Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 3

Ndani analemba Baibulo?

Ndani analemba Baibulo?

“Mose analemba mau onse a Yehova.”

Ekisodo 24:4

“Danieli analota maloto ndipo anaona masomphenya atagona pabedi lake. Pa nthawi imeneyo, analemba zimene analotazo, ndipo anafotokoza nkhani yonseyo.”

Danieli 7:1

“Pamene munalandila mau a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandile monga mau a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mau a Mulungu.”

1 Atesalonika 2:13

“Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa.”

2 Timoteyo 3:16

“Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mau ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu woyela.”

2 Petulo 1:21