Matsenga na Ufiti ni Vinthu Voipa
Phunzilo 13
Matsenga na Ufiti ni Vinthu Voipa
Satana amafuna kuti muzicita vamatsenga. Anthu ambili amapeleka nsembe ku mizimu ya akufa kuti iziwachinjiliza. Amacita zimenezi cifukwa amaopa mphamvu za mizimu yoipa. Amavala mphete (maling’i) zamatsenga kapena mabango (makhoza). Amamwa kapena kudzola mankhwala amene amaganiza kuti ali na mphamvu zowachinjiliza. Ena amabisa mankhwala mu nyumba kapena kukumbila pansi kuti achinjilize nyumba yawo, kapena kuti kuitsilikila. Palinso ena amene amaseŵenzetsa mankhwala cifukwa amakhulupilila kuti adzawapatsa mwayi pa bizinesi, pamayeso, kapena ofunila mkazi kapena mwamuna.
Njila yabwino kwambili yodzichinjiliza kwa Satana ni kukhala mnzake wa Yehova. Yehova na angelo ake ni amphamvu kwambili kuposa Satana na viŵanda vake. (Yakobo 2:19; Cibvumbulutso 12:9) Yehova ni wokonzekela kuseŵenzetsa mphamvu zake kuti achinjilize anthu amene ni anzake. Ameneŵa ni anthu amene ali okhulupilika kwa iye na mtima wonse.—2 Mbiri 16:9.
Mau a Mulungu amakamba kuti: “Musamacita nyanga kapena kuombeza.” Yehova amazonda zamatsenga, ufiti, kapena kuombeza. Zimenezi amazizonda cifukwa munthu amene amacita zinthu zimenezi amayamba kulamulilidwa na Satana Mdyelekezi.—Levitiko 19:26.