Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 1

Kodi Mulungu ndani?

Kodi Mulungu ndani?

“Kuti anthu adziŵe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.”

Salimo 83:18

“Dziŵani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndi amene anatipanga, sitinadzipange tokha.”

Salimo 100:3

“Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapeleka ulemu wanga kwa wina aliyense kapena kupeleka ulemelelo wanga kwa zifanizilo zogoba.”

Yesaya 42:8

“Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”

Aroma 10:13

“N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.”

Aheberi 3:4

“Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo? Ndi amene akutsogolela gulu lonse la nyenyezizo malinga ndi ciŵelengelo cake, ndipo amaziitana pochula iliyonse dzina lake. Cifukwa ca kuculuka kwa mphamvu zake zoopsa, ndiponso cifukwa cakuti ali ndi mphamvu zambili zocitila zinthu, palibe imene imasoŵa.”

Yesaya 40:26