Kodi Adani a Mulungu ni Andani?
Phunzilo 8
Kodi Adani a Mulungu ni Andani?
Satana Mdyelekezi ndiye mdani mkulu wa Mulungu. Iye ni mngelo amene anapandukila Yehova. Ndipo Satana ameneyo apitiliza kutsutsa Mulungu na kucititsa mavuto akulu kwa anthu. Satana ni woipa. Ni wabodza ndipo amapha anthu.—Yohane 8:44.
Angelo ena anagwilizana na Satana kupandukila Mulungu. Angelo amenewo Baibo imawaitana kuti viŵanda. Monga mmene Satana alili, viŵanda navo ni adani a anthu. Vimakonda kuvutitsa anthu. (Mateyu 9:32, 33; 12:22) Koma Yehova adzaonongelatu Satana na viŵanda vake. Iwo atsala na nthawi ing’ono cabe yovutitsa anthu.—Cibvumbulutso 12:12.
Ngati mufuna kukhala mnzake wa Mulungu, osacita zimene Satana amafuna kuti mucite. Satana na viŵanda vake amazondana na Yehova. Iwo ni adani a Mulungu, ndipo amafuna kuti na imwe mukhale mdani wa Mulungu. Conco, muyenela kusankha amene mufuna kukondweletsa—Satana kapena Yehova. Ngati mufuna moyo wosatha, muyenela kucita zimene Mulungu amafuna. Satana ali na njila zambili zonamilamo anthu. Iye amapusitsa anthu ambili.—Cibvumbulutso 12:9.