Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anzake a Mulungu Amakana Kucita Voipa

Anzake a Mulungu Amakana Kucita Voipa

Phunzilo 14

Anzake a Mulungu Amakana Kucita Voipa

Satana amanyengelela anthu kuti azicita vinthu voipa. Munthu amene amafuna kukhala mnzake wa Mulungu, naye afunika kuzonda vimene Mulungu amazonda. (Salmo 97:10) Onani vinthu vina voipa vimene anzake a Mulungu amakana kucita:

Macimo a zogonana. “Usacite cigololo.” (Eksodo 20:14) Nako kugonana mukalibe kukwatilana ni kulakwa.—1 Akorinto 6:18.

Kuledzela kapena ‘kukolewa.’ “Oledzela, . . . sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:10.

Kupha munthu, Kucotsa mimba. “Usaphe.”—Eksodo 20:13.

Kuba. “Usabe.”—Eksodo 20:15.

Kunama. Yehova amazonda munthu wa “lilime lonama.”—Miyambo 6:17.

Ciwawa na kukalipa kopitilila. ‘Yehova . . . amuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa.’ (Salmo 11:5) ‘Nchito za thupi, . . . [ziphatikizapo] kupsa mtima.’—Agalatiya 5:19, 20.

Njuga. “Muleke kuyanjana ndi aliyense . . . waumbombo.”—1 Akorinto 5:11, NW.

Kuzondana cifukwa cosiyana khungu (nkhanda) kapena kusiyana mitundu. ‘Kondanani nao adani anu, ndi kupemphelela iwo akuzunza inu.’—Mateyu 5:43, 44.

Zimene Mulungu amatiuza zimatipindulitsa. Nthawi zina cimavuta kukana voipa. Koma Yehova na Mboni zake angakuthandizeni kukana kucita voipa vimene Mulungu samafuna.—Yesaya 48:17; Afilipi 4:13; Ahebri 10:24, 25.