Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuti Musunge Ubwenzi, Mufunikila Kukhala Munthu Waubwenzi

Kuti Musunge Ubwenzi, Mufunikila Kukhala Munthu Waubwenzi

Phunzilo 17

Kuti Musunge Ubwenzi, Mufunikila Kukhala Munthu Waubwenzi

Kuti ubwenzi upitilize payenela kukhala cikondi. Mukaphunzila zambili ponena za Yehova, cikondi canu kwa iye cidzakula kwambili. Ndipo cikondi canu pa iye cikakula, cifuno canu comutumikila naco cidzakula. Zimenezi zidzakuthandizani kukhala wophunzila wa Yesu Khristu. (Mateyu 28:19) Mukaloŵa mu gulu la Mboni za Yehova, limene ni banja lacimwemwe, mudzakhala mnzake wa Mulungu kwamuyaya. Kodi mufunika kucita ciyani kuti muloŵe mu banja limeneli?

Mufunika kuonetsa cikondi canu kwa Mulungu mwa kusunga malamulo ake. “Ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ake; ndipo malamulo ake sali olemetsa.”—1 Yohane 5:3.

Muzicita zimene mumaphunzila. Yesu anasimba nthano ina imene imaonetsa zimenezi. Munthu wocenjela anamanga nyumba yake pa cimwala kapena kuti thanthwe. Koma munthu wopusa anamanga nyumba yake pamcenga. Pamene cimvula camphepo cinabwela, nyumba imene anamanga pacimwala siinagwe. Koma nyumba imene anamanga pamcenga inagwa kugwelatu. Ndiyeno, Yesu anakamba kuti anthu amene amamvela, na kucita zimene amawaphunzitsa, ali monga munthu wocenjela uja, amene anamanga nyumba yake pacimwala. Koma awo amene amamvela cabe zimene iye amaphunzitsa koma sazicita, ali monga munthu wopusa uja, amene anamanga nyumba yake pamcenga. Kodi imwe mufuna kukhala monga munthu uti?—Mateyu 7:24-27.

Kudzipeleka. Kudzipeleka kumatanthauza kumuuza Yehova m’pemphelo kuti mufuna kucita cifunilo cake kwamuyaya. Kucita cifunilo ca Mulungu kumaonetsa kuti ndimwe wophunzila wa Yesu Khristu.—Mateyu 11:29.

Ubatizo. ‘Ubatizidwe ndi kusamba kucotsa macimo ako, nuitane pa dzina lake.’—Macitidwe 22:16.

Tumikilani Mulungu na mtima wonse. ‘Ciliconse mukacicita, gwilani nchito mocokela mumtima, monga kwa Ambuye [Yehova, NW], osati kwa anthu ayi.’—Akolose 3:23.