Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mulungu Akupemphani Kuti Mukhale Mnzake

Mulungu Akupemphani Kuti Mukhale Mnzake

Phunzilo 1

Mulungu Akupemphani Kuti Mukhale Mnzake

Mulungu afuna kuti imwe mukhale mnzake. Kodi munaganizapo kuti imwe mungakhale mnzake wa Mulungu? Abulahamu, amene anakhalako kale kwambili, anali mnzake wa Mulungu. (Yakobo 2:23) Baibo imakamba za anthu ena amene anali anzake a Mulungu, ndipo Mulungu anawadalitsa kwambili. Masiku ano, padziko lonse lapansi, pali anthu amene akhala anzake a Mulungu. Na imwe mungakhale mnzake wa Mulungu.

Mulungu angakhale mnzanu woposa mnzanu aliyense. Mulungu salephela kucita zimene amalonjeza kwa anzake okhulupilika. (Salmo 18:25) Kukhala mnzake wa Mulungu nikwabwino kuposa kukhala na cuma. Munthu wolemela akafa, anthu ena amatenga cuma cake. Koma cuma cimene anzake a Mulungu ali naco, palibe munthu amene angacitenge.—Mateyu 6:19.

Anthu ena angayese kukuletsani kuphunzila za Mulungu. Ngakhale anzanu kapena acibanja angafune kukuletsani. (Mateyu 10:36, 37) Ngati ena akusekani kapena kukuopsani, mudzifunse kuti, ‘Kodi ine nifuna kukondweletsa ndani—anthu kapena Mulungu?’ Ganizilani izi: Ngati munthu wina akuuzani kuti muleke kudya, kodi mungaleke? Iyai. Mukaleka kudya mungafe. Koma Mulungu angakupatseni moyo wosatha! Conco, musavomele kuti aliyense akuletseni kuphunzila za kukhala mnzake wa Mulungu.—Yohane 17:3.