Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 16

Mungapilile bwanji nkhawa?

Mungapilile bwanji nkhawa?

“Umutulile Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakucilikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.”

Salimo 55:22

“Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”

Miyambo 21:5

“Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.”

Yesaya 41:10

“Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?”

Mateyu 6:27

“Musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.”

Mateyu 6:34

“Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.”

Afilipi 1:10

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”

Afilipi 4:6, 7