2:22, 26)

    2. Kodi mtsinje wa Yorodano unali bwanji pamene Aisiraeli anali kuoloka ndi kuloŵa mu Dziko Lolonjezedwa? Ndipo kodi zimenezi zinakweza bwanji dzina la Yehova? (Yos. 3:15; 4:18; Sal. 66:5-7)

  2. Ŵelenga Yoswa 4:1-18.

    Kodi miyala 12 imene anaitenga mu Yorodano ndi kukaiika ku Giligala, nchito yake inali ciani? (Yos. 4:4-7)

Nkhani 46

Mpanda wa Yeriko

  1. Kodi Yehova auza asilikali ndi ansembe kucita ciani kwa masiku 6?

  2. Kodi patsiku la 7 amuna amenewa ayenela kucita ciani?

  3. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa, n’ciani cicitikila cipupa ca Yeriko?

  4. Kodi n’cifukwa ciani nthambo yofiila iyi ili pawindo?

  5. Kodi Yoswa auza asilikali kuti acite ciani kwa anthu ndi mzinda? Nanga ayenela kucita ciani ndi siliva, golide, mkuwa, ndi citsulo?

  6. Kodi azondi aŵili auzidwa kucita ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yoswa 6:1-25.

    1. Kodi kuzungulila mzinda wa Yeriko kumene Aisiraeli anacita patsiku la 7 kufanana bwanji ndi nchito yolalikila ya Mboni za Yehova m’masiku ano otsiliza? (Yos. 6:15, 16; Yes. 60:22; Mat. 24:14; 1 Akor. 9:16)

    2. Kodi ulosi wolembedwa pa Yoswa 6:26 unakwanilitsika bwanji zaka 500 pambuyo pake, ndipo tiphunzilapo ciani za mau a Yehova? (1 Maf. 16:34; Yes. 55:11)

Nkhani 47

Kawalala mu Isiraeli

  1. Kodi pacithunzi-thunzi apa, mwamuna amene afocela cuma ca ku Yeriko ndani, nanga amene amuthandiza ndani?

  2. N’cifukwa ciani zimene Akani ndi banja lake acita ni chimo lalikulu?

  3. Kodi Yehova ayankha kuti ciani pamene Yoswa afunsa cimene Aisiraeli alemphelela nkhondo ku Ai?

  4. Kodi n’ciani cimene cicitika kwa Akani ndi banja lake pamene awabweletsa kwa Yoswa?

  5. Kodi ciweluzo ca Akani citipatsa phunzilo lofunika lakuti bwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yoswa 7:1-26.

    1. Kodi mapemphelo a Yoswa amatiuza ciani za unansi wake ndi Mlengi? (Yos. 7:7-9; Sal. 119:145; 1 Yoh. 5:14)

    2. Kodi citsanzo ca Akani citionetsa ciani, nanga n’cifukwa ciani limeneli lili cenjezo kwa ife? (Yos. 7:11, 14, 15; Miy. 15:3; 1 Tim. 5:24; Aheb. 4:13)

  2. Ŵelenga Yoswa 8:1-29.

    Kodi ife aliyense payekha, tili ndi udindo wanji mumpingo wacikristu masiku ano? (Yos. 7:13; Lev. 5:1; Miy. 28:13)

Nkhani 48

Agibeoni Anzelu

  1. Kodi anthu a ku Gibeoni asiyana bwanji ndi Akanani amene ali m’mizinda yapafupi?

  2. Ukaona pacithunzi-thunzi apa, kodi Agibeoni acita ciani? Nanga acitilanji zimenezo?

  3. Kodi Yoswa ndi atsogoleli a Aisiraeli alonjeza Agibeoni ciani? Koma io adziŵa ciani patangopita masiku atatu?

  4. Kodi mafumu a mizinda ina acita ciani pamene amvela kuti Agibeoni apangana za mtendele ndi Aisiraeli?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yoswa 9:1-27.

    1. Popeza Yehova analamula mtundu wa Aisiraeli kuti ‘uphe anthu onse okhala’ m’dzikolo, kodi iye anaonetsa makhalidwe ati polekelela Agibeoni? (Yos. 9:22, 24; Mat. 9:13; Mac. 10:34, 35; 2 Pet. 3:9)

    2. Mwa kusunga cipangano cimene anacita ndi Agibeoni, kodi Yoswa anapeleka bwanji citsanzo cabwino kwa Akristu masiku ano? (Yos. 9:18, 19; Mat. 5:37; Aef. 4:25)

  2. Ŵelenga Yoswa 10:1-5.

    Kodi masiku ano khamu lalikulu limatsatila bwanji citsanzo ca Agibeoni, ndipo limakhala mdani wa ndani? (Yos. 10:4; Zek. 8:23; Mat. 25:35-40; Chiv. 12:17)

Nkhani 49

Dzuŵa Liimilila

  1. Pacithunzi-thunzi apa, kodi Yoswa akamba ciani, ndipo n’cifukwa ciani?

  2. Kodi Yehova athandiza bwanji Yoswa ndi asilikali ake?

  3. Kodi Yoswa agonjetsa mafumu angati a adani, ndipo zimenezi zitenga nthawi yaitali bwanji?

  4. N’cifukwa ciani Yoswa agaŵa dziko la Kanani?

  5. Kodi Yoswa akufa ali ndi zaka zingati, nanga pambuyo pake n’ciani cicitika kwa anthu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yoswa 10:6-15.

    Popeza kuti tadziŵa kuti Yehova anacititsa dzuŵa ndi mwezi kuimilila kuti athandize Aisiraeli, kodi tili ndi cidalilo cabwanji masiku ano? (Yos. 10:8, 10, 12, 13; Sal. 18:3; Miy. 18:10)

  2. Ŵelenga Yoswa12:7-24.

    Kodi m’ceni-ceni ndani amene anagonjetsa mafumu 31 a ku Kanani? Ndipo n’cifukwa ciani kudziŵa zimenezi kuli kofunika kwa ife masiku ano? (Yos. 12:7; 24:11-13; Deut. 31:8; Luka 21:9, 25-28)

  3. Ŵelenga Yoswa 14:1-5.

    Kodi dziko analigaŵa bwanji pakati pa mafuko a Isiraeli, ndipo zimenezi zionetsa ciani ponena za coloŵa ca mu Paladaiso? (Yos. 14:2; Yes. 65:21; Ezek. 47:21-23; 1 Akor. 14:33)

  4. Ŵelenga Oweruza 2:8-13.

    Mofanana ndi Yoswa mu Isiraeli, kodi ndani masiku ano amene ali ngati woletsa mpatuko? (Ower. 2:8, 10, 11; Mat. 24:45-47; 2 Ates. 2:3-6; Tito 1:7-9; Chiv. 1:1; 2:1, 2)

Nkhani 50

Akazi Aŵili Olimba Mtima

  1. Kodi oweluza ndiye ndani, nanga ena maina ao anali ndani?

  2. Kodi Debora ali ndi udindo wapadela uti, ndipo udindo umenewu umaphatikizapo ciani?

  3. Pamene Mfumu Yabini ndi Sisera mkulu wa nkhondo afuna kumenyana ndi Aisiraeli, kodi ni uthenga uti wocokela kwa Yehova umene Debora auza woweluza Baraki? Ndipo akamba kuti ndani adzalandila ulemelelo?

  4. Kodi Yaeli aonetsa bwanji kuti ni mkazi wolimba mtima?

  5. Kodi cinacitika n’ciani pamene Mfumu Yabini anafa?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Oweruza 2:14-22.

    Kodi Aisiraeli anadzibweletsela bwanji mkwiyo wa Yehova, nanga tiphunzilapo ciani pamenepa? (Ower. 2:20; Miy. 3:1, 2; Ezek. 18:21-23)

  2. Ŵelenga Oweruza 4:1-24.

    Kodi akazi acikristu masiku ano angaphunzilepo ciani pa citsanzo ca Debora ndi Yaeli pankhani ya cikhulupililo ndi kulimba mtima? (Ower. 4:4, 8, 9, 14, 21, 22; Miy. 31:30; 1 Akor. 16:13)

  3. Ŵelenga Oweruza 5:1-31.

    Kodi n’cifukwa ciani nyimbo yacipambano ya Baraki ndi Debora ingatengedwenso ngati pemphelo lonena za nkhondo ya Aramagedo? (Ower. 5:3, 31; 1 Mbiri 16:8-10; Chiv. 7:9, 10; 16:16; 19:19-21)

Nkhani 51

Rute ndi Naomi

  1. Kodi Naomi apezeka bwanji ku dziko la Moabu?

  2. Kodi Rute ndi Olipa anali ndani?

  3. Kodi Rute ndi Olipa ayankha bwanji pamene Naomi awauza kuti abwelele kwa anthu akwao?

  4. Kodi Boazi ndani, ndipo athandiza bwanji Rute ndi Naomi?

  5. Kodi dzina la mwana amene Boazi ndi Rute akhala naye ndani, ndipo n’cifukwa ciani tiyenela kumukumbukila?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Rute 1:1-17.

    1. Kodi Rute akamba mau abwino ati oonetsa cikondi cosatha? (Rute 1:16, 17)

    2. Kodi maganizo a Rute aonetsa bwanji mtima umene a “nkhosa zina” ali nao kwa otsalila odzozedwa masiku ano? (Yoh. 10:16; Zek. 8:23)

  2. Ŵelenga Rute 2:1-23.

    Kodi Rute apeleka citsanzo cabwino cabwanji kwa akazi acitsikana masiku ano? (Rute 2:17, 18; Miy. 23:22; 31:15)

  3. Ŵelenga Rute 3:5-13.

    1. Kodi Boazi anamuona bwanji Rute pamene anafunitsitsa kukwatiwa ndi iye, m’malo mokwatiwa kwa mwamuna wacinyamata?

    2. Kodi zocita za Rute zitiphunzitsa ciani pankhani ya cikondi cosatha? (Rute 3:10; 1 Akor. 13:4, 5)

  4. Ŵelenga Rute 4:7-17.

    Kodi amuna acikristu masiku ano angakhale bwanji monga Boazi? (Rute 4:9, 10; 1 Tim. 3:1, 12, 13; 5:8)

Nkhani 52

Gidiyoni ndi Asilikali ake 300

  1. N’cifukwa ciani Aisiraeli ali m’mavuto ambili, ndipo apezeka bwanji m’mavuto amenewo?

  2. N’cifukwa ciani Yehova auza Gidiyoni kuti asilikali ake aculuka kwambili?

  3. Kodi ndi asilikali angati amene atsala pamene Gidiyoni wauza asilikali amantha kuti abwelele?

  4. Malinga ndi cithunzi-thunzi, fotokoza mmene Yehova acepetsela ciŵelengelo ca asilikali a Gidiyoni kukhala 300 cabe?

  5. Kodi Gidiyoni akonzekeletsa bwanji asilikali 300 amene ali nao, ndipo Isiraeli awina bwanji nkhondo?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Oweruza 6:36-40.

    1. Kodi Gidiyoni anatsimikizila bwanji kuti cifunilo ca Yehova cicitike?

    2. Kodi masiku ano timadziŵa bwanji kuti cifunilo ca Yehova n’citi? (Miy. 2:3-6; Mat. 7:7-11; 2 Tim. 3:16, 17)

  2. Ŵelenga Oweruza 7:1-25

    1. Kodi tingaphunzile ciani kwa asilikali 300 amene anakhala chelu kusiyana ndi amene anali osasamala (Ower. 7:3, 6; Aroma 13:11, 12; Aef. 5:15-17)

    2. Mofanana ndi asilikali 300 amene anaphunzila mwa kuyang’ana Gidiyoni, nanga ife timaphunzila bwanji mwa kuyang’ana Gidiyoni wamkulu, Yesu Kristu? (Ower. 7:17; Mat. 11:29, 30; 28:19, 20; 1 Pet. 2:21)

    3. Kodi lemba la Oweruza 7:21 litithandiza bwanji kukhala wokondwela kugwila nchito iliyonse imene tapatsidwa m’gulu la Yehova? (1 Akor. 4:2; 12:14-18; Yak. 4:10)

  3. Ŵelenga Oweruza 8:1-3.

    Pothetsa mikangano ndi abale kapena alongo, kodi tiphunzila ciani kuona mmene Gidiyoni anathetsela mkangano ndi Aefraimu? (Miy. 15:1; Mat. 5:23, 24; Luka 9:48)

Nkhani 53

Lonjezo la Yefita

  1. Kodi Yefita ndani, ndipo anakhalako panthawi iti?

  2. Kodi Yefita analonjeza ciani kwa Yehova?

  3. N’cifukwa ciani Yefita acita cisoni pamene abwelela kunyumba kucokela kunkhondo imene anapambana Aamoni?

  4. Kodi mwana wamkazi wa Yefita akamba ciani pamene amvela za lonjezo limene atate wake anapanga?

  5. N’cifukwa ciani anthu amukonda mwana wamkazi wa Yefita?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Oweruza 10:6-18.

    Kodi ni cenjezo liti limene tiyenela kulabadila pankhani ya Isiraeli yokhudza kusakhulupilila Yehova? (Ower. 10:6, 15, 16; Aroma 15:4; Chiv. 2:10)

  2. Ŵelenga Oweruza 11:1-11, 29-40.

    1. Kodi tidziŵa bwanji kuti pamene Yefita anapeleka mwana wake monga “nsembe yopseleza” sizinatanthauze kuti anatentha mwana wake m’moto kum’peleka nsembe? (Ower. 11:31; Lev. 16:24; Deut. 18:10, 12)

    2. Kodi Yefita anapeleka bwanji mwana wake monga nsembe?

    3. Kodi tingaphunzile ciani kuona mmene Yefita anacitila pa zimene analonjeza Yehova? (Ower. 11:35, 39; Mlal. 5:4, 5; Mat. 16:24)

    4. Kodi mwana wa Yefita n’citsanzo cabwino bwanji kwa Akristu acicepele pankhani ya utumiki wa nthawi zonse? (Ower. 11:36; Mat. 6:33; Afil. 3:8)

Nkhani 54

Munthu Wamphamvu Kupambana Onse

  1. Kodi dzina la munthu wamphamvu kupambana onse anali ndani, ndipo ndani anam’patsa mphamvu zimenezo?

  2. Panthawi ina, kodi Samsoni anacicita ciani cimkango cacikulu, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa?

  3. Kodi Samsoni auza Delila cisinsi canji pacithunzi-thunzi apa, ndipo zimenezi zinacititsa bwanji kuti Afilisti amugwile?

  4. Patsiku limene Samsoni anafa, kodi anaphanso bwanji Afilisti 3,000 amene anali adani ake?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Oweruza 13:1-14.

    Kodi Manowa ndi mkazi wake aonetsa bwanji citsanzo cabwino kwa makolo pankhani yolela ana ao? (Ower. 13:8; Sal. 127:3; Aef. 6:4)

  2. Ŵelenga Oweruza 14:5-9 ndi 15:9-16.

