Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mulungu Ndiye Angakhale Mnzanu Wabwino Kwambili

Mulungu Ndiye Angakhale Mnzanu Wabwino Kwambili

Phunzilo 2

Mulungu Ndiye Angakhale Mnzanu Wabwino Kwambili

Kukhala mnzake wa Mulungu ni cinthu cabwino kuposa ciliconse cimene mungakhale naco. Iye angakuphunzitseni mmene mungapezele cimwemwe na cisungiko. Ndiponso adzakumasulani ku ziphunzitso zonama na ku vocitacita voipa. Iye adzayamba kumvela mapemphelo anu. Adzakuthandizani kukhala na mtendele wa m’maganizo na cidalilo mwa iye. (Salmo 71:5; 73:28) Panthawi ya mavuto Mulungu adzakuthandizani. (Salmo 18:18) Ndiponso Mulungu akulonjezani mphatso ya moyo wosatha.—Aroma 6:23.

Mukakhala mnzake wa Mulungu, mabwenzi ake nawo adzakhala anzanu. Ndipo iwo adzakhala monga abale na alongo anu. Adzakondwela kukuphunzitsani za Mulungu ndipo adzakulimbikitsani.

Mulungu sitilingana naye. Pamene mufuna kukhala mnzake wa Mulungu, pali mfundo ina imene muyenela kuidziwa bwino. Mfundo imeneyo ni yakuti; mukakhala mnzake wa Mulungu sindiye kuti mwalingana naye iyai. Iye wakhalapo kwa zaka zambili, ali na nzelu na mphamvu zambili kuposa ife. Iye ndiye woyenela kutilamulila. Conco ngati tifuna kukhala mnzake wa Mulungu, tifunikila kumumvela na kucita zimene amatiuza. Tikacita zimenezo, zinthu zidzatiyendela bwino.—Yesaya 48:18.