Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 8

Kodi Mulungu ndiye amacititsa kuti anthu azivutika?

Kodi Mulungu ndiye amacititsa kuti anthu azivutika?

“Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.”

Yobu 34:10

“Munthu akakhala pa mayeselo asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.”

Yakobo 1:13

“Mutulileni nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.”

1 Petulo 5:7

“Yehova sakucedwa kukwanilitsa lonjezo lake, ngati mmene anthu ena amaonela kuti akucedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzaonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”

2 Petulo 3:9