Kodi Anzake a Mulungu ni Andani?
Phunzilo 9
Kodi Anzake a Mulungu ni Andani?
Yesu Khristu ni Mwana wa Mulungu, ndipo ni mnzake wapamtima. Poyamba, Yesu anali kumwamba monga mngelo wamphamvu. (Yohane 17:5) Ndiyeno, anabwela kudzakhala munthu padziko lapansi, kudzaphunzitsa coonadi ponena za Mulungu. (Yohane 18:37) Pambuyo pake, anataya moyo wake waumunthu kuti apulumutse anthu omvela Mulungu ku ucimo na imfa. (Aroma 6:23) Panthawi ino, Yesu ni Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewo ni boma imene idzabweletsa Paladaiso padziko lapansi pano.—Cibvumbulutso 19:16.
Angelo nawo ni anzake a Mulungu. Angelo sanayambile moyo wawo padziko lapansi. Mulungu anawalengela kumwamba akalibe kupanga dziko lapansi. (Yobu 38:4-7) Angelo aliko mamiliyoni ambili. (Danieli 7:10) Anzake a Mulungu akumwamba amenewa amafuna kuti anthu aphunzile coonadi conena za Yehova.—Cibvumbulutso 14:6, 7.
Mulungu ali na anzake ena padziko lapansi; iye amawaitana kuti mboni zake. Mboni, ni munthu amene mu khoti amanena zimene adziŵa ponena za munthu kapena cinthu cina. A Mboni za Yehova amauza anthu zimene adziŵa ponena za Yehova na cifunilo cake. (Yesaya 43:10) Mofanana na angelo, a Mboni amafuna kukuthandizani kuti muphunzile coonadi conena za Yehova. Afuna kuti na imwe mukhale mnzake wa Mulungu.