Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

4-A

Zocitika Zazikulu Paumoyo wa Yesu wa Padziko​—Zocitika Zotifikitsa pa Nthawi ya Utumiki wa Yesu

Zocitika Zazikulu Paumoyo wa Yesu wa Padziko​—Zocitika Zotifikitsa pa Nthawi ya Utumiki wa Yesu

Mauthenga Abwino Anai, Ondandalikidwa Motsatila Nthawi ya Zocitika

Machati otsatila ali ndi mamapu amene akusonyeza maulendo a Yesu aulaliki. Zizindikilo zoloza pa mapu sizikusonyeza miseu yeniyeni imene anagwilitsila nchito koma zikungosonyeza kumene anali kupita. Cizindikilo ca “c.” ciimila “m’ma” kapena “pafupifupi.”

Zocita Zotifikitsa pa Nthawi ya Utumiki wa Yesu

NTHAWI

MALO

ZOCITIKA

MATEYU

MALIKO

LUKA

YOHANE

3 B.C.E.

Yerusalemu, kacisi

Mngelo Gabirieli anenelatu za kubadwa kwa Yohane m’batizi kwa Zekariya

   

1:5-25

 

c. 2 B.C.E.

Nazareti; Yudeya

Mngelo Gabirieli anenelatu za kubadwa kwa Yesu kwa Mariya; apita kukaceza kwa m’bale wake Elizabeti

   

1:26-56

 

2 B.C.E.

Dela la kumapili la Yedeya

Yohane m’batizi abadwa ndi kupatsidwa dzina; Zekariya anenela kuti; Yohane adzakhala m’cipululu

   

1:57-80

 

2 B.C.E., c. Oct.

Betelehemu

Yesu abadwa; “Mau ameneyo anakhala ndi thupi”

1:1-25

 

2:1-7

1:1-5, 9-14

Pafupi ndi Betelehemu; Betelehemu

Mngelo alengeza uthenga wabwino kwa abusa; angelo atamanda Mulungu; Abusa apita kukaona khanda

   

2:8-20

 

Betelehemu; Yerusalemu

Yesu adulidwa (patsiku la 8); makolo ake amupeleka kukacisi (pambuyo pa tsiku la 40)

   

2:21-38

 

1 B.C.E. kapena 1 C.E.

Yerusalemu; Betelehemu; Iguputo; Nazareti

Okhulupilila nyenyezi am’cezela; banja lithawila ku Iguputo; Herode akupha ana aang’ono amuna; Banja libwelako ku Iguputo ndi kukhala ku Nazareti

2:1-23

 

2:39, 40

 

12 C.E., Pasika

Yerusalemu

Yesu wa zaka 12 pa kacisi afunsa mafunso aphunzitsi

   

2:41-50

 
 

Nazareti

Abwelela ku Nazareti; apitiliza kumvela makolo ake; aphunzila ukalipentala; Mariya abeleka ana amuna ena anai, ndi ana akazi (Mat. 13:55, 56; Maliko 6:3)

   

2:51, 52

 

29, March/April

Cipululu, Mtsinje wa Yorodano

Yohane Mbatizi ayamba utumiki wake

3:1-12

1:1-8

3:1-18

1:6-8, 15-28