Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

19

Kalendala ya Ciheberi

Kalendala ya Ciheberi

NISANI (ABIBU) March​—April

14 Pasika

15-21 Mkate Wopada Cotupitsa

16 Kupeleka zipatso zoyamba

Yorodano asefukila ndi mvula, ndi cipale cofewa

Balele

IYARA (ZIVI) April​—May

14 Pasika Wocitika Nthawi Yake Itapita

Cilimwe ciyamba, kuthambo kulibe mitambo

Tiligu

SIVANI May​—June

6 Cikondwelelo ca Masabata (Pentekosite)

Kunja kutentha, mpweya wabwino

Tiligu, nkhuyu zoyamba

TAMUZI June​—July

 

Kutentha kuonjezeleka, mame ambili m’malo ambili

Mpesa woyamba

AB July​—August

 

Kutentha kufika pacimake

Zipatso za m’cilimwe

ELULI August​—September

 

Kutentha kupitiliza

Kanjeza, mpesa, ndi nkhuyu

TISHIRI (ETANIMU) September​—October

1 Kuliza lipenga

10 Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo

15-21 Tsiku la Cikondwelelo ca Misasa

22 Msonkhano wapadela

Cilimwe cikutha, mvula iyamba kugwa

Kulima

HESHVANI (BULU) October​—November

 

Mvula yowaza

Maolivi

KISILEVI November​—December

25 Cikondwelelo ca Kupeleka Kacisi kwa Mulungu

Mvula ionjezeka, madzi aundana, Cipale cofewa pamapili

Atsekela ziŵeto m’khola

TEBETI December​—January

 

Kuzizila, mvula zifika pacimake, Cipale cofewa pa m’mapili

Zomela zimayamba kuphukilanso

SEBATI January​—February

 

Nyengo yozizila icepekela, mvula ipitiliza

Amondi acita maluwa

ADARA February​—March

14, 15 Purimu

Kucita mabingu ndi matalala kaŵilikaŵili

Fulakesi

VEADARA March

M’zaka 19 zilizonse anali kuonjezela mwezi wina wapadela maulendo 7