FUNSO 5
Kodi m’Baibulo Muli uthenga Wotani?
“Ndidzaika cidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake. Mbeu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza cidendene.”
Genesis 3:15
“Kudzela mwa mbeu yako, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso ndithu cifukwa cakuti wamvela mau anga.”
Genesis 22:18
“Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.”
“Mulungu amene amapatsa mtendele aphwanya Satana pansi pa mapazi anu posacedwapa.”
Aroma 16:20
“Zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzadziika pansi pa amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”
1 Akorinto 15:28
“Tsopano, malonjezo anapelekedwa kwa Abulahamu ndi kwa mbeu yake . . . , amene ndi Kristu. Ndiponso ngati muli a Kristu, ndinudi mbeu ya Abulahamu.”
Agalatiya 3:16, 29
“Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Kristu wake. Iye adzalamulila monga mfumu kwamuyaya.”
Chivumbulutso 11:15
“Conco cinjokaco cinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wochedwa Mdyelekezi ndi Satana, amene akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”
Chivumbulutso 12:9
“Kenako anagwila cinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyelekezi ndiponso Satana, ndi kumumanga zaka 1,000.”
Chivumbulutso 20:2