Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

2

Dzina la Mulungu m’Malemba Acikristu Acigiriki

Dzina la Mulungu m’Malemba Acikristu Acigiriki

Akatswili a Baibulo amavomeleza kuti dzina la Mulungu loimilidwa ndi zilembo zinai zaciheberi (יהוה), limaonekela nthawi pafupifupi 7,000 m’zolemba zoyambilila za Malemba Aciheberi. Komabe, ambili amaona kuti m’mipukutu yoyambilila ya Malemba Acikristu Acigiriki munalibe dzinali. Pa cifukwa cimeneci Mabaibulo ambili amakono Acingelezi sanalembemo dzina la Yehova pomasulila cimene amati Cipangano Catsopano. Ngakhale pomasulila mau ogwidwa m’Malemba Aciheberi mmene zilembo zinai zaciheberi zoimila dzina la Mulungu limaonekela, omasulila ambili amaikamo “Ambuye” m’malo molemba dzina lenileni la Mulungu.

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika silitsatila njila yofala imeneyi. Limagwilitsila nchito dzina lakuti Yehova nthawi 237 m’Malemba Acikristu Acigiriki. Posankha kuti azicita zimenezi, omasulila anaganizila mfundo ziŵili zofunika kwambili: (1) Mipukutu yacigiriki imene tili nayo masiku ano si yoyambilila yeniyeni. Pa mipukutu masauzande imene ilipo masiku ano, yambili mwa imeneyi inalembedwa patatha zaka 200 kucokela pamene mipukutu yoyambilila imeneyo inalembedwa. (2) Zikuoneka kuti pofika nthawi imeneyo, okopawo mwina anacotsa zilembo zinai zaciheberi zoimila dzina la Mulungu ndi kuikapo mau a Cigiriki akuti Kyʹri·os, amene amatanthauza kuti “Ambuye.” Ngati si conco, ndiye kuti anawakopa kucokela ku mipukutu imene dzina la Mulungu linali litacotsedwamo kale.

Akomiti Yomasulila Baibulo la Dziko Latsopano anaona kuti pali umboni wokwanila bwino wakuti Tetragalamatoni inalimo m’mipukutu yoyambilila ya Cigiriki. Ananena zimenezi cifukwa ca maumboni otsatilawa:

  • Makope a Malemba Aciheberi amene anali kugwilitsidwa nchito m’nthawi ya Yesu ndi atumwi anali ndi zilembo zinai zaciheberi (Tetragalamatoni). Kale, ndi anthu ocepa cabe amene anatsutsa umboni umenewo. Tsopano popeza kuti mipukutu ya Malemba Aciheberi ya m’zaka 100 zoyambilila inapezeka pafupi ndi Qumran, pali umboni wosatsutsika.

  • M’nthawi ya Yesu ndi atumwi ake, zilembo zinai zaciheberi zoimila dzina la Mulungu zinali kupezeka m’mipukutu ya Malemba Aciheberi. Kwa zaka mahandiledi angapo akatswili a maphunzilo anali kuganiza kuti zilembo zinai zimenezi sizinali kupezeka m’Malemba Aciheberi a mipukutu ya Baibulo la Greek Septuagint. Kenako ca pakati pa zaka za m’ma 1900, akatswili anapeza zidutswa zakale kwambili za Baibulo la Greek Septuagint zimene zinaliko m’nthawi ya Yesu. Zidutswa zimenezo zili ndi dzina la Mulungu lolembedwa m’zilembo za Ciheberi. Conco m’nthawi ya Yesu, mipukutu ya Malemba Acigiriki inali ndi dzina la Mulungu. Komabe, kufika ca m’ma 300 C.E., mipukutu yaikulu ya Greek Septuagint, monga Codex Vaticanus ndi Codex Sinaiticus, inalibe dzina la Mulungu kucokela Genesis mpaka Malaki (mabuku amene dzinali linali kupezeka m’mipukutu yoyambilila). Conco, n’zosadabwitsa kuti m’zolemba zimene anasunga kucokela nthawi imeneyo, dzina la Mulungu silimapezeka m’cimene amati Cipangano Catsopano, kapena mbali ya Malemba Acigiriki ya Baibulo.

