Mmene Mungadziŵile Cipembedzo Coona
Phunzilo 10
Mmene Mungadziŵile Cipembedzo Coona
Ngati mufuna kukhala mnzake wa Mulungu, mufunika kulambila mu cipembedzo cimene iye amavomeleza. Yesu anakamba kuti “olambila oona” adzalambila Mulungu mogwilizana na “coonadi.” (Yohane 4:23, 24) Pali njila imodzi cabe yoyenela kulambilila Mulungu. (Aefeso 4:4-6) Cipembedzo coona cimapeleka ku moyo wosatha, koma cipembedzo conama cimapeleka ku imfa.—Mateyu 7:13, 14.
Cipembedzo coona mungacidziŵe mwa kuona zocita za anthu ake. Cifukwa Yehova ni wabwino, nawo amene amamulambila m’njila yoyenela, ayenela kukhala anthu abwino. Monga mmene mtengo wabwino wa maolenji umabalila maolenji abwino, naco cipembedzo coona cimakhala na anthu abwino.—Mateyu 7:15-20.
Anzake a Yehova amalemekeza Baibo kwambili. Amadziŵa kuti Baibo inacokela kwa Mulungu. Amalola mau a m’Baibo kuwatsogolela m’moyo wawo. Mau a Mulungu amawathandiza kudziŵa mocitila na mavuto awo, ndipo amawathandiza kuphunzila za Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Ndipo iwo amacita zimene amalalikila.
Yohane 13:35.
Anzake a Yehova amakondana wina na mnzake. Yesu anaonetsa cikondi kwa anthu mwa kuwaphunzitsa za Mulungu, na kucilitsa odwala. Komanso, amene ali mu cipembezo coona amakondana wina na mnzake. Mofanana na Yesu, iwo samaona anthu osauka kapena a mtundu wina kukhala apansi. Yesu anakamba kuti anthu adzaŵadziŵa ophunzila ake cifukwa ca kukondana kwawo.—Anzake a Mulungu amalemekeza dzina la Mulungu, lakuti Yehova. Ngati munthu wina akana kuseŵenzetsa dzina lanu, kodi angakhale mnzanu wazoona? Kutalitali! Ngati tili na mnzathu timamutomola dzina lake, ndipo timakamba zabwino za iye kwa ena. Conco anthu amene afuna kukhala anzake a Mulungu afunika kuseŵenzetsa dzina lake na kuuzako ena za iye. Ni zimene Yehova afuna kuti tizicita.—Mateyu 6:9; Aroma 10:13, 14.
Mofanana na Yesu, Anzake a Mulungu amaphunzitsa ena za Ufumu wa Mulungu. Ufumu wa Mulungu ni boma yakumwamba imene idzabweletsa paladaiso padziko lapansi. Anzake a Mulungu amauzako anthu ena za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:14.
A Mboni za Yehova amalimbikila kukhala anzake a Mulungu. Amalemekeza Baibo na kukondana wina na mnzake. Amaseŵenzetsa dzina la Mulungu na kulilemekeza, komanso amaphunzitsa ena za Ufumu wake. A Mboni za Yehova padziko lonse lapansi amalambila mu cipembedzo coona.