Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mau Oyamba

Mau Oyamba

BUKULI lili ndi nkhani zimene zinacitika zoona. Nkhani zimenezi zicokela m’buku lofunika kwambili padziko lonse, ndipo buku limenelo ni Baibo. Nkhani zimenezi zidzakufotokozela mbili ya dziko kucokela pamene Mulungu anayamba kulenga zinthu mpaka kudzafika m’masiku athu ano. Udzaŵelenganso za malonjezo amene Mulungu adzabweletsa kutsogolo.

Buku limeneli lidzakupatsa cithunzi ca zimene zili m’Baibo. Lidzakuuza za anthu olembedwa m’Baibo ndi zimene anacita. Lidzakuuzanso za ciyembekezo cabwino kwambili ca moyo wamuyaya padziko lapansi m’paladaiso imene Mulungu walonjeza anthu.

M’buku lonse ili muli nkhani zokwanila 116, ndipo nkhani zimenezi zaikidwa m’magao okwanila 8. Peji yoyambilila pa cigao ciliconse, idzafotokoza mwacidule za m’cigao cimeneco. Nkhanizo zaikidwa motsatila dongosolo la mmene zinthu zinacitikila m’mbili. Zimenezi zidzakuthandiza kudziŵa nthawi imene zinthu zina zinacitika m’mbili, poziyelekezela ndi zocitika zina.

Nkhani zimenezo zalembedwa mu Cinyanja cosavuta. Ana ambili mudzakwanitsa kudziŵelengela nokha. Inu makolo, mudzaona kuti ana anu ang’ono adzasangalala kuti muziwaŵelengela nkhani zimenezi mobweleza-bweleza. Mudzapeza kuti bukuli lili ndi nkhani zimene zidzakondweletsa ana anu aang’ono ndi osinkhukilapo omwe.

Malemba osagwila mau aikidwa kumapeto kwa nkhani iliyonse. Tikulimbikitsani kuŵelenga malemba amenewa m’Baibo yanu pamene pacokela nkhani zimenezi. Mukatsiliza kuŵelenga nkhani iliyonse, muzionanso mafunso ophunzilila a nkhaniyo amene ali kumapeto kwa buku lino, ndipo muziyesa kukumbukila mayankho a mafunso amenewo.