Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

5

Uthenga wa m’Baibulo

Uthenga wa m’Baibulo

Yehova ndi woyenela kulamulila. Iye ndiye amalamulila bwino kwambili. Colinga cake kaamba ka dziko lapansi ndi mtundu wa anthu cidzakwanilitsika.

Pambuyo pa 4026 B.C.E.

“Njoka” inakaikila kuti Yehova ndi woyenela kulamulila ndiponso ulamulilo wake. Yehova analonjeza kuutsa “mbeu,” imene pothela pake idzaphwanya njoka, Satana. (Genesis 3:1-5, 15) Komabe, Yehova wapeleka nthawi kuti anthu adzilamulile mosonkhezeledwa ndi njoka.

1943 B.C.E.

Yehova anauza Abulahamu kuti “mbeu” yolonjezedwa idzakhala mmodzi wa mbadwa zake.—Genesis 22:18.

Pambuyo pa 1070 B.C.E.

Yehova anatsimikizila Mfumu Davide ndi mwana wake Solomoni kuti mbeu yolonjezedwa idzacokela m’mzela wa banja lake.—2 Samueli 7:12, 16; 1 Mafumu 9:3-5; Yesaya 9:6, 7.

29 C.E.

Yehova ananena kuti Yesu ndi “mbeu” yolonjezedwa imene idzakhala pampando wacifumu wa Davide.—Agalatiya 3:16; Luka 1:31-33; 3:21, 22.

33 C.E.

Njoka, Satana kwa kanthawi anaononga “mbeu” yolonjezedwa mwa kucititsa Yesu kuphedwa. Yehova anaukitsila Yesu kumoyo wakumwamba ndi kulandila mtengo wa moyo wa Yesu waungwilo, mwakutelo anakhazikitsa maziko akuti macimo akhululukidwe ndi kupeleka mwai kwa mbadwa za Adamu kuti zikapeze moyo wosatha.—Genesis 3:15; Machitidwe 2:32-36; 1 Akorinto 15:21, 22.

Ca m’ma 1914 C.E.

Yesu aponya cinjoka, Satana kudziko lapansi, ndi kumtsekela kumeneko kwa kanthawi kocepa.—Chivumbulutso 12:7-9, 12.

Mtsongolo

Yesu amanga Satana kwa zaka 1,000 ndiyeno kumuononga, m’mau ophiphilitsa am’phwanya mutu. Cifuno ca Yehova coyambilila cadziko lapansi ndi anthu cikwanilitsika, citonzo cicotsedwa padzina lake, ndipo ulamulilo wake utsimikizilidwa.—Chivumbulutso 20:1-3, 10; 21:3, 4.