Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 14

Cuma canu mungacisamalile bwanji??

Cuma canu mungacisamalile bwanji??

“Wokonda zosangalatsa adzakhala munthu wosauka. Wokonda vinyo ndi mafuta sadzapeza cuma.”

Miyambo 21:17

“Wobweleka amakhala kapolo wa wobweleketsayo.”

Miyambo 22:7

“Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuŵelengela ndalama zimene adzaononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanila kumalizila nsanjayo? Akapanda kutelo, angayale maziko koma osatha kuimaliza, ndipo onse oona angayambe kumuseka, n’kumanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba bwinobwino kumanga, koma zamukanika kumaliza.’”

Luka 14:28-30

“Anthu onsewo atakhuta, iye anauza ophunzila ake kuti: ‘Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasaonongeke ciliconse.’”

Yohane 6:12