Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kutengapo Phunzilo pa Zimene Zinacitika Kumbuyo

Kutengapo Phunzilo pa Zimene Zinacitika Kumbuyo

Phunzilo 7

Kutengapo Phunzilo pa Zimene Zinacitika Kumbuyo

Yehova sadzalola kuti anthu oipa akakhalemo mu Paladaiso cifukwa angaiwononge. Anzake cabe a Mulungu ni amene adzakhalamo. Nanga anthu oipa cidzawacitikila ni ciyani? Kuti mudziŵe, mvelani vimene vinacitika mu nthaŵi ya Nowa. Papita zaka masauzande pamene iye anakhalapo. Anali munthu wabwino wolimbikila kucita zimene Yehova anali kufuna. Koma anthu ena padziko lapansi anali kucita vinthu voipa. Conco, Yehova anauza Nowa kuti adzabweletsa cigumula ca madzi kuti aononge anthu onse oipa. Kuti Nowa na banja lake asafe pacigumula cimeneco, Yehova anamuuza kupanga cingalawa copulumukilamo.—Genesis 6:9-18.

Nowa na Banja lake anapanga cingalawa. Cigumula cikalibe kubwela, Nowa anacenjeza anthu, koma iwo sanamumvele. Iwo anapitiliza kucita vinthu voipa. Pamene Nowa anatsiliza kupanga cingalawa, analoŵetsamo vinyama. Ndiyeno, iye na banja lake anangena mu cingalawa. Pambuyo pake, Yehova anabweletsa cimvula cikulu. Cimvula cimeneco cinagwa kwa masiku 40 usana na usiku. Ndipo madzi amenewo anaculuka na kudzala padziko lonse lapansi.—Genesis 7:7-12.

Anthu oipa aja onse anafa, koma Nowa na banja lake anapulumuka. Pambuyo pakuti Yehova awapulumutsa ku cigumula, anawabwezela padziko lapansi limene anayeletsa mwa kucotsapo anthu oipa. (Genesis 7:22, 23) Baibo imakamba kuti mtsogolo Yehova adzaononganso anthu amene safuna kucita zinthu zabwino. Koma anthu abwino sadzawaononga. Iwo adzakhala na moyo wosatha mu Paladaiso padziko lapansi.—2 Petro 2:5, 6, 9.

Masiku ano anthu ambili amacita vinthu voipa. Mu dziko muli mavuto ambili. Yehova watumiza Mboni zake mobwelezabweleza kuti zicenjeze anthu, koma anthu ambili safuna kumvela mau ake. Iwo safuna kuleka makhalidwe awo oipa. Safuna kuti Mulungu aziwauza zimene zili zabwino na zoipa. Kodi ni ciyani cidzacitikila anthu amene ali conco? Kodi tsiku lina adzasintha makhalidwe awo? Ambili sadzaleka. Ndiye cifukwa cake nthawi ibwela pamene Mulungu adzaononga anthu onse oipa, cakuti sadzakhalaponso.—Salmo 92:7.

Dziko lapansi silidzaonongedwa; koma adzalipanga paladaiso. Anthu amene ni anzake a Mulungu adzakhala na moyo wosatha mu Paladaiso padziko lapansi.—Salmo 37:29.