Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 18

Mungayandikile bwanji Mulungu?

Mungayandikile bwanji Mulungu?

“Inu Wakumva pemphelo, anthu a mitundu yonse adzabwela kwa inu.”

Salimo 65:2

“Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzaongola njila zako.”

Miyambo 3:5, 6

“Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Kristu, amene inu munamutuma.”

Yohane 17:3

“Kwenikweni, [Mulungu] sali kutali ndi aliyense wa ife.”

Machitidwe 17:27

“Ine ndikupitiliza kupemphela kuti cikondi canu cipitilile kukula, limodzi ndi kudziŵa zinthu molondola, komanso kuzindikila zinthu bwino kwambili.”

Afilipi 1:9

“Conco ngati wina akusoŵa nzelu, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka moolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza.”

Yakobo 1:5

“Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani. Yeletsani manja anu ocimwa inu, ndipo yeletsani mitima yanu, okayikakayika inu.”

Yakobo 4:8

“Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”

1 Yohane 5:3