Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 6

Kodi Baibulo linalosela ciani za Mesiya?

Kodi Baibulo linalosela ciani za Mesiya?

MAULOSI

“Iwe Betelehemu Efurata,. . . mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulila mu Isiraeli.”

Mika 5:2

OKWANILITSIDWA

“Yesu atabadwa ku Betelehemu wa Yudeya m’masiku a mfumu Herode, okhulupilila nyenyezi ocokela kumadela a kum’mawa anabwela ku Yerusalemu.”

Mateyu 2:1

MAULOSI

“Iwo akugaŵana zovala zanga pakati pao, Ndipo akucita maele pazovala zanga.”

Salimo 22:18

OKWANILITSIDWA

“Tsopano asilikaliwo atamupacika Yesu, anatenga malaya ake akunja ndi kuwagawa m’zigawo zinai . . . Koma malaya amkatiwo analibe msoko, anali oombedwa kucokela pamwamba mpaka pansi. Conco iwo anayamba kukambilana kuti: ‘Malaya awa tisawang’ambe, koma tiyeni ticite maele kuti tidziŵe amene angatenge malaya amenewa.’”

Yohane 19:23, 24

MAULOSI

“Amateteza mafupa onse a wolungamayo. Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.”

Salimo 34:20

OKWANILITSIDWA

“Atafika pa Yesu, sanamuthyole miyendo poona kuti wafa kale.”

Yohane 19:33

MAULOSI

“Iye anabayidwa cifukwa ca zolakwa zathu.”

Yesaya 53:5

OKWANILITSIDWA

“Mmodzi wa asilikaliwo anamulasa ndi mkondo m’mbalimu cam’mimba, ndipo nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi.”

Yohane 19:34

MAULOSI

“Iwo anandipatsa ndalama 30 zasiliva monga malipilo anga.”

Zekariya 11:12, 13

OKWANILITSIDWA

“Pambuyo pake mmodzi wa ophunzila 12 aja, wochedwa Yudasi Isikariyoti, anapita kwa ansembe aakulu n’kuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa ciani ndikamupeleka kwa inu?” Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.”

Mateyu 26:14, 15; 27:55