Mufunikila Kuphunzila za Mulungu
Phunzilo 3
Mufunikila Kuphunzila za Mulungu
Kuti mukhale mnzake wa Mulungu, mufunikila kuphunzila za iye. Kodi anzanu dzina lanu alidziŵa, ndipo amalitomola? Inde. Naye Mulungu amafuna kuti dzina lake mulidziŵe, ndi kuti muzilitomola. Dzina lake ni Yehova. (Salmo 83:18; Mateyu 6:9) Ndiponso mufunikila kudziŵa zimene amafuna na zimene samafuna. Mufunikanso kudziŵa anzake na adani ake. Koma kudziŵa munthu kumatenga nthawi. Baibo imakamba kuti ni cinthu canzelu kupatula nthawi ya kuphunzila za Yehova.—Aefeso 5:15, 16.
Anzake a Mulungu amacita zimene zimamukondweletsa. Mwacitsanzo, tiyeni tikambe za anzanu. Ngati mumaŵavuta na kucita zinthu zimene samafuna, kodi angapitilize kukhala anzanu? Kutalitali! Ni cimodzimodzi na Mulungu. Ngati imwe mufuna kukhala mnzake, mufunikila kucita zimene iye amafuna.—Yohane 4:24.
Kodi zipembedzo zonse zingakuthandizeni kukhala mnzake wa Mulungu? Iyai. Yesu, amene ni mnzake wa Mulungu wapamtima, anaphunzitsa ponena za njila ziŵili. Ina niikulu ndipo ili ndi anthu ambili oyendamo. Njila imeneyo imapeleka ku cionongeko. Koma njila ina niing’ono ndipo anthu oyendamo ni ocepa. Njila imeneyi imapeleka ku moyo wosatha. Conco, ngati mufuna kukhala mnzake wa Mulungu, mufunikila kuphunzila mmene mungamulambilile mu njila yoyenela.—Mateyu 7:13, 14.