Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 7

Kodi Baibulo linalosela ciani za nthawi yathu ino?

Kodi Baibulo linalosela ciani za nthawi yathu ino?

“Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina . . . Zonsezi ndi ciyambi ca masautso, ngati mmene zimayambila zoŵaŵa za pobeleka.”

Mateyu 24:7, 8

“Kudzafika aneneli ambili onyenga ndipo adzasoceletsa anthu ambili. Cifukwa ca kuonjezeka kwa kusamvela malamulo, cikondi ca anthu ambili cidzazilala.”

Mateyu 24:11, 12

“Mukadzamva phokoso la nkhondo ndi mbili za nkhondo, musadzacite mantha. Zimenezi ziyenela kucitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.”

Maliko 13:7

“Kudzacitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala milili ndi njala m’malo osiyanasiyana. Kudzaoneka zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikilo zodabwitsa.”

Luka 21:11

“Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvela makolo, osayamika, osakhulupilika, osakonda acibale awo, osafuna kugwilizana ndi anzao, onenela anzao zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, aciwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipeleka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe.”

2 Timoteyo 3:1-5