Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 2

Mungaphunzile Bwanji za Mulungu?

Mungaphunzile Bwanji za Mulungu?

“Buku la malamulo ili lisacoke pakamwa pako, uziliŵelenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatila zonse zolembedwamo. Pakuti ukatelo, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzacita zinthu mwanzelu.”

Yoswa 1:8

“Iwo anapitiliza kuŵelenga bukulo mokweza. Anapitiliza kuŵelenga cilamulo ca Mulungu woona, kucifotokozela ndi kumveketsa tanthauzo lake. Iwo anapitiliza kuthandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuŵelenga.”

Nehemiya 8:8

“Wodala ndi munthu amene sayenda motsatila malangizo a anthu oipa . . . Koma amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, Ndipo amaŵelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku. . . . Zocita zake zonse zidzamuyendela bwino.”

Salimo 1:1-3

“Filipo anathamanga m’mbali mwa galetalo ndi kumumva akuŵelenga mokweza m’buku la Yesaya mneneli. Ndipo Filipo anafunsa kuti: ‘Kodi mukumvetsa zimene mukuŵelengazo?’ Poyankha iye anati: ‘Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulila?’”

Machitidwe 8:30, 31

“Cilengedwele dziko kupita mtsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekela m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso cifukwa comveka cosakhulupilila kuti kuli Mulungu.”

Aroma 1:20

“Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipeleke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”

1 Timoteyo 4:15

“Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.”

Aheberi 10:24, 25

“Ngati wina akusoŵa nzelu, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka moolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza.”

Yakobo 1:5