    1. Kodi nkhani za Samsoni zokhudza kupha mkango, kudula nthambo zatsopano zimene anam’mangila, ndi kugwilitsila nchito fupa la nsagwada la bulu wamphongo kupha nalo amuna 1,000, zionetsa bwanji kuti mzimu woyela wa Yehova unali kugwila nchito pa iye?

    2. Kodi mzimu woyela umatithandiza bwanji masiku ano? (Ower. 14:6; 15:14; Zek. 4:6; Mac. 4:31)

  3. Ŵelenga Oweruza 16:18-31.

    Kodi kuceza ndi anthu a makhalidwe oipa kunam’bweletsela bwanji mavuto Samsoni, ndipo zimenezi zitiphunzitsa ciani? (Ower. 16:18, 19; 1 Akor. 15:33)

Nkhani 55

Kamnyamata Kotumikila Mulungu

  1. Kodi kamnyamata kali pacithunzi-thunzi n’kandani?

  2. Kodi Hana apemphela kuti ciani tsiku lina pamene ayenda ku cihema ca Yehova, ndipo Yehova amuyankha bwanji?

  3. Kodi Samueli ali ndi zaka zingati pamene amupeleka kuti akatumikile pa cihema ca Yehova, ndipo amai ake am’citila ciani caka ciliconse?

  4. Kodi ana a Eli maina ao ndani, ndipo anali ndi makhalidwe abwanji?

  5. Kodi Yehova aitana bwanji Samueli, ndipo am’patsa uthenga wakuti ciani?

  6. Kodi Samueli akhala ndani pamene akula, ndipo n’ciani cicitika pamene wakalamba?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Samueli 1:1-28.

    1. Kodi Elikana anaonetsa citsanzo canji cabwino cimene mitu ya mabanja iyenela kutsatila potsogolela pakulambila koona? (1 Sam. 1:3, 21; Mat. 6:33; Afil. 1:10)

    2. Kodi tingaphunzile ciani poona mmene Hana anacitila polimbana ndi mavuto aakulu? (1 Sam. 1:10, 11; Sal. 55:22; Aroma 12:12)

  2. Ŵelenga 1 Samueli 2:11-36.

    Kodi Eli anaonetsa bwanji kulemekeza ana ake kuposa Yehova, ndipo zimenezi ndi cenjezo lanji kwa ife? (1 Sam. 2:22-24, 27, 29; Deut. 21:18-21; Mat. 10:36, 37)

  3. Ŵelenga 1 Samueli 4:16-18.

    Kodi ni mauthenga anai ati acisoni amene acokela kunkhondo, ndipo anam’khudza bwanji Eli?

  4. Ŵelenga 1 Samueli 8:4-9.

    Kodi Isiraeli analakwila kwambili Yehova bwanji, ndipo tingacilikize bwanji Ufumu wake mokhulupilika masiku ano?

Nkhani 56

Sauli—Mfumu Yoyamba ya Isiraeli

  1. Pacithunzi-thunzi apa, kodi Samueli acita ciani, ndipo n’cifukwa ciani?

  2. N’cifukwa ciani Yehova akonda Sauli, ndipo mwamunayu ni munthu wabwanji?

  3. Kodi mwana wa Sauli ndani, ndipo n’ciani cimene mwanayu acita?

  4. N’cifukwa ciani Sauli apeleka nsembe m’malo mwakuti ayembekezele Samueli?

  5. Kodi titengapo phunzilo lanji pankhani ya Sauli?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Samueli 9:15-21 ndi 10:17-27.

    Kodi khalidwe lodzicepetsa la Sauli linamuthandiza bwanji kusakwiya pamene amuna ena anakamba za iye mopanda ulemu? (1 Sam. 9:21; 10:21, 22, 27; Miy. 17:27)

  2. Ŵelenga 1 Samueli 13:5-14.

    Kodi Sauli anacita colakwa canji ku Giligala? (1 Sam. 10:8; 13:8, 9, 13)

  3. Ŵelenga 1 Samueli 15:1-35.

    1. Kodi Sauli anacita colakwa canji cacikulu kwa Agagi, mfumu ya Aamaleki? (1 Sam. 15:2, 3, 8, 9, 22)

    2. Kodi Sauli ayesa kupanga zodzikhululukila zabwanji pa zimene anacita, ndipo afuna bwanji kuimba ena mlandu? (1 Sam. 15:24)

    3. Kodi ni cenjezo lanji limene tifunikila kumvela masiku ano pamene tipatsidwa uphungu? (1 Sam. 15:19-21; Sal. 141:5; Miy. 9:8, 9; 11:2)

Nkhani 57

Mulungu Asankha Davide

  1. Kodi mnyamata ali pacithunzi-thunzi ndani dzina lake, ndipo tidziŵa bwanji kuti ni wolimba mtima?

  2. Kodi Davide akhala kuti, ndipo dzina la atate ndi ambuye ake ndani?

  3. N’cifukwa ciani Yehova auza Samueli kuyenda kunyumba ya Jese ku Betelehemu?

  4. Kodi cicitika n’ciani pamene Jese abweletsa ana ake 7 kwa Samueli?

  5. Pamene Davide abwela, kodi Yehova auza Samueli ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Samueli 17:34, 35.

    Kodi zocitika zimenezi zitsimikizila bwanji kuti Davide anali wolimba mtima, ndipo anali kudalila Yehova? (1 Sam. 17:37)

  2. Ŵelenga 1 Samueli 16:1-14.

    1. Kodi mau a Yehova opezeka pa 1 Samueli 16:7 amatithandiza bwanji kupewa tsankho ndi kukondela anthu cifukwa ca maonekedwe ao? (Mac. 10:34, 35; 1 Tim. 2:4)

    2. Kodi citsanzo ca Sauli cionetsa bwanji kuti ngati Yehova acotsa mzimu wake woyela pa munthu, ndiye kuti munthuyo amakhala ndi mzimu woipa, kapena kuti cikhumbo cofuna kucita zoipa? (1 Sam. 16:14; Mat. 12:43-45; Agal. 5:16)

Nkhani 58

Davide ndi Goliyati

  1. Kodi Goliyati abweletsa mavuto anji pa gulu la asilikali a Aisiraeli?

  2. Kodi Goliyati ni wamkulu bwanji, ndipo ni mphatso yanji imene Mfumu Sauli alonjeza kupatsa munthu amene adzapha Goliyati?

  3. Kodi Davide ayankha bwanji pamene Sauli amuuza kuti sangamenyane ndi Goliyati cifukwa iye ndi mwana?

  4. Poyankha Goliyati, kodi Davide aonetsa bwanji cikhulupililo cake mwa Yehova?

  5. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi Davide agwilitsila nchito ciani kupha Goliyati, ndipo pambuyo pake Afilisti acita ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Samueli 17:1-54.

    1. Kodi n’ciani cinacititsa Davide kuti akhale wopanda mantha, ndipo tingatengele bwanji kulimba mtima kwake? (1 Sam. 17:37, 45; Aef. 6:10, 11)

    2. N’cifukwa ciani Akristu ayenela kupewa mzimu wa mpikisano, monga wa Goliyati, pamene acita zamaseŵela kapena zosangulutsa? (1 Sam. 17:8; Agal. 5:26; 1 Tim. 4:8)

    3. Kodi mau a Davide aonetsa bwanji kuti anali ndi cidalilo cakuti Mulungu adzamuthandiza? (1 Sam. 17:45-47; 2 Mbiri 20:15)

    4. Kodi nkhani imeneyi ionetsa bwanji kuti mpikisano umenewu sunali cabe pakati pa magulu ankhondo aŵili okangana, koma m’ceni-ceni unali pakati pa milungu yonama ndi Mulungu woona, Yehova? (1 Sam. 17:43, 46, 47)

    5. Kodi otsalila odzozedwa angatsatile bwanji citsanzo ca Davide ca kudalila Yehova? (1 Sam. 17:37; Yer. 1:17-19; Chiv. 12:17)

Nkhani 59

Cifukwa Cake Davide Afunikila Kuthaŵa

  1. N’cifukwa ciani Sauli acitila nsanje Davide, koma Yonatani mwana wa Sauli ni wosiyana bwanji?

  2. Kodi n’ciani cicitika tsiku lina pamene Davide alizila Sauli zeze?

  3. Kodi Sauli akamba kuti Davide ayenela kucita ciani akalibe kutenga Mikala, mwana wake wamkazi kukhala mkazi wake, ndipo n’cifukwa ciani Sauli akamba conco?

  4. Pamene Davide alizila Sauli zeze, n’ciani cicitika kacitatu, monga mmene tionela pacithunzi-thunzi?

  5. Kodi Mikala athandiza bwanji kupulumutsa moyo wa Davide, ndipo Davide ayenela kucita ciani kwa zaka 7?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Samueli 18:1-30.

    1. Kodi cikondi cosatha ca Yonatani ndi Davide, cimaimila bwanji cikondi cimene cilipo pakati pa “nkhosa zina” ndi “kagulu ka nkhosa”? (1 Sam. 18:1; Yoh. 10:16; Luka 12:32; Zek. 8:23)

    2. Popeza Yonatani ndiye anali kufunikila kuloŵa m’malo Sauli, kodi lemba la 1 Samueli 18:4 lionetsa bwanji kuti Yonatani anali kugonjela kwambili munthu amene anasankhidwa kukhala mfumu?

    3. Kodi nkhani ya Sauli ionetsa bwanji kuti nsanje ingatsogolele ku chimo lalikulu, ndipo ni cenjezo liti limene titengapo? (1 Sam. 18:7-9, 25; Yak. 3:14-16)

  2. Ŵelenga 1 Samueli 19:1-17.

    Pamene Yonatani akamba ndi Sauli, kodi anaika bwanji moyo wake pangozi? (1 Sam. 19:1, 6; Miy.16:14)

Nkhani 60

Abigayeli ndi Davide

  1. Kodi dzina la mkazi amene abwela kudzakumana ndi Davide pacithunzi-thunzi apa ndani, ndipo ameneyu ni mkazi wabwanji?

  2. Kodi Nabala ndani?

  3. N’cifukwa ciani Davide atuma anyamata ake kuti akapemphe thandizo kwa Nabala?

  4. Kodi Nabala auza ciani anyamata a Davide, ndipo Davide acita ciani?

  5. Kodi Abigayeli aonetsa bwanji kuti ni mkazi wanzelu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Samueli 22:1-4.

    Kodi banja la Davide lipeleka citsanzo cabwino cabwanji ca mmene tiyenela kuthandizilana wina ndi mnzake m’gulu lonse la abale Acikristu? (Miy. 17:17; 1 Ates. 5:14)

  2. Ŵelenga 1 Samueli 25:1-43.

    1. N’cifukwa ciani Nabala afotokozedwa kuti ni munthu wacipongwe kwambili? (1 Sam. 25:2-5, 10, 14, 21, 25)

    2. Kodi akazi acikristu masiku ano angaphunzile ciani pa citsanzo ca Abigayeli? (1 Sam. 25:32, 33; Miy. 31:26; Aef. 5:24)

    3. Abigayeli analetsa Davide kucita zolakwa ziŵili ziti? (1 Sam. 25:31, 33; Aroma 12:19; Aef. 4:26)

    4. Kodi mmene Davide anacitila ndi zimene Abigayeli anakamba, ziyenela kuthandiza bwanji amuna masiku ano kuona akazi mmene Yehova amawaonela? (Mac. 21:8, 9; Aroma 2:11; 1 Pet. 3:7)

Nkhani 61

Davide Aikidwa Kukhala Mfumu

  1. Kodi Davide ndi Abisai anacita ciani pamene Sauli anali gone mu hema lake?

  2. Kodi Davide anafunsa Sauli mafunso ati?

  3. Kodi Davide anayenda kuti pamene anasiyana ndi Sauli?

  4. Kodi n’ciani cinacititsa kuti Davide akwiye cakuti analemba nyimbo yokondweletsa kwambili?

  5. Kodi Davide anali ndi zaka zingati pamene anakhala mfumu mu Heburoni, ndipo maina a ana ake ena anali ndani?

  6. Kodi n’kuti kumene Davide nthawi ina analamulila monga mfumu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Samueli 26:1-25.

    1. Mau a Davide opezeka pa 1 Samueli 26:11 amaonetsa bwanji maganizo amene tiyenela kukhala nao ponena za makonzedwe a Mulungu? (Sal. 37:7; Aroma 13:2)

    2. Ngati tiyesa-yesa kuonetsa kukoma mtima koma ena sayamikila kuyesa-yesa kwathu, kodi mau a Davide opezeka pa 1 Samueli 26:23 angatithandize bwanji kukhalabe ndi maganizo abwino? (1 Maf. 8:32; Sal. 18:20)

  2. Ŵelenga 2 Samueli 1:26.

    Kodi Akristu masiku ano angakhale bwanji “okondana kwambili” monga mmene Davide ndi Yonatani analili? (1 Pet. 4:8; Akol. 3:14; 1 Yoh. 4:12)

  3. Ŵelenga 2 Samueli 5:1-10.

    1. Kodi Davide analamulila monga mfumu kwa zaka zingati, ndipo nthawi imeneyi inagaŵidwa bwanji? (2 Sam. 5:4, 5)

    2. Kodi Davide anapambana cifukwa ca ndani, ndipo zimenezi ziyenela kutikumbutsa ciani masiku ano? (2 Sam. 5:10; 1 Sam. 16:13; 1 Akor. 1:31; Afil. 4:13)

Nkhani 62

Mavuto mu Nyumba ya Davide

  1. Mothandizidwa ndi Yehova, kodi n’ciani cicitikila dziko la Kanani potsilizila pake?

  2. Kodi n’ciani cicitika tsiku lina pamene Davide ali pa mtenje wa nyumba yacifumu?

  3. N’cifukwa ciani Yehova akwiyila Davide kwambili?

  4. Malinga ndi cithunzi-thunzi, kodi Yehova atumiza ndani kuti auze Davide za macimo ake, ndipo munthuyo akamba kuti n’ciani cidzacitikila Davide?

  5. Kodi Davide akhala ndi mavuto abwanji?

  6. Pambuyo pa Davide, ndani akhala mfumu ya Isiraeli?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 2 Samueli 11:1-27.

    1. Kodi kucita zambili muutumiki wa Yehova kumatichinjiliza bwanji?

    2. Kodi Davide anagwela bwanji mu chimo, ndipo n’cenjezo lanji limene atumiki a Yehova atengapo masiku ano? (2 Sam. 11:2; Mat. 5:27-29; 1 Akor. 10:12; Yak. 1:14, 15)

  2. Ŵelenga 2 Samueli 12:1-18.

