Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 17

Kodi Baibulo lingathandize bwanji banja lanu?

Kodi Baibulo lingathandize bwanji banja lanu?

AMUNA/ATATE

“Mwa njila imeneyi amuna akonde akazi ao monga matupi ao. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda . . . aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha.”

Aefeso 5:28, 29, 33

“Abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalele m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”

Aefeso 6:4

AKAZI

“Mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.”

Aefeso 5:33

“Inu akazi, muzigonjela amuna anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenela kwa anthu otsatila Ambuye.”

Akolose 3:18

ANA

“Ananu, muzimvela makolo anu mwa Ambuye, pakuti kucita zimenezi n’cilungamo. ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mai ako,’ ndilo lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo: ‘Kuti zinthu zikuyendele bwino, ndiponso kuti ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.’”

Aefeso 6:1-3

“Ananu, muzimvela makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kucita zimenezi kumakondweletsa Ambuye.”

Akolose 3:20