FUNSO 10
N’ciani cimene Baibulo limalonjeza ponena za mtsogolo?WEB:OnPageTitleSentenceCaseN’ciani cimene Baibulo limalonjeza ponena za mtsogolo?
“Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”
Salimo 37:29
“Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”
Mlaliki 1:4
“Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”
Yesaya 25:8
“Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwela phili ngati mmene imacitila mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa. Pakuti m’cipululu mudzatumphuka madzi ndipo m’dela lacipululu mudzayenda mitsinje.”
Yesaya 35:5, 6
“Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”
Chivumbulutso 21:4
“Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo, ndipo anthu anga osankhidwa mwapadela adzapindula mokwanila ndi nchito ya manja ao.”
Yesaya 65:21, 22