    1. Kodi akulu ndi makolo angaphunzile ciani akaona mmene Natani anafikila kwa Davide kuti amupatse uphungu? (2 Sam. 12:1-4; Miy. 12:18; Mat. 13:34)

    2. N’cifukwa ciani Yehova anamucitila cifundo Davide? (2 Sam. 12:13; Sal. 32:5; 2 Akor. 7:9, 10)

Nkhani 63

Solomo Mfumu Yanzelu

  1. Kodi Yehova afunsa Solomo ciani, ndipo iye ayankha bwanji?

  2. Popeza Yehova akondwela ndi zimene Solomo apempha, kodi amulonjeza ciani?

  3. Kodi ni vuto lalikulu liti limene akazi aŵili afotokozela Solomo?

  4. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi Solomo alithetsa bwanji vutolo?

  5. Kodi ulamulilo wa Solomo unali bwanji, ndipo n’cifukwa ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Mafumu 3:3-28.

    1. Kodi amuna amene apatsidwa udindo m’gulu la Mulungu, angaphunzile ciani pa mau a Solomo ocokela pansi pamtima opezeka pa 1 Mafumu 3:7? (Sal. 119:105; Miy. 3:5, 6)

    2. Kodi pempho la Solomo n’citsanzo cabwino bwanji ca zinthu zoyenela zimene tifunikila kuchula m’pemphelo? (1 Maf. 3:9, 11; Miy. 30:8, 9; 1 Yoh. 5:14)

    3. Kodi mmene Solomo anathetsela vuto la akazi aŵili, citipatsa cidalilo canji mu ulamulilo wamtsogolo wa Solomo wamkulu, Yesu Kristu? (1 Maf. 3:28; Yes. 9:6, 7; 11:2-4)

  2. Ŵelenga 1 Mafumu 4:29-34.

    1. Kodi Yehova anayankha bwanji pempho la Solomo lokhala ndi mtima womvela? (1 Maf. 4:29)

    2. Poona mmene anthu anacitila pofuna kumvetsela nzelu za Solomo, kodi kuphunzila mau a Mulungu tiyenela kukuona bwanji? (1 Maf. 4:29, 34; Yoh. 17:3; 2 Tim. 3:16)

Nkhani 64

Solomo Amanga Kacisi

  1. Kodi cimutengela nthawi itali bwanji Solomo kumanga kacisi wa Yehova, ndipo n’cifukwa ciani cimango cimeneci citenga ndalama zambili?

  2. Kodi mu kacisi muli zipinda zingati, ndipo mu cipinda ca mkati aikamo ciani?

  3. Kodi Solomo akamba ciani m’pemphelo lake pamene atsiliza kumanga kacisi?

  4. Kodi Yehova waonetsa bwanji kuti wakondwela ndi pemphelo la Solomo?

  5. Kodi akazi a Solomo am’pangitsa kucita ciani, ndipo n’ciani cim’citikila Solomo?

  6. N’cifukwa ciani Yehova akwiyila Solomo, ndipo Yehova akamba ciani kwa iye?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Mbiri 28:9, 10.

    Malinga ndi mau a Davide opezeka pa 1 Mbiri 28:9, 10, kodi tiyenela kuyesa-yesa kucita ciani tsiku ndi tsiku? (Sal. 19:14; Afil. 4:8, 9)

  2. Ŵelenga 2 Mbiri 6:12-21, 32-42.

    1. Kodi Solomo anaonetsa bwanji kuti palibe nyumba yomangidwa ndi munthu imene Mulungu Wam’mwamba-mwamba angakwanemo? (2 Mbiri 6:18; Mac. 17:24, 25)

    2. Kodi mau a Solomo opezeka pa 2 Mbiri 6:32, 33 aonetsa ciani ponena za Yehova? (Mac. 10:34, 35; Agal. 2:6)

  3. Ŵelenga 2 Mbiri 7:1-5.

    Pamene Aisiraeli anaona ulemelelo wa Yehova, anasonkhezeleka kum’tamanda, mofanana ndi zimenezi, kodi ife masiku ano tiyenela kukhudzidwa bwanji tikaganizila mmene Yehova wadalitsila anthu ake? (2 Mbiri 7:3; Sal. 22:22; 34:1; 96:2)

  4. Ŵelenga 1 Mbiri 11:9-13.

    Kodi moyo wa Solomo umaonetsa bwanji kufunika kokhalabe wokhulupilika mpaka mapeto? (1 Maf. 11:4, 9; Mat. 10:22; Chiv. 2:10)

Nkhani 65

Ufumu Ugaŵanika

  1. Chula maina a amuna aŵili ali pacithunzi-thunzi apa, ndipo ndi anthu abwanji?

  2. Kodi Ahiya acita ciani ndi mkanjo umene wavala, ndipo kucita zimenezi kutanthauza ciani?

  3. Kodi Solomo afuna kumucita ciani Yeroboamu?

  4. N’cifukwa niji anthu aika Yeroboamu kukhala mfumu ya mafuko 10?

  5. N’cifukwa ciani Yeroboamu apanga ana a ng’ombe aŵili a golide, ndipo n’ciani cicitika mu dzikolo pambuyo pake?

  6. Kodi n’ciani cicitika mu ufumu wa mafuko aŵili ndi kacisi wa Yehova ku Yerusalemu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Mafumu 11:26-43.

    Kodi Yeroboamu anali munthu wabwanji, ndipo Yehova anamulonjeza ciani akanamvela malamulo a Mulungu? (1 Maf. 11:28, 38)

  2. Ŵelenga 1 Mafumu 12:1-33.

    1. Kodi makolo ndi akulu angaphunzile ciani pacitsanzo coipa ca Rehoboamu ponena za kugwilitsila nchito udindo molakwa? (1 Maf. 12:13; Mlal. 7:7; 1 Pet. 5:2, 3)

    2. Kodi acicepele masiku ano angapite kuti kaamba ka citsogozo codalilika popanga zosankha zazikulu? (1 Maf. 12:6, 7; Miy. 1:8, 9; 2 Tim. 3:16, 17; Aheb. 13:7)

    3. Kodi n’ciani cinacititsa Yeroboamu kukhazikitsa malo aŵili olambililako ana a n’gombe, ndipo zimenezi zinaonetsa bwanji kuti sanakhulupilile Yehova? (1 Maf. 11:37; 12:26-28)

    4. Kodi ndani anatsogolela anthu a mu ufumu wa mafuko 10 kuti aleke kulambila koona? (1 Maf. 12:32, 33)

Nkhani 66

Yezebeli—Mfumukazi Yoipa

  1. Kodi Yezebeli ndani?

  2. N’cifukwa ciani Mfumu Ahabu anali ndi cisoni tsiku lina?

  3. Kodi Yezebeli acita ciani kuti atengele mwamuna wake Ahabu munda wa mpesa wa Naboti?

  4. Kodi Yehova atumiza ndani kuti akalange Yezebeli?

  5. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa, n’ciani cicitika pamene Yehu afika ku nyumba yacifumu ya Yezebeli?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Mafumu 16:29-33 ndi 18:3, 4.

    Kodi zinthu zinali zoipa bwanji mu Isiraeli pamene Mfumu Ahabu anali kulamulila? (1 Maf. 14:9)

  2. Ŵelenga 1 Mafumu 21:1-16.

    1. Kodi Naboti anaonetsa bwanji kuti anali wolimba mtima ndi wokhulupilika kwa Yehova? (1 Maf. 21:1-3; Lev. 25:23-28)

    2. Kodi citsanzo ca Ahabu citiphunzitsa ciani pamene tikumana ndi zinthu zokhumudwitsa? (1 Maf. 21:4; Aroma 5:3-5)

  3. Ŵelenga 2 Mafumu 9:30-37.

    Kodi cangu ca Yehu pocita cifunilo ca Yehova citiphunzitsa ciani? (2 Maf. 9:4-10; 2 Akor. 9:1, 2; 2 Tim. 4:2)

Nkhani 67

Yehosafati Adalila Yehova

  1. Kodi Yehosafati ndani, ndipo akhalako panthawi iti?

  2. N’cifukwa ciani Aisiraeli acita mantha, ndipo ambili acita ciani?

  3. Kodi Yehova apeleka yankho lanji ku pemphelo la Yehosafati?

  4. Kodi Yehova apangitsa ciani kucitika nkhondo ikalibe kuyamba?

  5. Kodi tiphunzila ciani kwa Yehosafati?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 2 Mbiri 20:1-30.

    1. Kodi Yehosafati anaonetsa bwanji zimene atumiki a Yehova okhulupilika ayenela kucita akakumana ndi zoopsa? (2 Mbiri 20:12; Sal. 25:15; 62:1)

    2. Popeza Yehova nthawi zonse amagwilitsila nchito njila yokambitsilana ndi anthu ake, kodi masiku ano amagwilitsila nchito njila iti? (2 Mbiri 20:14, 15; Mat. 24:45-47; Yoh. 15:15)

    3. Pamene Mulungu adzayambitsa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,” kodi zinthu zidzafanana bwanji ndi nthawi ya Yehosafati? (2 Mbiri 20:15, 17; 32:8; Chiv. 16:14, 16)

    4. Potengela citsanzo ca Alevi, kodi apainiya ndi amishonale masiku ano amathandiza bwanji panchito yolalikila padziko lonse? (2 Mbiri 20:19, 21; Aroma 10:13-15; 2 Tim. 4:2)

Nkhani 68

Anyamata Aŵili Amene Akhalanso ndi Moyo

  1. Kodi anthu atatu amene ali pacithunzi-thunzi ndani, ndipo n’ciani cicitika kwa mnyamata?

  2. Kodi Eliya apemphela ciani ponena za mnyamata, ndipo pacitika ciani?

  3. Kodi wothandiza wa Eliya ndani dzina lake?

  4. N’cifukwa ciani Elisa anaitanidwa kunyumba ya mkazi wa ku Sunemu?

  5. Kodi Elisa acita ciani, ndipo n’ciani cicitika kwa mwana wakufa?

  6. Kodi Yehova ali ndi mphamvu zabwanji, monga mmene anaonetsela kupyolela mwa Eliya ndi Elisa?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Mafumu 17:8-24.

    1. Kodi kumvela ndi cikhulupililo ca Eliya zinayesedwa bwanji? (1 Maf. 17:9; 19:1-4, 10)

    2. N’cifukwa ciani cikhulupililo ca mkazi wa masiye wa ku Zarefati cinali capadela kwambili? (1 Maf. 17:12-16; Luka 4:25, 26)

    3. Kodi zimene mkazi wa masiye wa ku Zarefati anakumana nazo zimaonetsa bwanji kuti mau a Yesu opezeka pa Mateyu 10:41, 42, ndi oona? (1 Maf. 17:10-12, 17, 23, 24)

  2. Ŵelenga 2 Mafumu 4:8-37.

    1. Kodi mkazi wa ku Sunemu atiphunzitsa ciani pankhani yoceleza alendo? (2 Maf. 4:8; Luka 6:38; Aroma 12:13; 1 Yoh. 3:17)

    2. Kodi ni m’njila ziti mmene tingaonetsele kukoma mtima kwa atumiki a Mulungu masiku ano? (Mac. 20:35; 28:1, 2; Agal. 6:9, 10; Aheb. 6:10)

Nkhani 69

Kamtsikana Kathandiza Munthu Wamphamvu Kwambili

  1. Pacithunzi-thunzi apa, kodi kamtsikana kauza ciani mkaziyu?

  2. Kodi mkazi amene ali pacithunzi-thunzi ndani, ndipo kamtsikana kacita ciani panyumba pake?

  3. Kodi Elisa auza mtumiki wake kuti auze Namani ciani, ndipo n’cifukwa ciani Namani akalipa?

  4. Kodi cicitika n’ciani pamene Namani amvela kwa mtumiki wake?

  5. N’cifukwa ciani Elisa akana mphatso ya Namani, nanga Gehazi acita ciani?

  6. N’ciani cicitika kwa Gehazi, ndipo tiphunzila ciani pa zimenezi?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 2 Mafumu 5:1-27.

    1.    

    2. N’cifukwa ciani ndi bwino kukumbukila citsanzo ca Namani pamene tipatsidwa uphungu wa m’Malemba? (2 Maf. 5:15; Aheb. 12:5, 6; Yak. 4:6)

    3. Kodi tiphunzila ciani tikaona kusiyana kwa citsanzo ca Elisa ndi ca Gehazi? (2 Maf. 5:9, 10, 14-16, 20; Mat. 10:8; Mac. 5:1-5; 2 Akor. 2:17)

Nkhani 70

Yona ndi Cinsomba

  1. Kodi Yona ndani, ndipo Yehova amuuza kucita ciani?

  2. Popeza kuti Yona safuna kuyenda kumene Yehova wamuuza, kodi iye acita ciani?

  3. Kodi Yona auza oyendetsa boti kucita ciani kuti cimphepo cileke?

  4. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi n’ciani cicitika pamene Yona ambila m’madzi?

  5. Kodi Yona akhala m’cinsomba masiku angati, ndipo acita ciani pamene ali mmenemo?

  6. Kodi Yona ayenda kuti pamene acoka m’cinsomba, ndipo zimenezi zitiphunzitsa ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yona 1:1-17.

    Kodi Yona anaiona bwanji nchito yolalikila ku Nineve? (Yona 1:2, 3; Miy. 3:7; Mlal. 8:12)

  2. Ŵelenga Yona 2:1, 2, 10.

    Kodi cokumana naco ca Yona citipatsa bwanji cidalilo cakuti Yehova amayankha mapemphelo athu? (Sal. 22:24; 34:6; 1 Yoh. 5:14)

  3. Ŵelenga Yona 3:1-10.

    1. Kodi n’cilimbikitso canji cimene tipeza poona kuti Yehova anapitilizabe kugwilitsila nchito Yona, ngakhale kuti poyamba analephela kucita nchito yake? (Sal. 103:14; 1 Pet. 5:10)

    2. Kodi zimene zinacitikila Yona pamene anayenda ku Nineve, zitiphunzitsa ciani pankhani yoweluzilatu anthu a m’gao lathu? (Yona 3:6-9; Mlal. 11:6; Mac. 13:48)

Nkhani 71

Mulungu Analonjeza Paladaiso

  1. Kodi Yesaya ndani, anakhalako liti, ndipo Yehova anamuonetsa ciani?

  2. Kodi mau akuti “paladaiso” atanthauza ciani, ndipo akukumbutsa ciani?

  3. Kodi Yehova anauza Yesaya kulemba ciani ponena za Paladaiso yatsopano?

  4. N’cifukwa ciani Adamu ndi Hava anataya malo ao abwino?

  5. Kodi Yehova walonjeza kuwapatsa ciani anthu amene amukonda?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yesaya 11:6-9.

    1. Kodi Mau a Mulungu amaonetsa bwanji mtendele umene udzakhalapo pakati pa zinyama ndi anthu m’dziko latsopano? (Sal. 148:10, 13; Yes. 65:25; Ezek. 34:25)

    2. Kodi ndi kukwanilitsika kwa kuuzimu kuti kwa mau a Yesaya kumene kucitika masiku ano pakati pa anthu a Yehova? (Aroma 12:2; Aef. 4:23, 24)

    3. Kodi ndani ayenela kuyamikilidwa cifukwa ca kusintha makhalidwe kumene anthu acita tsopano, ndi kumene adzacita m’dziko latsopano? (Yes. 48:17, 18; Agal. 5:22, 23; Afil. 4:7)

  2. Ŵelenga Chivumbulutso 21:3, 4.

