Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 11

N’ciani Cimacitika Munthu Akafa?

N’ciani Cimacitika Munthu Akafa?

“Mzimu wake umacoka, ndipo iye amabwelela kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimathelatu.”

Salimo 146:4

“Pakuti amoyo amadziŵa kuti adzafa, koma akufa sadziŵa ciliconse . . . “Ciliconse cimene dzanja lako lapeza kuti licite, ucicite ndi mphamvu zako zonse, pakuti kulibe kugwila nchito, kuganiza zocita, kudziŵa zinthu, kapena nzelu, ku Manda kumene ukupitako.”

Mlaliki 9:5, 10

“[Yesu] anauza ophunzila akewo kuti: ‘Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.’ Apa Yesu anali kunena za imfa yake. Koma io anaganiza kuti anali kunena za kugona tulo teniteni. Conco, Yesu tsopano anawauza momveka bwino kuti: ‘Lazaro wamwalila.’”

Yohane 11:11, 13, 14