Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

FUNSO 13

Kodi Baibulo limakamba ciani za nchito?

Kodi Baibulo limakamba ciani za nchito?

“Kodi wamuona munthu waluso pa nchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu. Sadzaima pamaso pa anthu wamba.”

Miyambo 22:29

“Wakubayo asabenso, koma agwile nchito molimbikila. Agwile ndi manja ake nchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosoŵa.”

Aefeso 4:28

“Munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, cifukwa coti wagwila nchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.”

Mlaliki 3:13