    1. Kodi malemba aonetsa bwanji kuti kukhala pamodzi ndi anthu padziko lapansi, kumene Mulungu adzacita kumatanthauza kukhala nao mophiphilitsa, osati kukhala nao kweni-kweni? (Lev. 26:11, 12; 2 Mbiri 6:18; Yes. 66:1; Chiv. 21:2, 3, 22-24)

    2. Kodi ni misozi ndi kupweteka kwabwanji kumene kudzacotsedwa? (Luka 8:49-52; Aroma 8:21, 22; Chiv. 21:4)

Nkhani 72

Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya

  1. Kodi mwamuna amene ali pacithunzi-thunzi ndani, ndipo n’cifukwa ciani ali m’mavuto kwambili?

  2. Kodi ni makalata abwanji amene Hezekiya waika pamaso pa Mulungu, ndipo Hezekiya apemphela kuti ciani?

  3. Kodi Hezekiya ni mfumu yabwanji, ndipo ni uthenga wanji umene Yehova atumiza kwa iye kupitila mwa mneneli Yesaya?

  4. Kodi mngelo wa Yehova acita ciani kwa Asuri, monga mmene tionela pacithunzi-thunzi?

  5. Ngakhale kuti ufumu wa mafuko aŵili uli pamtendele kwa kanthawi, kodi n’ciani cicitika pambuyo pa imfa ya Hezekiya?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 2 Mafumu 18:1-36.

    1. Kodi Rabisake amene anali wokambilako Asuri, ayesa bwanji kufooketsa cikhulupililo ca Aisiraeli? (2 Maf. 18:19, 21; Eks. 5:2; Sal. 64:3)

    2. Pocita ndi otsutsa, kodi mboni za Yehova zimatengela bwanji citsanzo ca Hezekiya? (2 Maf. 18:36; Sal. 39:1; Miy. 26:4; 2 Tim. 2:24)

  2. Ŵelenga 2 Mafumu 19:1-37.

    1. Kodi anthu a Yehova masiku ano amatengela bwanji citsanzo ca Hezekiya panthawi ya mavuto? (2 Maf. 19:1, 2; Miy. 3:5, 6; Aheb. 10:24, 25; Yak. 5:14, 15)

    2. Kodi Mfumu Senakeribu anagonjetsedwa bwanji pambali zitatu, ndipo amaimila ndani mwaulosi? (2 Maf. 19:32, 35, 37; Chiv. 20:2, 3)

  3. Ŵelenga 2 Mafumu 21:1-6, 16.

    N’cifukwa ciani tingakambe kuti Manase anali mfumu yoipa kwambili kupambana mafumu onse amene analamulila mu Yerusalemu? (2 Mbiri 33:4-6, 9)

Nkhani 73

Mfumu Yabwino Yotsilizila ya Isiraeli

  1. Kodi Yosiya ali ndi zaka zingati pamene akhala mfumu, ndipo atalamulila kwa zaka 7 ayamba kucita ciani?

  2. Pacithunzi-thunzi coyambilila ici, kodi Yosiya acita ciani?

  3. Kodi wansembe wamkulu apeza ciani pamene amuna akonza kacisi?

  4. N’cifukwa ciani Yosiya ang’amba malaya ake?

  5. Kodi ni uthenga uti wa Yehova umene Hulida mneneli wacikazi auza Yosiya?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 2 Mbiri 34:1-28.

    1. Kodi Yosiya apeleka citsanzo canji kwa anthu amene anapilila mavuto ambili pamene anali ana? (2 Mbiri 33:21-25; 34:1, 2; Sal. 27:10)

    2. Kodi Yosiya anacita zinthu zofunika ziti kuti apititse patsogolo kulambila koona m’zaka za 8, 12, ndi 18 za kulamulila kwake? (2 Mbiri 34:3, 8)

    3. Kodi tiphunzila ciani pa citsanzo ca Yosiya ndi wansembe wamkulu Hilikiya pankhani yosamalila malo athu olambilila? (2 Mbiri 34:9-13; Miy. 11:14; 1 Akor. 10:31)

Nkhani 74

Mwamuna Wosaopa Munthu

  1. Kodi mwamuna wacinyamata pacithunzi-thunzi apa ndani?

  2. Kodi Yeremiya aganiza ciani zakuti iye akhale mneneli, koma Yehova amuuza ciani?

  3. Kodi Yeremiya apitiliza kuuza anthu uthenga wanji?

  4. Kodi ansembe acita ciani kuti alefule Yeremiya, koma Yeremiya aonetsa bwanji kuti saopa?

  5. Kodi n’ciani cicitika pamene Aisiraeli sasintha makhalidwe ao?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yeremiya 1:1-8.

    1. Monga mmene tionela citsanzo ca Yeremiya, n’ciani cimene ciyeneletsa munthu kucita nchito ya Yehova? (2 Akor. 3:5, 6)

    2. Kodi citsanzo ca Yeremiya cipeleka cilimbikitso canji kwa Akristu acicepele masiku ano? (Mlal. 12:1; 1 Tim. 4:12)

  2. Ŵelenga Yeremiya 10:1-5.

    Kodi ni fanizo loyenelela liti limene Yeremiya agwilitsila nchito kuonetsa kuti n’kusoŵa nzelu kukhulupilila mafano? (Yer. 10:5; Yes. 46:7; Hab. 2:19)

  3. Ŵelenga Yeremiya 26:1-16.

    1. Pofalitsa uthenga wocenjeza masiku ano, kodi otsalila odzozedwa alabadila bwanji mau a Yehova kwa Yeremiya akuti ‘usacotsepo mau ngakhale amodzi’? (Yer. 26:2; Deut. 4:2; Mac. 20:27)

    2. Kodi Yeremiya apeleka citsanzo canji cabwino masiku ano kwa Mboni za Yehova pankhani yofalitsa uthenga wocenjeza wa Yehova? (Yer. 26:8, 12, 14, 15; 2 Tim. 4:1-5)

  4. Ŵelenga 2 Mafumu 24:1-17.

    Kodi n’zotulukapo zoipa ziti zimene Ayuda anakhala nazo cifukwa ca kukhala osakhulupilika kwa Yehova? (2 Maf. 24:2-4, 14)

Nkhani 75

Anyamata Anai ku Babulo

  1. Kodi anyamata anai amene ali pacithunzi-thunzi ndani, ndipo n’cifukwa ciani ali ku Babulo?

  2. Kodi Nebukadinezara afuna kucita ciani kwa anyamata anai amenewa, ndipo walamula atumiki ake kucita ciani?

  3. Kodi Danieli apempha ciani pa zakudya ndi zakumwa zimene iye ndi anzake atatu ayenela kumapatsidwa?

  4. Pambuyo pakudya zakudya zamasamba kwa masiku 10, kodi Danieli ndi anzake atatu aoneka bwanji kuyelekezela ndi anyamata ena?

  5. Kodi Danieli ndi anzake atatu anapezeka bwanji m’nyumba ya mfumu, ndipo aposa bwanji ansembe ndi amuna anzelu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Danieli 1:1-21.

    1. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tilimbane ndi ziyeso ndi kugonjetsa zofooka? (Dan. 1:8; Gen. 39:7, 10; Agal. 6:9)

    2. Kodi acicepele masiku ano angayesedwe kapena kukakamizidwa bwanji pankhani yoloŵelela m’zimene ena amati “zakudya zabwino”? (Dan. 1:8; Miy. 20:1; 2 Akor. 6:17–7:1)

    3. Kodi nkhani ya m’Baibo ya Aheberi acicepele anai, itithandiza bwanji za mmene tiyenela kuonela maphunzilo a kudziko? (Dan. 1:20; Yes. 54:13; 1 Akor. 3:18-20)

Nkhani 76

Yerusalemu Aonongedwa

  1. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi n’ciani cicitikila Yerusalemu ndi Aisiraeli?

  2. Kodi Ezekieli ndani, ndipo Yehova amuonetsa zinthu zanji zodabwitsa?

  3. Cifukwa cakuti Aisiraeli salemekeza Yehova, kodi iye awalonjeza ciani?

  4. Kodi Mfumu Nebukadinezara acita ciani pamene Aisiraeli am’pandukila?

  5. N’cifukwa ciani Yehova walola cionongeko cacikulu ici kucitikila Aisiraeli?

  6. Kodi dziko la Isiraeli litsala bwanji lopanda anthu, ndipo kwautali wabwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 2 Mafumu 25:1-26.

    1. Kodi Zedekiya anali ndani, n’ciani cinamucitikila, ndipo zimenezi zikwanilitsa bwanji ulosi wa m’Baibo? (2 Maf. 25:5-7; Ezek. 12:13-15)

    2. Kodi Yehova anapatsa ndani mlandu wa kusakhulupilika konse kwa Aisiraeli? (2 Maf. 25:9, 11, 12, 18, 19; 2 Mbiri 36:14, 17)

  2. Ŵelenga Ezekieli 8:1-18.

    Kodi Machalichi Acikristu atsatila bwanji Aisiraeli ampatuko amene anali kulambila dzuŵa? (Ezek. 8:16; Yes. 5:20, 21; Yoh. 3:19-21; 2 Tim. 4:3)

Nkhani 77

Iwo Sanagwadile Fano

  1. Kodi ni lamulo liti limene Nebukadinezara, mfumu ya Babulo, apeleka kwa anthu?

  2. N’cifukwa ciani anzake atatu a Danieli sagwadila fano lagolide?

  3. Pamene Nebukadinezara auzanso Aheberi atatu aja kuti agwadile fano, kodi io aonetsa bwanji cikhulupililo cao mwa Yehova?

  4. Kodi Nebukadinezara auza anchito ake kuti acite ciani kwa Sadirake, Mesake ndi Abedinego?

  5. Kodi Nebukadinezara aona ciani pamene ayang’ana mu ng’anjo ya moto?

  6. N’cifukwa ciani mfumu itamanda Mulungu wa Sadirake, Mesake ndi Abedinego, ndipo io atipatsa citsanzo canji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Danieli 3:1-30.

    1. Kodi Aheberi acicepele atatu aonetsa khalidwe lanji, limene atumiki a Mulungu onse ayenela kutengelako pamene cikhulupililo cao ciyesedwa? (Dan. 3:17, 18; Mat. 10:28; Aroma 14:7, 8)

    2. Kodi ni phunzilo lofunika liti limene Yehova Mulungu anaphunzitsa Nebukadinezara? (Dan. 3:28, 29; 4:34, 35)

Nkhani 78

Dzanja Lilemba Pacipupa

  1. Kodi n’ciani cicitika pamene mfumu ya Babulo ikhala ndi phwando lalikulu ndipo igwilitsila nchito makapu ndi mbale zimene inatenga ku kacisi wa Yehova ku Yerusalemu?

  2. Kodi Belisazara auza ciani amuna ake anzelu, koma io alephela kucita ciani?

  3. Kodi amai a mfumu auza mfumu kucita ciani?

  4. Malinga n’zimene Danieli auza mfumu, n’cifukwa ciani Mulungu watumiza dzanja kuti lilembe pacipupa?

  5. Kodi Danieli afotokoza kuti mau amene ali pacipupa atanthauza ciani?

  6. Kodi n’ciani cicitika pamene Danieli akali kukamba?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Danieli 5:1-31.

    1. Chula kusiyana kulipo pakati pa mantha aumulungu ndi mantha amene Belisazara anamvela pamene anaona mau olembedwa pacipupa. (Dan. 5:6, 7; Sal. 19:9; Aroma 8:35-39)

    2. Kodi Danieli anaonetsa bwanji kulimba mtima kwakukulu pamene anali kukamba ndi Belisazara ndi nduna zake? (Dan. 5:17, 18, 22, 26-28; Mac. 4:29)

    3. Kodi lemba la Danieli caputa 5, ligogomeza bwanji ulamulilo wa Yehova m’cilengedwe conse? (Dan. 4:17, 25; 5:21)

Nkhani 79

Danieli mu Dzenje la Mikango

  1. Kodi Dariyo ndani, ndipo amaona bwanji Danieli?

  2. Kodi anthu ansanje apangitsa Dariyo kucita ciani?

  3. Kodi Danieli acita ciani pamene amvela za lamulo latsopano?

  4. N’cifukwa ciani Dariyo akalipa kwambili cakuti sagona tulo usiku, ndipo acita ciani m’maŵa patsiku lotsatila?

  5. Kodi Danieli ayankha bwanji kwa Dariyo?

  6. N’ciani cicitika kwa amuna oipa amene anafuna kupha Danieli, ndipo Dariyo alemba ciani kwa anthu onse mu ufumu wake?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Danieli 6:1-28.

    1. Kodi ciwembu cimene anthu anacitila Danieli, citikumbutsa ciani tikaona zimene otsutsa masiku ano amacita kuti nchito ya Mboni za Yehova isapite patsogolo? (Dan. 6:7; Sal. 94:20; Yes 10:1, Aroma 8:31)

    2. Kodi atumiki a Mulungu masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca Danieli pankhani yomvela “olamulila akulu-akulu”? (Dan. 6:5, Aroma 13:1, Mac. 5:29)

    3. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Danieli pankhani yotumikila Mulungu ‘mosalekeza’? (Dan. 6:16, 20; Afil. 3:16; Chiv. 7:15)

Nkhani 80

Anthu a Mulungu Acoka ku Babulo

  1. Monga mmene tionela pacithunzi-thunzi, kodi Aisiraeli acita ciani?

  2. Kodi Koresi aukwanilitsa bwanji ulosi umene Yehova anapeleka kupyolela mwa Yesaya?

  3. Kodi Koresi awauza ciani Aisiraeli amene sangabwelele ku Yerusalemu?

  4. Kodi Koresi apatsa ciani anthu kuti abweze ku Yerusalemu?

  5. Kodi ciwatengela utali wabwanji Aisiraeli kuti akafike ku Yerusalemu?

  6. Kodi papita zaka zingati kucokela pamene mu Yerusalemu munatsala mulibiletu anthu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yesaya 44:28 ndi 45:1-4.

    1. Kodi Yehova anatsimikizila bwanji kuti ulosi wokhudza Koresi udzakwanilitsika? (Yes. 55:10, 11; Aroma 4:17)

    2. Kodi ulosi wa Yesaya wokhudza Koresi, uonetsa bwanji mphamvu za Yehova Mulungu zonenelatu zakutsogolo (Yes. 42:9; 45:21; 46:10, 11; 2 Pet. 1:20)

  2. Ŵelenga Ezara 1:1-11.