    Yesu ananena mosapita mbali kuti: “Ndabwela m’dzina la Atate wanga.” Anagogomezelanso kuti nchito zake anazicita mu ‘dzina la Atate’ wake

  • Malemba Acikristu Acigiriki amanena kuti nthawi zambili Yesu anali kugwilitsila dzina la Mulungu ndipo anali kulidziŵikitsa kwa ena. (Yohane 17:6, 11, 12, 26) Yesu ananena momveka bwino kuti: “Ndabwela m’dzina la Atate wanga.” Iye anagogomezelanso kuti nchito zake anazicita ‘m’dzina la Atate wake.’—Yohane 5:43; 10:25.

  • Popeza kuti Malemba Acikristu Acigiriki anali mbali ya Malemba ouzilidwa oonjezela pa Malemba Aciheberi opatulika, kusapezeka kwa dzina la Yehova sikugwilizana ndi zimenezo. Capakati pa zaka 100 zoyambilila, wophunzila Yakobo anauza akulu a ku Yerusalemu kuti: “Sumeoni wafotokoza bwino mmene Mulungu anaceukila anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa io atengemo anthu odziŵika ndi dzina lake.” (Macitidwe 15:14) Sicikanakhala canzelu kwa Yakobo kunena mau amenewa ngati anthu m’zaka 100 zoyambilila sanali kudziŵa dzina la Mulungu ndipo sanali kuligwilitsila nchito.

  • Dzina la Mulungu limapezeka m’Malemba Acikristu Acigiliki m’kalembedwe kake kacidule. Pa lemba la Chivumbulutso 19:1, 3, 4, 6 dzina la Mulungu lili m’mau akuti “Aleluya.” Mau amenewa amacokela ku mau Aciheberi amene amatanthauza kuti “Tamandani Ya.” Mau akuti “Ya” ndi cidule ca dzina la Yehova. Maina ambili amene anagwilitsidwa nchito m’Malemba Acikristu Acigiriki anatengedwa ku dzina la Mulungu. Ndipo mabuku ena amafotokoza kuti dzina lake lenileni la Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Cipulumutso.”

  • Mabuku akale a Aciyuda amasonyeza kuti Akristu Aciyuda anagwilitsila nchito dzina la Mulungu m’zolemba zao. Buku lakale la malamulo a Ayuda, lochedwa Tosefta, limene anamaliza kulilemba m’zaka 300 zoyambilila, limanena mau otsatilawa pofotokoza za mabuku a Akristu amene anatenthedwa tsiku la Sabata: “Mabuku a anthu olengeza Uthenga Wabwino ndi mabuku a minim [amene anali kuwaganizila kuti ndi mabuku a Akristu Aciyuda] anawatentha pamoto. Anatentha mipukutu imeneyo kumene aipeza, ndi mipukutu yokhala ndi Dzina la Mulungu.” Buku limeneli limagwilanso mau a Rabi Yosé wa ku Galileya, amene anakhalako ndi moyo kumayambililo a zaka 100 zoyambilila, limati pa masiku ena a mlungu, “munthu amacotsako masamba ena amene ali ndi Dzina la Mulungu [zioneka kuti anali kunena zolemba zacikristu] ndi kukawabisa kwina, ndipo otsala onse n’kuwatentha.”

  • Akatswili ena olemba Baibulo amanena kuti zioneka kuti dzina la Mulungu linalimo m’Malemba Aciheberi ojambulidwa opezeka m’Malemba Acikristu Acigiliki. Pa kamutu kakuti “Zilembo Zinai Zaciheberi za Dzina la Mulungu m’Cipangano Catsopano,” buku lina lomasulila mau (Anchor Bible Dictionary) limati: “Pali umboni wakuti Tetragalamatoni, Dzina la Mulungu, Yahweh, linalimo m’Malemba ena kapena Malemba onse a C[ipangano] C[akale], opezeka m’C[ipangano] C[atsopano] panthawi yoyamba imene Cipangano Catsopano cinali kulembedwa.” Katswili wa maphunzilo a Baibulo, George Howard, anati: “Popeza kuti zilembo zinai zaciheberi zinali kupezekabe m’Mabaibulo a Cigiriki [a Septuagint] amene Akristu oyambilila anali kugwilitsila nchito, m’pomveka kunena kuti olemba C[ipangano] C[atsopano], pogwila Malemba sanali kucotsa zilembo zinai zaciheberi za m’Cipangano Cakale.”

