Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

4-E

Zocitika zazikulu za paumoyo wa Yesu Padziko​—Utumiki wa Yesu ku Galileya (Mbali 3) ku Yudeya

Zocitika zazikulu za paumoyo wa Yesu Padziko​—Utumiki wa Yesu ku Galileya (Mbali 3) ku Yudeya

NTHAWI

MALO

COCITIKA

MATEYU

MALIKO

LUKA

YOHANE

32, pambuyo pa Pasika

Nyanja ya Galileya; Betsaida

M’bwato paulendo wa ku Betsaida, Yesu acenjeza za cofufumitsa ca Afalisi; acilitsa munthu wakhungu

16:5-12

8:13-26

   

Dela la Kaisara wa ku Filipi

Makiyi a Ufumu; anenelatu za imfa ndi kuukitsidwa kwake

16:13-28

8:27–9:1

9:18-27

 

Mwina Phili la Herimoni

Kusandulika; Yehova alankhula

17:1-13

9:2-13

9:28-36

 

Cigawo ca Kaisareya wa Filipi

Acilitsa mnyamata wakhunyu

17:14-20

9:14-29

9:37-43

 

Galileya

Anenelatunso za imfa yake

17:22, 23

9:30-32

9:43-45

 

Kaperenao

Akhoma msonkho ndi kobidi ya mkamwa mwa nsomba

17:24-27

     

Wamkulu mu Ufumu; mafanizo a nkhosa yotaika ndi kapolo wosakhululukila

18:1-35

9:33-50

9:46-50

 

Galileya-Samariya

Ulendo wa ku Yerusalemu, auza ophunzila ake kuti adzafunika kuika Ufumu poyamba

8:19-22

 

9:51-62

7:2-10

Utumiki wa Yesu Wakumapeto mu Yudeya

NTHAWI

MALO

COCITIKA

MATEYU

MALIKO

LUKA

YOHANE

32, Cikondwelelo ca Misasa

Yerusalemu

Aphunzitsa pa Cikondwelelo ca Misasa; asilikali abwela kudzamugwila

     

7:11-52

Anena kuti “Ine ndine kuwala kwa dziko”; acilitsa munthu wakhungu

     

8:12–9:41

Mwina ku Yudeya

Atumiza atumwi 70; abwelako osangalala

   

10:1-24

 

Yudeya; Betaniya

Fanizo la Msamariya wacifundo; Apita kukaceza kunyumba ya Mariya ndi Marita

   

10:25-42

 

Mwina ku Yudeya

Aphunzitsanso pemphelo la citsanzo; fanizo la bwenzi loumilila

   

11:1-13

 

Kutulutsa ziŵanda ndi cala ca Mulungu; apelekanso cizindikilo ca Yona

   

11:14-36

 

Akudya ndi Mfalisi; atsutsa cinyengo ca Afalisi

   

11:37-54

 

Mafanizo: munthu wacuma wopanda nzelu ndi mtumiki wokhulupilika

   

12:1-59

 

Acilitsa mai wopunduka pa Sabata; mafanizo a kanjele ka mpilu ndi zofufumitsa

   

13:1-21

 

32, Cikondwelelo Copeleka Kacisi

Yerusalemu

Mafanizo a m’busa wabwino ndi khola la nkhosa; Ayuda ayesa kumponya miyala; apita ku Betaniya kutsidya la Yorodano

     

10:1-39