    Tikaona citsanzo ca anthu amene sanakwanitse kubwelela ku Yerusalemu, kodi masiku ano tingalimbikitse bwanji anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse? (Ezara 1:4, 6; Aroma 12:13; Akol. 4:12)

Nkhani 81

Kudalila Thandizo la Mulungu

  1. Kodi ni anthu angati amene ayenda ulendo wautali wocoka ku Babulo kupita ku Yerusalemu, ndipo pamene afika kumeneko apezako ciani?

  2. Pamene afika, kodi Aisiraeli ayamba kumanga ciani? Koma adani ao acita ciani?

  3. Kodi Hagai ndi Zekariya ndani, ndipo awauza ciani anthu?

  4. N’cifukwa ciani Tatenai atumiza kalata ku Babulo, ndipo alandila yankho lanji?

  5. Kodi Ezara acita ciani pamene amvela za nchito yokonza kacisi wa Yehova?

  6. Kodi n’cifukwa ciani Ezara apemphela monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa, ndipo zimenezi zitiphunzitsa ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Ezara 3:1-13.

    Ngati tapezeka kumalo kumene kulibe mpingo wa anthu a Mulungu, kodi n’ciani cimene tiyenela kupitiliza kucita? (Ezara 3:3, 6; Mac. 17:16, 17; Aheb. 13:15)

  2. Ŵelenga Ezara 4:1-7.

    Kodi Zerubabele apeleka citsanzo canji kwa anthu a Yehova pankhani ya kuphatikiza zipembedzo? (Eks. 34:12; 1 Akor. 15:33; 2 Akor. 6:14-17)

  3. Ŵelenga Ezara 5:1-5, 17 ndi 6:1-22.

    1. N’cifukwa ciani otsutsa analephela kuletsa nchito yomanga kacisi? (Ezara 5:5; Yes. 54:17)

    2. Kodi zimene akulu a Ayuda acita, ziwathandiza bwanji akulu acikristu pankhani yopempha citsogozo ca Yehova pamene akumana ndi otsutsa? (Ezara 6:14; Sal. 32:8; Aroma 8:31; Yak. 1:5)

  4. Ŵelenga Ezara 8:21-23, 28-36.

    Tikalibe kucita cinthu ciliconse, kodi n’citsanzo ca Ezara citi cimene tiyenela kutengela? (Ezara 8:23; Sal. 127:1; Miy. 10:22; Yak. 4:13-15)

Nkhani 82

Mordekai ndi Estere

  1. Kodi Mordekai ndi Estere ndani?

  2. N’cifukwa ciani Mfumu Ahaswero ifuna kukwatila mkazi wina, ndipo isankha ndani?

  3. Kodi Hamani ndani, ndipo n’ciani cim’kalipitsa kwambili?

  4. Kodi ni lamulo liti limene lipangidwa, ndipo Estere acita ciani pamene alandila uthenga kucokela kwa Mordekai?

  5. Kodi n’ciani cicitika kwa Hamani? Nanga n’ciani cicitika kwa Mordekai?

  6. Kodi Aisiraeli apulumuka bwanji kwa adani ao?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Estere 2:12-18.

    Kodi Estere anaonetsa bwanji kufunika kwa kukhala ndi “mzimu wabata ndi wofatsa”? (Estere 2:15; 1 Pet. 3:1-5)

  2. Ŵelenga Estere 4:1-17.

    Estere anapatsidwa mwai wocilikiza kulambila koona, kodi ifenso masiku ano tapatsidwa mwai wanji woonetsa kudzipeleka ndi kukhulupilika kwathu kwa Yehova? (Estere 4:13, 14; Mat. 5:14-16; 24:14)

  3. Ŵelenga Estere 7:1-6.

    Monga mmene Estere anacitila, kodi anthu a Mulungu ambili masiku ano alola bwanji kukumana ndi mazunzo? (Estere 7:4; Mat. 10:16-22; 1 Pet. 2:12)

Nkhani 83

Mpanda wa Yerusalemu

  1. Kodi Aisiraeli anali kumva bwanji kuona Yerusalemu mzinda wao ulibe mpanda?

  2. Kodi Nehemiya ndani?

  3. Kodi nchito yake n’ciani, ndipo n’cifukwa ciani ni yofunika?

  4. Kodi ni uthenga wanji umene upangitsa Nehemiya kukhala wacisoni, ndipo acita ciani?

  5. Kodi mfumu Aritasasta aonetsa bwanji kukoma mtima kwa Nehemiya?

  6. Kodi Nehemiya anakonza bwanji nchito yomanga cakuti adani a Isiraeli sanakwanitse kuiimitsa?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Nehemiya 1:4-6 ndi 2:1-20.

    Kodi Nehemiya apempha bwanji citsogozo ca Yehova? (Neh. 2:4, 5; Aroma 12:12; 1 Pet. 4:7)

  2. Ŵelenga Nehemiya 3:3-5.

    Kodi akulu ndi atumiki othandiza angaphunzile ciani pa kusiyana kwa Atekowa ndi ‘anthu ochuka amene anali pakati pao’? (Neh. 3:5, 27; 2 Ates. 3:7-10; 1 Pet. 5:5)

  3. Ŵelenga Nehemiya 4:1-23.

    1. Kodi n’ciani cinalimbikitsa Aisiraeli kupitiliza kumanga ngakhale kuti panali citsutso coopsa kwambili? (Neh. 4:6, 8, 9; Sal. 50:15; Yes. 65:13, 14)

    2. Kodi citsanzo ca Aisiraeli cimatilimbikitsa m’njila iti masiku ano?

  4. Ŵelenga Nehemiya 6:15.

    Mpanda wa Yerusalemu unamalizidwa pa miyezi iŵili cabe, kodi zimenezi zimaonetsa ciani ponena za mphamvu ya cikhulupililo? (Sal. 56:3, 4; Mat. 17:20; 19:26)

Nkhani 84

Mngelo Acezela Mariya

  1. Kodi mkazi amene ali pacithunzi-thunzi apa ndani?

  2. Kodi Gabrieli auza Mariya ciani?

  3. Kodi Gabrieli wafotokoza bwanji kwa Mariya kuti ngakhale kuti sanagonepo ndi mwamuna adzakhala ndi mwana?

  4. Kodi cacitika n’ciani pamene Mariya acezela Elizabeti m’bululu wake?

  5. Kodi Yosefe aganiza ciani pamene adziŵa kuti Mariya adzakhala ndi mwana, koma n’cifukwa ciani anasintha nzelu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Luka 1:26-56.

    1. Kodi lemba la Luka 1:35 lionetsa ciani ponena za kupanda ungwilo kulikonse kocokela kwa Adamu m’dzila la Mariya pamene moyo wa Mwana wa Mulungu unasamutsidwa kucokela kumwamba? (Hagai 2:11-13; Yoh. 6:69; Aheb. 7:26; 10:5)

    2. Kodi Yesu analandila bwanji ulemu ngakhale pamene anali asanabadwe? (Luka 1:41-43)

    3. Kodi n’citsanzo cabwino citi cimene Mariya anaonetsa kwa Akristu amene masiku ano amalandila mwai wapadela wautumiki? (Luka 1:38, 46-49; 17:10; Miy. 11:2)

  2. Ŵelenga Mateyu 1:18-25.

    Ngakhale kuti Yesu sanali kugwilitsila nchito dzina lakuti Emanueli, kodi zimene anacita monga munthu zinakwanilitsa bwanji tanthauzo la dzina limeneli? (Mat. 1:22, 23; Yoh. 14:8-10; Aheb. 1:1-3)

Nkhani 85

Yesu Abadwila mu Khola

  1. Kodi wakadziŵa kamwana kamene kali pacithunzi-thunzi apa, ndipo Mariya wakagoneka m’ciani?

  2. N’cifukwa ninji Yesu anabadwila mu khola mmene munali zinyama?

  3. Kodi amuna amene aloŵa mu khola pacithunzi-thunzi ndani, ndipo mngelo waauza ciani?

  4. N’cifukwa ciani Yesu ni wapadela?

  5. N’cifukwa ciani Yesu amachedwa mwana wa Mulungu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Luka 2:1-20.

    1. Kodi Kaisara Augusito anacita mbali yanji pokwanilitsa ulosi wonena za kubadwa kwa Yesu? (Luka 2:1-4; Mika 5:2)

    2. Kodi munthu angakhale bwanji mmodzi wa anthu amene amachedwa kuti “anthu amene iye amakondwela nao”? (Luka 2:14; Mat. 16:24; Yoh. 17:3; Mac. 3:19; Aheb. 11:6)

    3.     

Nkhani 86

Nyenyezi Itsogolela Amuna Akum’maŵa

  1. Kodi amuna amene ali pacithunzi-thunzi ndani, ndipo n’cifukwa ciani mmodzi asontha nyenyezi yowala?

  2. N’cifukwa ciani Mfumu Herode akalipa kwambili, ndipo acita ciani?

  3. Kodi nyenyezi yowala iwatsogolela kuti amuna amenewa, koma n’cifukwa ciani iwo anagwilitsila nchito njila ina pobwelela ku dziko lakwao?

  4. Kodi Herode anapeleka lamulo lakuti ciani, ndipo cifukwa ciani?

  5. Kodi Yehova auza Yosefe kucita ciani?

  6. Kodi ndani anacititsa kuti nyenyezi yatsopano iwale, ndipo n’cifukwa ciani?

Funso Loonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 2:1-23.

    Kodi Yesu anali wa msinkhu wanji ndiponso anali kukhala kuti pamene okhulupilila nyenyezi anabwela kudzamuona? (Mat. 2:1, 11, 16)

Nkhani 87

Yesu Wacicepele Ali mu Kacisi

  1. Kodi Yesu ni wamsinkhu wanji pacithunzi-thunzi apa, ndipo ali kuti?

  2. Kodi Yosefe amacita ciani ndi banja lake caka ciliconse?

  3. Atayenda kwa tsiku limodzi pobwelela kwao, n’cifukwa ciani Yosefe ndi Mariya abwelela ku Yerusalemu?

  4. Kodi ni kuti kumene Yosefe ndi Mariya apeza Yesu, ndipo ni cifukwa ciani anthu amene ali kumeneko adabwa?

  5. Kodi Yesu akamba ciani kwa Mariya amai ake?

  6. Kodi tingakhale bwanji monga Yesu pophunzila za Mulungu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Luka 2:41-52.

    1. Ngakhale kuti Cilamulo cinali kunena kuti amuna cabe ni amene ayenela kupezeka pa zikondwelelo za pacaka, kodi Yosefe ndi Mariya anaonetsa citsanzo canji cabwino kwa makolo masiku ano? (Luka 2:41; Deut. 16:16; 31:12; Miy. 22:6)

    2. Kodi Yesu anaonetsa bwanji citsanzo cabwino kwa acicepele masiku ano pankhani yomvela makolo? (Luka 2:51; Deut. 5:16; Miy. 23:22; Akol. 3:20)

  2. Ŵelenga Mateyu 13:53-56.

    Kodi abale a Yesu eni-eni anai amene amachulidwa m’Baibo ndani, ndipo aŵili anagwilitsidwa nchito bwanji mumpingo wacikhristu panthawi ina? (Mat. 13:55; Mac. 12:17; 15:6, 13; 21:18; Agal. 1:19; Yak. 1:1; Yuda 1)

Nkhani 88

Yohane Abatiza Yesu

  1. Kodi amuna aŵili amene ali pacithunzi-thunzi apa ndani?

  2. Kodi munthu amabatizika bwanji?

  3. Kodi Yohane abatiza anthu abwanji?

  4. Kodi Yesu apempha Yohane kuti am’batize pa cifukwa capadela citi?

  5. Kodi Mulungu aonetsa bwanji kuti wakondwela poona kuti Yesu wabatizika?

  6. Kodi n’ciani cicitika pamene Yesu apita kumalo a yekha kwa masiku 40?

  7. Kodi otsatila kapena ophunzila oyamba a Yesu anali ati, ndipo cozizwitsa cake coyamba cinali ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 3:13-17.

    Kodi Yesu anapeleka citsanzo canji ca ubatizo wa ophunzila ake? (Sal. 40:7, 8; Mat. 28:19, 20; Luka 3:21, 22)

  2. Ŵelenga Mateyu 4:1-11.

    Kodi kugwilitsila nchito Malemba mwaluso kwa Yesu kumatithandiza bwanji kuphunzila Baibo nthawi zonse? (Mat. 4:5-7; 2 Pet. 3:17, 18; 1 Yoh. 4:1)

  3. Ŵelenga Yohane 1:29-51.

    Kodi Yohane mbatizi anali kutsogolela ophunzila ake kwa ndani, ndipo tingatengele bwanji citsanzo cake masiku ano? (Yoh. 1:29, 35, 36; 3:30; Mat. 23:10)

  4. Ŵelenga Yohane 2:1-12.

    Kodi cozizwitsa coyamba ca Yesu cimaonetsa bwanji kuti Yehova samana atumiki Ake zinthu zabwino? (Yoh. 2:9, 10; Sal. 84:11; Yak. 1:17)

Nkhani 89

Yesu Ayeletsa Kacisi

  1. N’cifukwa ciani anthu agulitsa zinyama pakacisi?

  2. Kodi n’ciani cacititsa kuti Yesu akalipe?

  3. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi, kodi Yesu acita ciani? Ndipo auza anthu ogulitsa nkhunda kuti acite ciani?

  4. Pamene otsatila a Yesu aona zimene acita, kodi akumbukila ciani?

  5. Kodi Yesu apitila m’cigao citi paulendo wake wobwelela ku Galileya?

Funso loonjezela:

  1. Ŵelenga Yohane 2:13-25.

    Poona mmene Yesu anakalipilila anthu osintha ndalama pakacisi, kodi tiyenela kucita malonda pa Nyumba ya Ufumu? (Yoh. 2:15, 16; 1 Akor. 10:24, 31-33)

Nkhani 90

Yesu ali pa Citsime ndi Mkazi

  1. N’cifukwa ciani Yesu waima pacitsime ku Samariya, ndipo akamba ciani kwa mkaziyo?

  2. N’cifukwa ciani mkaziyu wadabwa, nanga Yesu amuuza ciani, ndipo n’cifukwa ciani?

  3. Kodi mkaziyu aganiza kuti Yesu akamba za madzi abwanji, koma kodi kweni-kweni atanthauza madzi ati?

  4. N’cifukwa ciani mkazi wadabwa kwambili kuona zimene Yesu adziŵa ponena za iye, ndipo Yesu anadziŵa bwanji zimenezi?

  5. Nanga tiphunzilapo ciani pankhani ya mkazi amene anali pacitsime?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yohane 4:5-43.