  • Omasulila Baibulo odziŵika anagwilitsila nchito dzina la Mulungu m’Malemba Acikristu Acigiriki. Omasulila ena amenewa anamasulila malemba kalekale, Baibulo lathu la Dziko Latsopano lisanafalitsidwe. Ndipo omasulila amenewa ndi nchito zao zimaphatikizapo Mabaibulo monga: A Literal Translation of the New Testament . . From the Text of the Vatican Manuscript, yolembedwa ndi Herman Heinfetter (1863); Baibulo la The Emphatic Diaglott, la Benjamin Wilson (1864); Baibulo la The Epistles of Paul in Modern English, la George Barker Stevens (1898); Baibulo la St. Paul’s Epistle to the Romans, lolembedwa ndi W. G. Rutherford (1900); Baibulo la The New Testament Letters, lolembedwa ndi J.W.C. Wand, Bishopu wa ku London (1946). Ndiponso, m’Baibulo limene linamasulidwa ndi Pablo Besson m’Cisipanishi kumayamblilo kwa m’ma 1900, muli dzina lakuti “Jehová” pa Yuda 14, ndipo pafupifupi mau a munsi 100 m’Baibulo limeneli amasonyeza kuti dzina la Mulungu lingaikidwenso pa lembalo. Kalekale malembawo asanamasulilidwe, Baibulo la Malemba Acikristu Acigiliki la m’zaka za m’ma 1500 kupita mtsogolo mumapezeka zilembo zinai zaciheberi zoimila dzina la Mulungu. M’cinenelo ca Cijeremani cokha, pafupifupi Mabaibulo 11 amagwilitsila nchito dzina la “Yehova” (kapena “Yahweh” lotsatila kachulidwe ka Ciheberi) m’Malemba Acikristu Acigiliki, pamene omasulila anai anaika dzinalo mumkutilamau [mabulaketi] patsogolo pa mau akuti “Ambuye.” Mabaibulo Acijeremani oposa 70 amagwilitsila nchito dzina la Mulungu m’mau a munsi kapena m’ndemanga.

  • Mabaibulo a m’zinenelo zoposa 100 ali ndi dzina la Mulungu m’Malemba Acikristu Acigiriki. Mabaibulo ambili a zinenelo za ku Africa, ku America, Asia, ndi zilumba za ku Ulaya ndi za m’nyanja ya Pacific, amagwilitsila nchito dzina la Mulungu momasuka. (Onani mndandanda pa masamba 1742 ndi 1743 mu Baibulo la Dziko Latsopano la Cingelezi) Omasulila Mabaibulo amenewa anasankha kugwilitsila nchito dzina la Mulungu pa zifukwa zofanana ndi zimene tachula pamwambapa. Ena mwa Mabaibulo amenewa a Malemba Acikrisutu Acigiriki akhala akupezeka m’zaka zaposacedwapa. Citsanzo ndi Baibulo la Rotuman (1999), limene lili ndi dzina lakuti Jihova nthawi 51 m’mavesi 48, ndi Baibulo la Batak (Toba) (1989) la ku Indonesia limagwilitsila nchito dzina lakuti “Jahowa” nthawi 110.

Dzina la Mulungu pa Maliko 12:29, 30 m’cinenelo ca ku Hawaii limene linamasulilidwa mu 1816)

Mosakaikila konse, pali umboni woonekelatu wobwezeletsa dzina la Yehova m’Malemba Acikristu Acigiliki. Zimenezi n’zimene omasulila Baibulo la Dziko Latsopano acita. Iwo amalemekeza kwambili dzina la Mulungu, ndipo amaopa kukhumudwitsa Mulungu mwakucotsa zilizonse zimene zinali m’mipukutu yoyambilila.—Chivumbulutso 22:18, 19.