    1. Potengela citsanzo ca Yesu, kodi tiyenela kuwaona bwanji anthu a mtundu wina, kapena amene ali ndi cikhalidwe cosiyana ndi cathu? (Yoh. 4:9; 1 Akor. 9:22; 1 Tim. 2:3, 4; Tito 2:11)

    2. Kodi munthu amene wakhala wophunzila wa Yesu amapeza mapindu anji? (Yoh. 4:14; Yes. 58:11; 2 Akor. 4:16)

    3. Kodi tingaonetse bwanji kuyamikila monga mkazi wacisamariya uja, amene anali wofunitsitsa kuuza ena zimene anaphunzila? (Yoh. 4:7, 28; Mat. 6:33; Luka 10:40-42)

Nkhani 91

Yesu Aphunzitsa pa Phili

  1. Pacithunzi-thunzi apa, kodi Yesu ali kuti pamene aphunzitsa, ndipo ndani amene wakhala nao pafupi kwambili?

  2. Kodi maina a atumwi 12 ni ati?

  3. Kodi Ufumu umene Yesu alalikila ni uti?

  4. Kodi Yesu aphunzitsa anthu kupemphelela ciani?

  5. Kodi Yesu akamba ciani za mmene anthu ayenela kucitila zinthu ndi anzao?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 5:1-12.

    Kodi tingaonetse m’njila ziti kuti timazindikila zinthu zofunika zakuuzimu? (Mat. 5:3; Aroma 10:13-15; 1 Tim. 4:13, 15, 16)

  2. Ŵelenga Mateyu 5:21-26.

    Kodi lemba la Mateyu 5:23, 24 limaonetsa bwanji kuti unansi wathu ndi abale athu umakhudza unansi wathu ndi Yehova? (Mat. 6:14, 15; Sal. 133:1; Akol. 3:13; 1 Yoh. 4:20)

  3. Ŵelenga Mateyu 6:1-8.

    Kodi n’kudzilungamitsa kuti kumene Akristu ayenela kupewa? (Luka 18:11, 12; 1 Akor. 4:6, 7; 2 Akor. 9:7)

  4. Ŵelenga Mateyu 6:25-34.

    Kodi Yesu anaphunzitsa ciani pankhani ya kudalila Yehova pa zofunika zakuthupi? (Ex. 16:4; Ps. 37:25; Phil. 4:6)

  5. Ŵelenga Mateyu 7:1-11.

    Kodi fanizo lomveka bwino lopezeka pa Mateyu 7:5 litiphunzitsa ciani? (Miy. 26:12; Aroma 2:1; 14:10; Yak. 4:11, 12)

Nkhani 92

Yesu Aukitsa Akufa

  1. Kodi atate a mtsikana amene ali pacithunzi-thunzi apa ndani, ndipo n’cifukwa ciani mwamunayu ndi mkazi wake ali ndi nkhawa kwambili?

  2. Kodi Yairo acita ciani pamene apeza Yesu?

  3. Kodi n’ciani cicitika pamene Yesu apita kunyumba kwa Yairo, ndipo ni uthenga wanji umene Yairo alandila pamene akali m’njila?

  4. N’cifukwa ciani anthu amene ali m’nyumba ya Yairo aseka Yesu?

  5. Pamene Yesu atenga atumwi ake atatu ndi atate ndi amai a mtsikana mu cipinda, kodi iye acita ciani?

  6. Ndani wina amene Yesu anamuukitsa ku imfa, ndipo zimenezi zionetsa ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Luka 8:40-56.

    Kodi Yesu anaonetsa bwanji cifundo ndi kulolela kwa mkazi amene anali ndi nthenda yotaya magazi, ndipo akulu ampingo masiku ano aphunzilapo ciani pa zimenezi? (Luka 8:43, 44, 47, 48; Lev. 15:25-27; Mat. 9:12, 13; Akol. 3:12-14)

  2. Ŵelenga Luka 7:11-17.

    N’cifukwa ciani anthu amene anataikilidwa okondedwa ao mu imfa angapeze citonthozo cacikulu, poona mmene Yesu anayankhila mkazi wamasiye wa ku Naini? (Luka 7:13; 2 Akor. 1:3, 4; Aheb. 4:15)

  3. Ŵelenga Yohane 11:17-44.

    Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti sikulakwa kulila pamene wokondedwa wathu wamwalila? (Yoh. 11:33-36, 38; 2 Sam. 18:33; 19:1-4)

Nkhani 93

Yesu Adyetsa Anthu Ambili

  1. Kodi n’cinthu coipa cabwanji cimene cacitikila Yohane Mbatizi, ndipo Yesu akumvela bwanji?

  2. Kodi Yesu adyetsa bwanji anthu amene amutsatila, ndipo patsala cakudya coculuka bwanji?

  3. N’cifukwa ciani ophunzila acita mantha usiku, ndipo n’ciani cicitikila Petulo?

  4. Kodi Yesu adyetsa bwanji kaciŵili anthu masauzande?

  5. N’cifukwa ciani cidzakhala cokondweletsa pamene Yesu adzayamba kulamulila dziko lapansi monga Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 14:1-32.

    1. Kodi nkhani yopezeka pa Mateyu 14:23-32 imationetsa ciani ponena za umunthu wa Petulo?

    2. Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti m’kupita kwa nthawi Petulo anasintha mtima wake wothamangila kucita zinthu? (Mat. 14:27-30; Yoh. 18:10; 21:7; Mac. 2:14, 37-40; 1 Pet. 5:6, 10)

  2. Ŵelenga Mateyu 15:29-38.

    Kodi Yesu anaonetsa bwanji ulemu pazinthu zakuthupi zimene analandila kwa Atate wake? (Mat. 15:37; Yoh. 6:12; Akol. 3:15)

  3. Ŵelenga Yohane 6:1-21.

    Kodi Akristu masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca Yesu pankhani yolemekeza boma? (Yoh. 6:15; Mat. 22:21; Aroma 12:2; 13:1-4)

Nkhani 94

Yesu Amakonda Tuŵana

  1. Kodi atumwi akangana ciani m’njila pobwelako ku ulendo wao wautali?

  2. N’cifukwa ciani Yesu aitana kamwana ndi kukaimika pakati pa atumwi?

  3. Kodi ni m’njila iti imene atumwi ayenela kuphunzila kukhala ngati ana?

  4. Patapita miyezi yocepa, kodi Yesu aonetsa bwanji kuti amakonda ana?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 18:1-4.

    N’cifukwa ciani Yesu agwilitsila nchito mafunso pophunzitsa? (Mat. 13:34, 36; Maliko 4:33, 34)

  2. Ŵelenga Mateyu 19:13-15.

    Kodi ni makhalidwe ati a ana amene tiyenela kutengela kuti tikalandile madalitso a Ufumu (Sal. 25:9; 138:6; 1 Akor. 14:20)

  3. Ŵelenga Maliko 9:33-37.

    Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzila ake ciani pankhani ya kufuna malo apamwamba? (Maliko 9:35; Mat. 20:25, 26; Agal. 6:3; Afil. 2:5-8)

  4. Ŵelenga Maliko 10:13-16.

    Kodi Yesu anali wofikilika bwanji, ndipo akulu mumpingo angaphunzile ciani pacitsanzo cake? (Maliko 6:30-34; Afil. 2:1-4; 1 Tim. 4:12)

Nkhani 95

Mmene Yesu Amaphunzitsila

  1. Kodi munthu wina afunsa Yesu funso lanji, ndipo n’cifukwa ciani?

  2. Kodi Yesu nthawi zina pophunzitsa agwilitsila nchito ciani, ndipo taphunzila ciani ponena za Ayuda ndi Asamariya?

  3. Mu fanizo limene Yesu wafotokoza, kodi n’ciani cimene cicitikila Myuda amene ayenda pamseu wopita ku Yeriko?

  4. Nanga n’ciani cicitika pamene wansembe waciyuda ndi Mlevi ayenda pamseu umenewu?

  5. Pacithunzi-thunzi apa, kodi ndani amene athandiza Myuda amene wavulala?

  6. Pamene Yesu atsiliza kufotokoza fanizo, kodi afunsa funso lanji, ndipo munthuyu ayankha kuti bwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Luka 10:25-37.

    1. M’malo mopeleka yankho lacindunji, kodi Yesu anathandiza bwanji munthu wodziŵa Cilamulo kuganiza pankhaniyo? (Luka 10:26; Mat. 16:13-16)

    2. Kodi Yesu anagwilitsila nchito bwanji mafanizo pothandiza omvela ake amene anali ndi maganizo atsankho? (Luka 10:36, 37; 18:9-14; Tito 1:9)

Nkhani 96

Yesu Acilitsa Odwala

  1. Kodi Yesu acita ciani pamene ayenda-ayenda m’dziko lonse?

  2. Patapita zaka zitatu kucokela pamene Yesu anabatizika, kodi auza ciani atumwi ake?

  3. Kodi anthu ali pacithunzi-thunzi apa ndani, ndipo Yesu amucitila ciani mkazi uyu?

  4. N’cifukwa ciani atsogoleli acipembedzo acita manyazi ndi mmene Yesu wayankhila pamene anali kumutsutsa?

  5. Pamene Yesu ndi atumwi ake ali pafupi ndi Yeriko, kodi Yesu awacitila ciani anthu akhungu aŵili opempha-pempha?

  6. Kodi n’cifukwa ciani Yesu acita zozizwitsa?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 15:30, 31.

    Kodi mphamvu za Yehova zionekela bwanji kupyolela mwa Yesu, ndipo zimenezi ziyenela kukhudza bwanji mmene timamvelela ndi zimene Yehova walonjeza mu dziko latsopano? (Sal. 37:29; Yes. 33:24)

  2. Ŵelenga Luka 13:10-17.

    Kodi pamene Yesu anacita zina mwa zozizwitsa zake zazikulu patsiku la Sabata, zimaonetsa bwanji mpumulo umene adzabweletsa kwa anthu mu ulamulilo wake wa zaka 1000? (Luka 13:10-13; Sal. 46:9; Mat. 12:8; Akol. 2:16, 17; Chiv. 21:1-4)

  3. Ŵelenga Mateyu 20:29-34.

    Kodi nkhani imeneyi ionetsa bwanji kuti Yesu anali kupatula nthawi yothandiza anthu, ngakhale kuti anali wotangwanika kwambili, ndipo tingaphunzilepo ciani pa zimenezi? (Deut. 15:7; Yak. 2:15, 16; 1 Yoh. 3:17)

Nkhani 97

Yesu Abwela Monga Mfumu

  1. Pamene Yesu afika m’mudzi waung’ono umene uli pafupi ndi Yerusalemu, kodi auza ophunzila ake kucita ciani?

  2. Monga mmene tionela pacithunzi-thunzi apa, n’ciani cicitika pamene Yesu afika pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu?

  3. Kodi ana ang’ono acita ciani pamene aona Yesu acilitsa anthu akhungu ndi olemala?

  4. Kodi Yesu awauza ciani ansembe amene akalipa?

  5. Kodi tingakhale bwanji monga ana amene atamanda Yesu?

  6. Kodi ophunzila afuna kudziŵa ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 21:1-17.

    1. Kodi kuloŵa kwa Yesu monga Mfumu mu Yerusalemu kusiyana bwanji ndi kwa akazembe a m’nthawi ya Aroma? (Mat. 21:4, 5; Zek. 9:9; Afil. 2:5-8; Akol. 2:15)

    2. Kodi ni phunzilo lanji limene ana angaphunzile kwa ana aciisiraeli amene anawagwila mau a pa lemba la Salimo 118, pamene Yesu anali kuloŵa m’kacisi? (Mat. 21:9, 15; Sal. 118:25, 26; 2 Tim. 3:15; 2 Pet. 3:18)

  2. Ŵelenga Yohane 12:12-16.

    Kodi kugwilitsila nchito masamba a kanjedza kumene anthu anacita potamanda Yesu kumaimila ciani? (Yoh. 12:13; Afil. 2:10; Chiv. 7:9, 10)

Nkhani 98

Pa Phili la Maolivi

  1. Pacithunzi-thunzi apa, kodi Yesu ni uti, ndipo awa amene ali nao ndani?

  2. Kodi ansembe anafuna kucita ciani kwa Yesu pamene anali m’kacisi, ndipo iye anati ciani kwa io?

  3. Kodi atumwi amufunsa ciani Yesu?

  4. N’cifukwa ciani Yesu auza atumwi ake zinthu zina zimene zidzacitika padziko lapansi pamene iye adzalamulila monga Mfumu kumwamba?

  5. Kodi Yesu anati cidzacitika coyamba n’ciani akalibe kucotsa zoipa zonse padziko lapansi?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 23:1-39.

    1. Ngakhale kuti malemba amaonetsa kuti kugwilitsila nchito maina aulemu kungakhale koyenela, kodi mau a Yesu apa Mateyu 23:8-11 amaonetsa ciani ponena za kugwilitsila nchito maina okweza anthu mumpingo wacikristu? (Mac. 26:25; Aroma 13:7; 1 Pet. 2:13, 14)

    2. Kodi Afalisi anagwilitsila nchito ciani poletsa anthu kukhala Akristu, nanga atsogoleli acipembedzo masiku ano amagwilitsila nchito bwanji njila imeneyi? (Mat. 23:13; Luka 11:52; Yoh. 9:22; 12:42; 1 Ates. 2:16)

  2. Ŵelenga Mateyu 24:1-14.

    1. Kodi lemba la Mateyu 24:13 limagogomeza bwanji kuti kupilila n’kofunika?

    2. Kodi mau akuti “mapeto” opezeka pa Mateyu 24:13 amatanthauza ciani? (Mat. 16:27; Aroma 14:10-12; 2 Akor. 5:10)

  3. Ŵelenga Maliko 13:3-10.

    Kodi ndi mau ati pa Maliko 13:10 amene aonetsa kuti kulalikila uthenga wabwino n’kofunika kwambili, ndipo mau a Yesu amenewo ayenela kutikhudza bwanji? (Aroma 13:11, 12; 1 Akor. 7:29-31; 2 Tim. 4:2)

Nkhani 99

M’cipinda Capamwamba

  1. Monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa, n’cifukwa ciani Yesu ndi atumwi ake 12 ali m’cipinda capamwamba cacikulu?

  2. Kodi mwamuna uyu amene coka ndani, ndipo ayenda kukacita ciani?

  3. Pamene Yesu anatsiliza kucita Paska, kodi anayamba phwando lapadela liti?

  4. Kodi Paska inali kukumbutsa Aisiraeli cocitika citi, ndipo phwando lapadela limeneli likumbutsa otsatila a Yesu ciani?

  5. Pambuyo pa Mgonelo wa Ambuye, kodi Yesu auza otsatila ake ciani, ndipo io acita ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 26:14-30.

    1. Kodi lemba la Mateyu 26:15 limaonetsa bwanji kuti Yudasi anacitila dala kupeleka Yesu?

    2. Kodi magazi amene Yesu anakhetsa amakwanilitsa zolinga ziŵili ziti? (Mat. 26:27, 28; Yer. 31:31-33; Aef. 1:7; Aheb. 9:19, 20)

  2. Ŵelenga Luka 22:1-39.

    N’cifukwa ciani tinganene kuti Satana analoŵa mwa Yudasi? (Luka 22:3; Yoh. 13:2; Mac. 1:24, 25)

  3. Ŵelenga Yohane 13:1-20.

    1. Malinga ndi nkhani ya pa Yohane 13:2, kodi Yudasi angapatsidwe mlandu pa zimene anacita, ndipo ni phunzilo labwanji limene atumiki a Mulungu angatengepo pamenepa? (Gen. 4:7; 2 Akor. 2:11; Agal. 6:1; Yak. 1:13, 14)

    2. Kodi n’citsanzo camphamvu citi cimene Yesu anapeleka? (Yoh. 13:15; Mat. 23:11; 1 Pet. 2:21)

  4. Ŵelenga Yohane 17:1-26.

    Kodi Yesu anapemphela kuti otsatila ake akhale “amodzi” m’lingalilo lanji? (Yoh. 17:11, 21-23; Aroma 13:8; 14:19; Akol. 3:14)

Nkhani 100

Yesu Ali m’Munda

  1. Kodi Yesu ndi atumwi ake ayenda kuti pamene acoka m’cipinda capamwamba, ndipo awauza kucita ciani?

  2. Kodi Yesu apeza ciani pamene abwelela pamene pali atumwi ake, ndipo zimenezi zicitika kangati?

  3. Ndani amene aloŵa m’mundamo, ndipo Yudasi Isikariyoti acita ciani, monga mmene tionela pacithunzi-thunzi?

  4. N’cifukwa ciani Yudasi apsompsona Yesu, ndipo Petulo acita ciani?

  5. Kodi Yesu auza Petulo ciani, koma n’cifukwa ciani Yesu sapempha Mulungu kutumiza angelo?

Mfunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 26:36-56.

    1. N’cifukwa ciani njila imene Yesu anapelekela uphungu kwa ophunzila ake ili citsanzo cabwino kwa akulu masiku ano? (Mat. 20:25-28; 26:40, 41; Agal. 5:17; Aef. 4:29, 31, 32)

    2. Kodi Yesu amaona bwanji kugwilitsila nchito zida tikakangana ndi anzathu? (Mat. 26:52; Luka 6:27, 28; Yoh. 18:36)

  2. Ŵelenga Luka 22:39-53.

    Pamene mngelo anaonekela kwa Yesu kuti am’limbikitse m’munda wa Getsemane, kodi zimenezi zinaonetsa kuti cikhulupililo ca Yesu sicinali colimba? Fotokoza. (Luka 22:41-43; Yes. 49:8; Mat. 4:10, 11; Aheb. 5:7)

  3. Ŵelenga Yohane 18:1-12.

    Kodi Yesu anachinjiliza bwanji ophunzila ake kwa adani ake, ndipo tiphunzilapo ciani pa citsanzo cimeneci? (Yoh. 10:11, 12; 18:1, 6-9; Aheb. 13:6; Yak. 2:25)

Nkhani 101

Yesu Aphedwa

  1. Ndani kweni-kweni amene wacititsa kuti Yesu aphedwe?

  2. Kodi atumwi acita ciani pamene Yesu atengedwa ndi atsogoleli acipembedzo?

  3. N’ciani cicitika kunyumba kwa Kayafa, mkulu wansembe?

  4. N’cifukwa ciani Petulo acokapo ndi kuyamba kulila?

  5. Pamene Yesu abwezedwa kwa Pilato, kodi ansembe afuula kuti ciani?

  6. N’ciani cicitika kwa Yesu kuciyambi kwa masana pa Cisanu, ndipo ni lonjezo labwanji limene apeleka kwa munthu woipa amene wapacikidwa pamtengo pafupi naye?

  7. Kodi Paladaiso imene Yesu anakamba idzakhala kuti?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 26:57-75.

    Kodi ziwalo za khoti yalikulu ya Ayuda zinaonetsa bwanji kuti mitima yao inali yoipa? (Mat. 26:59, 67, 68)

  2. Ŵelenga Mateyu 27:1-50.

    N’cifukwa ciani tingakambe kuti cisoni cimene Yudasi anamvela sicinali ceni-ceni? (Mat. 27:3, 4; Maliko 3:29; 14:21; 2 Akor. 7:10, 11)

  3. Ŵelenga Luka 22:54-71.

    Kodi titengapo phunzilo lanji tikaona mmene Petulo anakanila Yesu usiku umene anapatsidwa mlandu ndi kumangidwa? (Luka 22:60-62; Mat. 26:31-35; 1 Akor. 10:12)

  4. Ŵelenga Luka 23:1-49.

    Kodi Yesu anacita bwanji pamene anam’citila zinthu mopanda cilungamo, ndipo tiphunzilapo ciani? (Luka 23:33, 34; Aroma 12:17-19; 1 Pet. 2:23)

  5. Ŵelenga Yohane 18:12-40.

    Ngakhale kuti Petulo anafooka kwa kanthawi cifukwa coopa anthu, analimbanso ndi kukhala mtumwi wocita bwino. Kodi zimenezi zimationetsa ciani? (Yoh. 18:25-27; 1 Akor. 4:2; 1 Pet. 3:14, 15; 5:8, 9)

  6. Ŵelenga Yohane 19:1-30.

    1. Kodi n’kaonedwe koyenela kati ka zinthu zakuthupi kamene Yesu anali nako? (Yoh. 2:1, 2, 9, 10; 19:23, 24; Mat. 6:31, 32; 8:20)

    2. Kodi mau amene Yesu anakamba pakufa anaonetsa bwanji kuti anapambana pankhani ya kucilikiza ulamulilo wa Yehova? (Yoh. 16:33; 19:30; 2 Pet. 3:14; 1 Yoh. 5:4)

Nkhani 102

Yesu Ali Moyo

  1. Kodi Mkazi amene ali pacithunzi-thunzi ndani, nanga amuna aŵili awa ndani, ndipo kumalo kumene ali n’kuti?

  2. N’cifukwa ciani Pilato auza ansembe kuti atumize asilikali kuti akalonde manda a Yesu?

  3. Kodi mngelo acita ciani m’mamawa patsiku lacitatu kucokela pamene Yesu anamwalila, koma kodi ansembe acita ciani?

  4. N’cifukwa ciani akazi adabwa pamene afika pa manda a Yesu?

  5. N’cifukwa ciani Petulo ndi Yohane athamangila kumanda a Yesu, ndipo apeze ciani kumeneko?

  6. N’ciani cinacitikila thupi la Yesu, koma iye acita ciani kuti aonetse ophunzila ake kuti ali moyo?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Mateyu 27:62-66 ndi 28:1-15.

    Pamene Yesu anaukitsidwa, kodi akulu a ansembe, Afalisi ndi amuna akulu anacimwila bwanji mzimu woyela? (Mat. 12:24, 31, 32; 28:11-15)

  2. Ŵelenga Luka 24:1-12.

    Kodi nkhani ya kuukitsidwa kwa Yesu, ionetsa bwanji kuti Yehova amaona akazi kukhala mboni zokhulupilika? (Luka 24:4, 9, 10; Mat. 28:1-7)

  3. Ŵelenga Yohane 20:1-12.

    Lemba la Yohane 20:8, 9 limatithandiza bwanji kuti kuleza mtima n’kofunika ngati sitimvetsetsa kukwanilitsika kwa ulosi wa m’Baibo? (Miy. 4:18; Mat. 17:22, 23; Luka 24:5-8; Yoh. 16:12)

Nkhani 103

Aloŵa m’Cipinda Cokhoma

  1. Kodi Mariya akuti ciani kwa mwamuna amene iye aganiza kuti ni wosamalila munda, koma n’ciani cim’thandiza kudziŵa kuti mwamunayo kweni-kweni ni Yesu?

  2. Kodi n’ciani cicitika kwa ophunzila aŵili amene ali paulendo wopita ku mudzi wa Emau?

  3. Kodi n’cinthu cokodweletsa cabwanji cimene cicitika pamene ophunzila aŵili auza atumwi kuti aona Yesu?

  4. Kodi Yesu aonekela kangati kwa otsatila ake?

  5. Kodi Tomasi akuti bwanji pamene amvela kuti ophunzila aona Ambuye, koma n’ciani cicitika patapita masiku 8?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yohane 20:11-29.

    Pa lemba la Yohane 20:23, kodi Yesu anali kukamba kuti anthu ni ololedwa kukhululukila macimo? Fotokoza. (Sal. 49:2, 7; Yes. 55:7; 1 Tim. 2:5, 6; 1 Yoh. 2:1, 2)

  2. Ŵelenga Luka 24:13-43.

    Kodi tingakonzekele bwanji m’mitima yathu kulandila coonadi ca m’Baibo? (Luka 24:32, 33; Ezara 7:10; Mat. 5:3; Mac. 16:14; Ahe. 5:11-14)

Nkhani 104

Yesu Abwelela Kumwamba

  1. Kodi ni ophunzila angati amene aona Yesu panthawi imodzi, ndipo awauza ciani?

  2. Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani, ndipo zinthu zidzakhala bwanji padziko lapansi pamene Yesu adzalamulila monga Mfumu kwa zaka 1000?

  3. Yesu wakhala akuonekela kwa ophunzila ake kwa masiku angati, koma kodi iyi tsopano ni nthawi yakuti iye acite ciani?

  4. Kodi Yesu auza ciani ophunzila ake atatsala pang’ono kucoka?

  5. Kodi n’ciani cicitika pacithunzi-thunzi ici, ndipo Yesu abisika bwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga 1 Akorinto 15:3-8.

    N’cifukwa ciani mtumwi Paulo akamba mwacidalilo za kuuka kwa Yesu, ndipo Akristu masiku ano angakambe mwacidalilo za ciani? (1 Ako. 15:4, 7, 8; Yes. 2:2, 3; Mat. 24:14; 2 Tim. 3:1-5)

  2. Ŵelenga Machitidwe 1:1-11.

    Kodi kulalikidwa kwa uthenga wabwino kunafalikila bwanji, mogwilizana ndi ulosi wa Machitidwe 1:8? (Mac. 6:7; 9:31; 11:19-21; Akol. 1:23)

Nkhani 105

Ayembekezela mu Yerusalemu

  1. Malinga ndi mmene cithunzi-thunzi cionetsela, kodi n’ciani cicitika kwa otsatila a Yesu amene akhala akuyembekeza mu Yerusalemu?

  2. Kodi alendo amene abwela ku Yerusalemu aona ciani codabwitsa?

  3. Kodi Petulo afotokoza ciani kwa anthu?

  4. Kodi anthu amvela bwanji pambuyo pomvetsela kwa Petulo, ndipo awauza kucita ciani?

  5. Ni anthu angati amene anabatizika patsiku la Pentekosite, mu 33 C.E.?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 2:1-47.

    1. Kodi mau a Petulo opezeka pa Machitidwe 2:23, 36 amaonetsa bwanji kuti mtundu wonse wa Ayuda unali ndi mlandu pakuphedwa kwa Yesu? (1 Ates. 2:14, 15)

    2. Kodi Petulo anaonetsa bwanji citsanzo cabwino cogwilitsila nchito Malemba pokambitsilana? (Mac. 2:16, 17, 29, 31, 36, 39; Akol. 4:6)

    3. Kodi Petulo anagwilitsila nchito bwanji ‘makiyi oyamba a ufumu wakumwamba’ amene Yesu analonjeza kum’patsa? (Mac. 2:14, 22-24, 37, 38; Mat. 16:19)

Nkhani 106

Awacotsa m’Ndende

  1. Kodi n’ciani cicitika kwa Petulo ndi Yohane tsiku lina, nthawi ya kumasana pamene apita ku kacisi?

  2. Kodi Petulo akamba ciani kwa munthu wolemala, ndipo Petulo am’patsa ciani cimene cili camtengo wapamwamba kupambana ndalama?

  3. N’cifukwa ciani atsogoleli acipembedzo ni okalipa, ndipo acita ciani kwa Petulo ndi Yohane?

  4. Kodi Petulo auza ciani atsogoleli acipembedzo, ndipo io apatsa atumwiwo cenjezo lakuti ciani?

  5. N’cifukwa ciani atsogoleli acipembedzo acita nsanje? Koma cicitika n’ciani pamene atumwi anaponyedwa m’ndende kaciŵili?

  6. Kodi atumwi ayankha bwanji pamene anawabweletsa mu holo ya Khoti Yaikulu ya Ayuda?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 3:1-10.

    Ngakhale kuti masiku ano tilibe mphamvu yocita zozizwitsa, kodi mau a Petulo opezeka pa Machitidwe 3:6 amatithandiza bwanji kuona ubwino wa uthenga wa Ufumu? (Yoh. 17:3; 2 Akor. 5:18-20; Afil. 3:8)

  2. Ŵelenga Machitidwe 4:1-31.

    Pamene tikumana ndi citsutso muulaliki, kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Akristu anzathu a m’zaka za zana loyamba? (Mac. 4:29, 31; Aef. 6:18-20; 1 Ates. 2:2)

  3. Ŵelenga Machitidwe 5:17-42.

    Kodi anthu amene si Mboni masiku ano ndi m’nthawi yakale, aonetsa bwanji mtima wololela panchito yolalikila? (Mac. 5:34-39)

Nkhani 107

Stefano Aponyedwa Miyala

  1. Kodi Stefano ndani, ndipo Mulungu am’thandiza kucita ciani?

  2. Kodi Stefano akamba ciani cimene cakalipitsa kwambili atsogoleli acipembedzo?

  3. Pamene anthu ena akokela Stefano kunja kwa mzinda, kodi am’cita ciani?

  4. Pacithunzi-thunzi apa, kodi wacinyamata amene waimilila pafupi ndi zovala ndani?

  5. Kodi Stefano akalibe kufa, apempha ciani kwa Yehova?

  6. Kuti titsatile citsanzo ca Stefano, kodi tiyenela kucita ciani ngati munthu wina waticitila coipa?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 6:8-15.

    Kodi atsogoleli acipembedzo amagwilitsila nchito macenjela ati pofuna kulepheletsa nchito yolalikila ya Mboni za Yehova? (Mac. 6:9, 11, 13)

  2. Ŵelenga Machitidwe 7:1-60.

    1. N’ciani cinathandiza Stefano kukhalila kumbuyo molimba mtima uthenga wabwino pamaso pa Khoti Yaikulu ya Ayuda? Ndipo tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cake? (Mac. 7:51-53; Aroma 15:4; 2 Tim. 3:14-17; 1 Pet. 3:15)

    2. Kodi anthu amene amatsutsa nchito yathu yolalikila tiyenela kuwaona bwanji? (Mac. 7:58-60; Mat. 5:44; Luka 23:33, 34)

Nkhani 108

Paulendo Wopita ku Damasiko

  1. Kodi Saulo acita ciani pambuyo pakuti Stefano waphedwa?

  2. Pamene Saulo ali paulendo wopita ku Damasiko, kodi pacitika cinthu codabwitsa cabwanji?

  3. Kodi Yesu auza Saulo kucita ciani?

  4. Kodi Yesu apatsa Hananiya malangizo anji, ndipo Saulo ayambanso bwanji kuona?

  5. Kodi Saulo ayamba kuchedwa ndi dzina liti, ndipo agwilitsilidwa nchito bwanji?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 8:1-4.

    Kodi cizunzo cimene cinagwela mpingo wacikristu umene unali watsopano cinathandiza bwanji kufalitsa cikhulupililo cacikristu, ndipo zimenezo zicitikanso bwanji masiku ano? (Mac. 8:4; Yes. 54:17)

  2. Ŵelenga Machitidwe 9:1-20.

    Kodi ni nchito ya mbali zitatu iti ya Saulo imene Yesu anavumbula? (Mac. 9:15; 13:5; 26:1; 27:24; Aroma 11:13)

  3. Ŵelenga Machitidwe 22:6-16.

    Kodi tingakhale bwanji monga Hananiya, ndipo n’cifukwa ciani zimenezi n’zofunika? (Mac. 22:12; 1 Tim. 3:7; 1 Pet. 1:14-16; 2:12)

  4. Ŵelenga Machitidwe 26:8-20.

    Kodi kutembenuka kwa Saulo kukhala Mkristu kumalimbikitsa bwanji anthu amene amuna awo, kapena akazi ao, si Akristu? (Mac. 26:11; 1 Tim. 1:14-16; 2 Tim. 4:2; 1 Pet. 3:1-3)

Nkhani 109

Petulo Acezela Korneliyo

  1. Kodi mwamuna amene wagwada pacithunzi-thunzi ndani?

  2. Kodi mngelo akamba ciani kwa Korneliyo?

  3. Kodi Mulungu acititsa Petulo kuona ciani pamene ali pamtenje wa nyumba ya Simiyoni ku Yopa?

  4. N’cifukwa ciani Petulo auza Korneliyo kuti sayenela kugwada ndi kum’lambila?

  5. N’cifukwa ciani ophunzila aciyuda amene ali ndi Petulo adabwa kwambili?

  6. Kodi ni phunzilo lofunika liti limene titengapo paulendo wa Petulo wokacezela Korneliyo?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 10:1-48.

    Kodi mau a Petulo opezeka pa Machitidwe 10:42 aonetsa ciani ponena za nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu? (Mat. 28:19; Maliko 13:10; Mac. 1:8)

  2. Ŵelenga Machitidwe 11:1-18.

    Kodi Petulo anaonetsa maganizo ati pamene colinga ca Yehova cokhudza anthu amitundu ina cinadziŵika, ndipo tingatsatile bwanji citsanzo cake? (Mac. 11:17, 18; 2 Akor. 10:5; Aef. 5:17)

Nkhani 110

Timoteyo—Mthandizi Watsopano wa Paulo

  1. Kodi mwamuna wacinyamata ali pacithunzi-thunzi ndani, akhala kuti, ndipo dzina la amai ndi ambuye ake ndani?

  2. Kodi Timoteyo ayankha kuti ciani, pamene Paulo am’funsa ngati angafune kupita pamodzi ndi Sila ndi Paulo, m’nchito yolalikila anthu a kumadela akutali?

  3. Kodi n’kuti kumene ophunzila a Yesu ayamba achedwa kuti Akristu?

  4. Pamene Paulo, Sila ndi Timoteyo acoka ku Lustra, kodi acezela mizinda ina iti?

  5. Kodi Timoteyo athandiza bwanji Paulo, ndipo ni mafunso ati amene acicepele ayenela kudzifunsa masiku ano?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 9:19-30.

    Kodi mtumwi Paulo anaonetsa bwanji nzelu pamene anakumana ndi citsutso polalikila uthenga wabwino? (Mac. 9:22-25, 29, 30; Mat. 10:16)

  2. Ŵelenga Machitidwe 11:19-26.

    Kodi nkhani ya pa Machitidwe 11:19-21, 26, ionetsa bwanji kuti mzimu wa Yehova umatsogolela nchito yolalikila?

  3. Ŵelenga Machitidwe 13:13-16, 42-52.

    Kodi lemba la Machitidwe 13:51, 52, lionetsa bwanji kuti ophunzila sanalole kuti citsutso ciwalefule? (Mat. 10:14; Mac. 18:6; 1 Pet. 4:14)

  4. Ŵelenga Machitidwe 14:1-6, 19-28.

    Kodi mau akuti “anawapeleka kwa Yehova” amatithandiza bwanji kuthetsa nkhawa iliyonse pamene tithandiza atsopano? (Mac. 14:21-23; 20:32; Yoh. 6:44)

  5. Ŵelenga Machitidwe 16:1-5.

    Timoteyo mofunitsitsa anavomela kuti adulidwe, kodi zimenezi zigogomeza bwanji kufunika kwa “kucita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino”? (Mac. 16:3; 1 Akor. 9:23; 1 Ates. 2:8)

  6. Ŵelenga Macitidwe 18:1-11, 18-22.

    Kodi lemba la Machitidwe 18:9, 10 limaonetsa ciani cosonyeza kuti Yesu ndiye amatsogolela nchito yolalikila, ndipo zimenezi zitipatsa cidalilo cabwanji masiku ano? (Mat. 28:20)

Nkhani 111

Mnyamata Amene Anagona Tulo

  1. Pacithunzi-thunzi apa, kodi mnyamata amene wagona pansi ndani, ndipo n’ciani cacitika kwa iye?

  2. Kodi Paulo acita ciani pamene aona kuti mnyamatayu wamwalila?

  3. Kodi Paulo, Timoteyo ndi ena amene ali nao paulendo apita kuti, ndipo ni’iani cicitika pamene aiima ku Melito?

  4. Kodi n’cenjezo lanji limene mneneli Agabo apatsa Paulo, ndipo zicitika bwanji monga mmene mneneliyo anakambila?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 20:7-38.

    1. Malinga ndi mau a Paulo opezeka pa Machitiidwe 20:26, 27, kodi tingakhale bwanji ‘oyela pa mlandu wa magazi a anthu onse’? (Ezek. 33:8; Mac. 18:6, 7)

    2. N’cifukwa ciani akulu ayenela ‘kugwila mwamphamvu mau okhulupilika’ pamene aphunzitsa? (Mac. 20:17, 29, 30; Tito 1:7-9; 2 Tim. 1:13)

  2. Ŵelenga Machitidwe 26:24-32.

    Kodi Paulo anagwilitsila nchito bwanji unzika wake waciroma kucita nchito yolalikila imene anapatsidwa ndi Yesu? (Mac. 9:15; 16:37, 38; 25:11, 12; 26:32; Luka 21:12, 13)

Nkhani 112

Boti Ionongeka Pacisumbu

  1. Kodi n’ciani cicitikila boti imene Paulo alimo pamene ipitila pafupi ndi cisumbu ca Kerete?

  2. Kodi Paulo awauza ciani anthu amene ali nao m’boti?

  3. Kodi boti ipwanyika bwanji ndi kukhala zidutswa-zidutswa?

  4. Kodi msilikali woŵayang’anila aŵapatsa malangizo akuti ciani, ndipo ni anthu angati amene apulumuka ndi kufika kumtunda?

  5. Kodi io afika pacisumbu citi, ndipo pamene cimphepho cileka kuomba, n’ciani cicitika kwa Paulo?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 27:1-44

    Kodi cidalilo cathu cakuti Baibo ni yoona cimalimbikitsidwa bwanji pamene tiŵelenga nkhani ya ulendo wa Paulo wopita ku Roma? (Mac. 27:16-19, 27-32; Luka 1:3; 2 Tim. 3:16, 17)

  2. Ŵelenga Machitidwe 28:1-14.

    Ngati anthu osadziŵa Mulungu a ku Melita, anaonetsa mtumwi Paulo ndi anzake amene anali naye pangozi “kukoma mtima kwa umunthu kwapadela,” kodi Akristu ayenela kuonetsa ciani, ndipo maka-maka mwa njila iti? (Mac. 28:1, 2; Aheb. 13:1, 2; 1 Pet. 4:9)

Nkhani 113

Paulo Ali ku Roma

  1. Kodi Paulo alalikila kwa ndani pamene ali m’ndende ku Roma?

  2. Pacithunzi-thunzi, kodi mlendo uyu amene ali pathebulo ndani, ndipo acitila Paulo ciani?

  3. Kodi Epafurodito ndani, ndipo atenga ciani pamene abwelela ku Filipi?

  4. N’cifukwa ciani Paulo alembela Filimoni kalata, mnzake wa pamtima?

  5. Kodi Paulo acita ciani pamene amasulidwa, ndipo n’ciani cimucitikila pambuyo pake?

  6. Kodi Yehova anagwilitsila nchito ndani kulemba mabuku otsilizila a Baibo, ndipo buku la Chivumbulutso limafotokoza za ciani?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Machitidwe 28:16-31 ndi Afilipi 1:13.

    Kodi Paulo anagwilitsila nchito bwanji nthawi yake pamene anali m’ndende ku Roma, ndipo cikhulupililo cake colimba cinakhudza bwanji mpingo wacikritsu? (Mac. 28:23, 30; Afil. 1:14)

  2. Ŵelenga Afilipi 2:19-30.

    Kodi ni mau otani amene Paulo anakamba oyamikila Timoteyo ndi Epafurodito, ndipo tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo? (Afil. 2:20, 22, 25, 29, 30; 1 Akor. 16:18; 1 Ates. 5:12, 13)

  3. Ŵelenga Filimoni 1-25.

    1. Kodi n’cifukwa ciani Paulo analangiza Filimoni kucita cinthu coyenela, ndipo zimenezi zithandiza bwanji akulu masiku ano? (Filim. 9; 2 Akor. 8:8; Agal. 5:13)

    2. Kodi mau a Paulo opezeka pa Filimoni 13, 14, amaonetsa bwanji kuti iye anali kulemekeza cikumbumtima ca ena mu mpingo? (1 Akor. 8:7, 13; 10:31-33)

  4. Ŵelenga 2 Timoteyo 4:7-9.

    Mofanana ndi mtumwi Paulo, kodi ifenso tingakhale bwanji ndi cidalilo cakuti Yehova adzatipatsa mphoto tikapitiliza kukhala okhulupilika mpaka kumapeto? (Mat. 24:13; Aheb. 6:10)

Nkhani 114

Mapeto a Zoipa Zonse

  1. N’cifukwa ciani Baibo ikamba za mahosi a kumwamba?

  2. Kodi dzina la nkhondo ya Mulungu imene adzabweletsa pa anthu oipa padziko lapansi n’ciani, ndipo colinga ca nkhondo imeneyi n’ciani?

  3. Tikaona pacithunzi-thunzi apa, kodi ndani adzatsogolela pa kumenya nkhondo imeneyi? Nanga n’cifukwa ciani wavala cisoti cacifumu, ndipo lupanga lake litanthauza ciani?

  4. Tikakumbukila zimene tinaphunzila m’nkhani namba 10, 15 ndi 33, n’cifukwa ciani sitiyenela kudabwa kuti Mulungu adzaononga anthu oipa?

  5. Nanga nkhani namba 36 ndi 76 zionetsa bwanji kuti Mulungu adzaononga anthu oipa ngakhale io amakamba kuti amam’lambila?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Chivumbulutso. 19:11-16.

    1. Kodi Malemba aonetsa bwino bwanji kuti Yesu Kristu ndiye wokwela hosi yoyela? (Chiv. 1:5; 3:14; 19:11; Yes. 11:4)

    2. Kodi magazi owazidwa ku malaya ovala pamwamba a Yesu atsimikizila bwanji kuti kugonjetsa kwake kudzakhala kosakaikitsa ndi kothelatu? (Chiv. 14:18-20; 19:13)

    3. Kodi ndani mwacionekele amene aphatikizidwamo m’gulu la asilikali amene atsatila hosi yoyela ya Yesu? (Chiv. 12:7; 19:14; Mat. 25:31, 32)

Nkhani 115

Paladaiso Yatsopano Padziko Lapansi

  1. Kodi Baibo imaonetsa kuti tidzasangala ndi moyo wabwanji mu Paladaiso padziko lapansi?

  2. Kodi Baibo imawalonjeza ciani anthu amene adzakhala mu Paladaiso?

  3. Kodi ni liti pamene Yesu adzatsimikiza kuti kusintha kwabwino kumeneku kwacitika?

  4. Pamene Yesu anali padziko lapansi, kodi anacita ciani kuonetsa zimene angacite monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu?

  5. Kodi Yesu ndi olamulila anzake adzatsimikiza ciani pamene adzalamulila dziko lapansi kucokela kumwamba?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Chivumbulutso 5:9, 10.

    N’cifukwa ciani tingakhale ndi cidalilo cakuti ao amene adzalamulila dziko lapansi mu ulamulilo wa zaka cikwi, adzakhala mafumu ndi ansembe acifundo? (Aef. 4:20-24; 1 Pet. 1:7; 3:8; 5:6-10)

  2. Ŵelenga Chivumbulutso 14:1-3.

    Kodi kulembedwa kwa dzina la Atate ndi la mwana wa nkhosa pamphumi za a 144,000, kutanthauza ciani? (1 Akor. 3:23; 2 Tim. 2:19; Chiv. 3:12)

Nkhani 116

Mmene Tingapezele Moyo Wamuyaya

  1. Kodi tifunika kudziŵa ciani ngati tifuna kuti tikapeze moyo wamuyaya?

  2. Monga zimene kamtsikana ndi anzake acita pacitunzi-thunzi apa, kodi tingaphunzile bwanji za Yehova Mulungu ndi Yesu?

  3. Kodi pacithunzi-thunzi apa uonaponso buku lina liti, ndipo n’cifukwa ciani tiyenela kuliŵelenga nthawi zonse?

  4. Kusiyapo kuphunzila za Yehova ndi Yesu, n’cianinso cina cimene tiyenela kucita kuti tikapeze moyo wamuyaya?

  5. Kodi titengamo phunzilo lanjia m’nkhani namba 69?

  6. Kodi citsanzo cabwino ca Samueli m’nkhani namba 55 citionetsa ciani?

  7. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu Kristu, ndipo tikacita zimenezo, tidzakhoza kucita ciani mtsogolo?

Mafunso oonjezela:

  1. Ŵelenga Yohane 17:3.

    Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti kudziŵa za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu si kutanthauza cabe kuloŵeza mfundo pamtima. (Mat. 7:21; Yak. 2:18-20; 1 Yoh. 2:17)

  2. Ŵelenga Masalimo 145:1-21.

    1. Kodi tili ndi zifukwa zambili bwanji zotamandila Yehova? (Sal. 145:8-11; Chiv. 4:11)

    2. Kodi Yehova ‘amakomela bwanji mtima aliyense,’ ndipo zimenezi zingatithandize bwanji kumuyandikila kwambili? (Sal. 145:9; Mat. 5:43-45)

    3. Ngati timaona kuti Yehova ni wofunika kwambili kwa ife, kodi cidzatilimbikitsa kucita ciani? (Sal. 119:171, 172, 175; 145:11, 12, 21)